路加福音 8 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

路加福音 8:1-56

撒种的比喻

1此后,耶稣到各城镇去传扬上帝国的福音。同行的有十二使徒, 2还有几个曾被邪灵和疾病缠身、现在已被医治的妇女。其中有抹大拉玛丽亚,耶稣曾经从她身上赶出七个鬼, 3还有希律的管家苦撒的妻子约亚拿,此外还有苏撒拿等其他妇女。她们用自己的钱财资助耶稣和门徒。

4那时,人群络绎不绝地从各地聚集到耶稣面前,耶稣用比喻教导他们,说: 5“有一个农夫到田里撒种,有些种子落在路旁,被人践踏,又被飞鸟吃掉了; 6有些落在盖着浅土的石头地上,因水分不足,幼苗刚长出来就枯萎了; 7有些落在荆棘丛中,荆棘长起来便把幼苗挤住了; 8有些落在沃土里,发芽生长,结出百倍的果实。”耶稣讲完这番话后,高声说:“有耳可听的,就要留心听。”

9门徒请耶稣解释这比喻的意思, 10耶稣便说:“上帝国的奥秘只让你们知道,对其他人,我就用比喻,使他们看却看不见,听却听不明白。 11这个比喻的意思是这样,种子代表上帝的道, 12种子落在路旁是指人听了道,随后魔鬼来把道从他们心里夺走了,不让他们相信并得救。 13种子落在盖着浅土的石头地上是指人听了道,欣然接受了,但是没有根基,只是暂时相信,一遇到试炼就放弃了。 14种子落在荆棘丛中是指人听了道,后来被生活的忧虑、钱财和享乐缠住了,以致结不出成熟的果实来。 15种子落在沃土里则是指人听了道,用诚实良善的心坚忍持守,至终结出果实。

点灯的比喻

16“没有人点了灯,却用器皿把它盖起来或放到床底下,而是放在灯台上,使进来的人能见到光。 17掩盖的事终会暴露出来,隐藏的秘密终会被人知道。 18因此,你们要留心听,因为凡有的,还要给他更多;凡没有的,连他自以为已经拥有的也要被夺去。”

耶稣的亲属

19这时,耶稣的母亲和兄弟来找祂,由于人太多,他们无法靠近耶稣, 20有人就对祂说:“你的母亲和兄弟在外面想见你。” 21耶稣却说:“听见上帝的话语并遵行的人就是我的母亲、我的弟兄。”

平静风浪

22有一天,耶稣对门徒说:“我们到湖的对岸去吧。”于是他们坐船前往对岸。 23途中耶稣睡着了。不料湖上忽然狂风大作,船灌满了水,非常危险。 24门徒过来唤醒耶稣,说:“主啊,主啊!我们快淹死了!”

耶稣醒来,就斥责风浪,顿时风平浪静了。

25耶稣对他们说:“你们的信心在哪里呢?”

门徒又惊又怕,彼此议论说:“祂究竟是谁?一发命令,连风浪都听祂的!”

格拉森赶鬼

26他们渡过加利利湖,到了格拉森地区。 27耶稣上岸后,迎面遇见当地一个被鬼附身的人。那人长期赤身露体,不住在房屋里,只住在墓穴中。 28他一见到耶稣,就扑倒在祂面前,高声喊叫:“至高上帝的儿子耶稣,我和你有什么关系?求求你,不要折磨我!” 29这是因为耶稣已命令污鬼离开那人。那人多次被污鬼操纵,人们用铁链脚镣把他锁起来看管,他竟把锁链也扯断,被鬼催逼到荒野。

30耶稣问他:“你叫什么名字?”

他说:“我叫‘群’。”因为有一大群鬼附在那人身上。 31鬼不断央求耶稣不要叫它们到无底坑去。

32当时有一大群猪在附近山坡上觅食,污鬼就央求耶稣准许它们进入猪群,耶稣答应了。 33于是那群鬼便离开那人,进入猪群。那群猪就一路奔下陡坡,冲进湖里淹死了。 34放猪的人见此情形拔腿就跑,把这事告诉了城里和乡下的人。 35人们出来看个究竟,到了耶稣那里,发现那曾被鬼附身的人衣着整齐、神智清醒地坐在耶稣脚前,他们都很害怕。 36目击者把事情的始末告诉了他们。 37格拉森地区的居民都十分害怕,请求耶稣离开那里,耶稣便乘船回去了。

38那从前被鬼附身的人恳求跟耶稣同行,耶稣却对他说: 39“你回家吧,把上帝为你所行的奇事告诉别人。”他就回去,走遍全城,四处传扬耶稣为他所行的奇事。

雅鲁求救

40耶稣回到对岸,受到等候在那里的百姓的欢迎。 41一个名叫雅鲁的会堂主管走过来俯伏在耶稣脚前,求耶稣到他家去,因为他有一个大约十二岁的独生女快要死了。

42耶稣前去雅鲁家的时候,人群拥挤着祂。

患血漏病妇人的信心

43有一个患了十二年血漏病的妇人耗尽了积蓄,到处求医,但没有人能医治她。 44妇人挤到耶稣的背后,摸了一下祂衣服的穗边,她的血漏立刻止住了。

45耶稣问:“谁摸我?”没有人说摸过祂。

彼得说:“老师,众人都在拥挤你。”

46耶稣却说:“一定有人摸了我,因为我感觉有能力从我身上出去。”

47那妇人知道无法隐瞒,就战战兢兢地走过来,俯伏在耶稣脚前,把她摸了耶稣的衣裳后顽疾马上痊愈的始末当众说了出来。

48耶稣对她说:“女儿,你的信心救了你!安心回去吧。”

雅鲁女儿死而复活

49耶稣还在说话的时候,有人从雅鲁家赶来,对雅鲁说:“你的女儿已经死了,不用麻烦老师了。”

50耶稣听见,就对雅鲁说:“不要怕,只要信。你的女儿一定会好的!”

51到了雅鲁家,耶稣只准彼得雅各约翰雅鲁夫妇跟祂进去。 52屋内的人都在为那女孩哀伤哭泣,耶稣说:“不要哭,她没有死,只是睡着了。” 53众人就讥笑祂,因为他们明明知道那女孩死了。 54耶稣拉着那女孩的手,说:“孩子,起来!” 55她的灵魂就回来了,她立刻站了起来。耶稣吩咐人给她东西吃。 56她的父母非常惊讶,耶稣却嘱咐他们不要把这事传开。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Luka 8:1-56

Fanizo la Wofesa

1Zitatha izi, Yesu anayendayenda kuchoka mzinda wina kupita wina ndiponso mudzi wina kupita wina, akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu. Ophunzira ake khumi ndi awiri aja anali naye, 2komanso akazi ena amene anachiritsidwa ku mizimu yoyipa ndi matenda: Mariya, wotchedwa Magadalena, amene mwa iye munatuluka ziwanda zisanu ndi ziwiri; 3Yohana mkazi wa Kuza, woyangʼanira mʼnyumba ya Herode; Suzana; ndi ena ambiri analinso. Akazi awa ankawathandiza ndi chuma chawo.

4Anthu ambiri ankasonkhana, ndipo pamene anthu ankabwera kwa Yesu kuchokera ku midzi, Iye anawawuza fanizo ili, 5“Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa mbewuzo, zina zinagwa mʼmbali mwa njira; zinapondedwa, ndipo mbalame zamlengalenga zinadya. 6Zina zinagwa pa thanthwe, ndipo pamene zinamera, zinafota chifukwa panalibe chinyezi. 7Mbewu zina zinagwera pakati pa minga, zinakulira pamodzi ndi mingazo ndipo zinalepheretsa mmerawo kukula. 8Mbewu zina zinagwera pa nthaka yabwino. Zinamera ndipo zinabala mowirikiza 100 kuposa zimene zinafesedwa zija.”

Atanena izi, anafuwula kuti, “Amene ali ndi makutu, amve.”

9Ophunzira ake anamufunsa tanthauzo lake la fanizolo. 10Iye anati, “Kudziwa zinsinsi za ufumu wa Mulungu kwapatsidwa kwa inu, koma kwa ena ndimawayankhula mʼmafanizo kuti,

“ngakhale akuona, asapenye;

ngakhale akumva, asazindikire.”

11“Tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbewu ndi mawu a Mulungu. 12Mbewu za mʼmbali mwa njira ndi anthu amene amamva mawu, ndipo kenaka mdierekezi amabwera ndi kuchotsa mawuwo mʼmitima mwawo kuti asakhulupirire ndi kupulumutsidwa. 13Mbewu za pa thanthwe ndi anthu amene amalandira mawu mwachimwemwe pamene akumva, koma mawuwo sazika mizu. Iwo amakhulupirira kwa kanthawi, koma pa nthawi ya mayesero, amagwa. 14Mbewu zimene zinagwa pakati pa minga zikuyimira anthu amene amamva mawu, koma akamayenda mʼnjira zawo amatsamwitsidwa ndi zodandaulitsa za moyo uno, chuma ndi zosangalatsa, ndipo iwo samakhwima. 15Koma mbewu za pa nthaka yabwino zikuyimira anthu amene ali ndi mtima woona ndi wabwino, amene amamva mawu nawasunga, ndipo amalimbikira mpaka amabala zipatso.

Nyale ndi Choyikapo Chake

16“Palibe amayatsa nyale ndi kuyibisa mu mtsuko kapena kuyika pansi pa bedi. Koma mʼmalo mwake, amayika pa choyikapo chake, kuti anthu olowamo aone kuwala. 17Pakuti palibe kanthu kobisika kamene sikadzawululika, ndipo palibe kanthu kophimbika kamene sikadzadziwika kapena kuonetsedwa poyera. 18Choncho ganizirani mozama. Iye amene ali nazo adzapatsidwa zambiri, iye amene alibe, ngakhale chimene akuganiza kuti ali nacho adzalandidwa.”

Amayi ndi Abale a Yesu

19Tsopano amayi ndi abale a Yesu anabwera kudzamuona Iye, koma analephera kuti afike pafupi ndi Iye chifukwa cha gulu la anthu. 20Wina anamuwuza Iye kuti, “Amayi ndi abale anu ayima kunja, akufuna kukuonani.”

21Yesu anayankha kuti, “Amayi ndi abale anga ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kumachita zimene mawuwo akunena.”

Yesu Aletsa Namondwe

22Tsiku lina Yesu anati kwa ophunzira ake, “Tiyeni tiwolokere tsidya lina la nyanja.” Ndipo analowa mʼbwato nanyamuka. 23Akuwoloka, Iye anagona tulo. Namondwe wamkulu anayamba pa nyanja, ndipo bwatolo linayamba kudzaza ndi madzi ndipo anali pa chiopsezo chachikulu.

24Ophunzira anapita ndi kukamudzutsa Iye, nati, “Ambuye, Ambuye, ife tikumira!”

Anadzuka ndipo anadzudzula mphepo ndi madzi owindukawo. Namondwe anasiya, ndipo panali bata. 25Iye anafunsa ophunzira ake kuti, “Chikhulupiriro chanu chili kuti?”

Koma pogwidwa ndi mantha ndi kudabwa anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Uyu ndi ndani? Iye alamulira ngakhale mphepo ndi madzi, ndipo zimumvera Iye.”

Achiritsidwa Munthu Wogwidwa ndi Ziwanda

26Iwo anawolokera ku chigawo cha Gerasa chimene chili tsidya lina la nyanja kuchokera ku Galileya. 27Yesu ataponda pa mtunda, anakumana ndi munthu wogwidwa ndi ziwanda wochokera mu mzindawo. Kwa nthawi yayitali munthuyu sanavale zovala kapena kukhala mʼnyumba, koma amakhala ku manda. 28Iye ataona Yesu, anakuwa nagwa pa mapazi ake akufuwula kwambiri kuti, “Mukufuna chiyani ndi ine, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Ndikupemphani Inu, musandizunze ine!” 29Pakuti Yesu analamula mzimu woyipawo kuti utuluke mwa munthuyo. Kawirikawiri umamugwira iye, ndipo ngakhale anali womangidwa ndi unyolo dzanja ndi mwendo ndi kuti ankamuyangʼanira, koma amadula maunyolo akewo ndipo ziwanda zimamutengera kumalo a yekha.

30Yesu anamufunsa kuti, “Dzina lako ndani?”

Iye anayankha kuti, “Legiyo,” chifukwa ziwanda zambiri zinalowa mwa iye. 31Ndipo ziwandazo zimamupempha mobwerezabwereza kuti asazitumize ku dzenje la mdima.

32Gulu lalikulu la nkhumba limadya pamenepo mʼmbali mwa phiri. Ziwandazo zinamupempha Yesu kuti azilole kuti zikalowe mu nkhumbazo ndipo Iye anazilola. 33Ziwanda zija zitatuluka mwa munthuyo, zinakalowa mwa nkhumbazo, ndipo gulu lonselo linathamangira ku mtsetse ndi kukalowa mʼnyanja ndi kumira.

34Oweta nkhumbazo ataona zimene zinachitikazo, anathamanga ndi kukanena izi mu mzinda ndi ku madera a ku midzi. 35Ndipo anthu anapita kukaona zimene zinachitika. Atafika kwa Yesu, anapeza munthu amene anatulutsidwa ziwanda uja atakhala pa mapazi a Yesu, atavala ndipo ali ndi nzeru zake; ndipo iwo anachita mantha. 36Amene anaona izi anawuza anthu mmene munthu wogwidwa ndi ziwandayo anachiritsidwira. 37Kenaka anthu onse a ku chigawo cha Gerasa anamupempha Yesu kuti achoke kwa iwo, chifukwa anadzazidwa ndi mantha. Choncho Iye analowa mʼbwato nachoka.

38Munthu amene anatulutsidwa ziwanda uja, anapempha Yesu kuti apite nawo, koma Yesu anamubweza nati, 39“Bwerera kwanu kafotokoze zimene Mulungu wakuchitira.” Ndipo munthuyo anachoka ndi kukanena ku mzinda wonsewo zimene Yesu anamuchitira iye.

Mwana Wamkazi wa Yairo ndi Mayi Wokhudza Chovala cha Yesu

40Yesu atabwerera, gulu lalikulu la anthu linamulandira, chifukwa onse ankamuyembekezera. 41Nthawi yomweyo munthu wotchedwa Yairo, woweruza wa mu sunagoge, anabwera ndi kugwa pa mapazi a Yesu, namupempha Iye kuti apite ku nyumba kwake, 42chifukwa mwana wake yekhayo wamkazi, kamtsikana ka zaka khumi ndi ziwiri, kanali pafupi kufa.

Pamene Yesu ankapita gulu la anthu linkamupanikiza. 43Ndipo pomwepo panali mayi wina amene ankataya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri, koma panalibe wina akanamuchiritsa. 44Iye anafika kumbuyo kwake ndi kukhudza mothera mwa chovala chake, ndipo nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka.

45Yesu anafunsa kuti, “Wandikhudza ndani?”

Onse atakana, Petro anati, “Anthu akukupanikizani ndi kukukankhani.”

46Koma Yesu anati, “Wina wandikhudza; ndikudziwa chifukwa mphamvu yachoka mwa Ine.”

47Ndipo mayiyo podziwa kuti sanathe kuchoka wosadziwika, anabwera akunjenjemera ndipo anagwa pa mapazi a Yesu. Pamaso pa anthu onse, anafotokoza chifukwa chimene anamukhudzira Iye ndi mmene iye anachiritsidwira nthawi yomweyo. 48Kenaka anati kwa iye, “Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere.”

49Pamene Yesu ankayankhulabe, munthu wina anabwera kuchokera ku nyumba ya Yairo, woweruza wa ku sunagoge uja. Iye anati, “Mwana wanu wa mkazi wamwalira, musawavutitsenso Aphunzitsiwa.”

50Atamva zimenezi, Yesu anati kwa Yairo, “Usachite mantha, ingokhulupirira basi ndipo adzachiritsidwa.”

51Iye atafika ku nyumba ya Yairo, sanalole wina aliyense kulowa kupatula Petro, Yohane, ndi Yakobo ndi abambo ndi amayi a mwanayo. 52Pa nthawiyi nʼkuti anthu onse akubuma ndi kumulirira iye. Yesu anati, “Lekani kulira, sanafe koma wagona tulo.”

53Iwo anamuseka podziwa kuti anali atamwalira. 54Koma Iye anamugwira dzanja lake ndipo anati, “Mwana wanga, dzuka!” 55Mzimu wake unabwerera, ndipo nthawi yomweyo anayimirira. Kenaka Yesu anawawuza kuti amupatse chakudya. 56Makolo ake anadabwa, koma Iye anawalamulira kuti asawuze wina aliyense zimene zinachitikazo.