路加福音 21 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

路加福音 21:1-38

穷寡妇的奉献

1耶稣抬头观看,见有钱人正把捐项投进奉献箱里, 2又见一个穷寡妇投进两个小铜钱, 3就说:“我实在告诉你们,这位穷寡妇奉献的比其他人都多。 4因为他们不过奉献了自己剩余的,但这穷寡妇却奉献了她赖以为生的一切。”

预言将来的事

5有些人正在谈论由精美的石头和珍贵的供物所装饰的圣殿, 6耶稣说:“你们现在所见到的,将来有一天要被完全拆毁,找不到两块叠在一起的石头。”

7他们问:“老师,这些事什么时候会发生呢?发生的时候有什么预兆呢?”

8耶稣回答说:“你们要小心提防,不要被迷惑。因为将来会有许多人冒我的名来,说,‘我就是基督’,或说,‘时候到了’,你们切勿跟从他们。 9你们听见打仗和叛乱的事,不要害怕,因为这些事一定会先发生,但末日将不会立刻来临。”

10耶稣接着说:“民族将与民族互斗,国家将与国家相争, 11将有大地震,各处将有饥荒和瘟疫,天上也将出现恐怖的景象和大异兆。

12“这些事情出现之前,人们要拘捕你们,迫害你们,把你们押到会堂和监牢,你们将为了我的名而被君王和官长审问。 13那时,正是你们为我做见证的好机会。 14你们要立定心志,不要为怎样申辩而忧虑, 15因为我会赐给你们口才、智慧,使你们的仇敌全无反驳的余地。 16你们将被父母、弟兄、亲戚、朋友出卖,你们有些人会被他们害死。 17你们将为我的名而被众人憎恨, 18但你们连一根头发也不会失落。 19你们只要坚忍到底,必能保全自己的灵魂。

20“你们看见耶路撒冷被重兵包围时,就知道它被毁灭的日子快到了。 21那时,住在犹太地区的人要赶快逃到山上去,住在城里的人要跑到城外,住在乡村的人不要进城, 22因为那是报应的日子,要应验圣经的全部记载。 23那时,孕妇和哺育婴儿的母亲们可就遭殃了!因为将有大灾难降在这地方,烈怒要临到这些人民。 24他们要死在刀剑之下,要被掳到外国去。耶路撒冷要被外族人蹂躏,直到外族人肆虐的日期满了为止。

25“日月星辰必显出异兆,怒海汹涌、波涛翻腾,令各国惊恐不安。 26天体必震动,人类想到世界要面临的事都吓得魂不附体。 27那时,他们要看见人子驾着云、带着能力和极大的荣耀降临。 28当这些事发生时,你们要昂首挺胸,因为你们蒙救赎的日子近了。”

警醒祷告

29耶稣又讲了一个比喻:“看看无花果树和其他树木吧。 30当你们看见树木发芽长叶时,就知道夏天近了。 31同样,当你们看见这些事情发生时,就知道上帝的国近了。

32“我实在告诉你们,这个世代还没有过去,这一切都要发生。 33天地都要消逝,但我的话永不消逝。

34“你们要小心,不要被宴乐、醉酒和人生的挂虑所拖累,免得那日子像网罗般突然临到你们, 35因为那日子将要这样临到世上每一个人。 36你们要时刻警醒,常常祷告,使你们能逃过这一切将要发生的灾难,并能站在人子面前。”

37耶稣每天在圣殿里讲道,晚上则到城外的橄榄山上过夜。 38百姓一早都赶去圣殿听祂的教导。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Luka 21:1-38

Chopereka cha Mayi Wamasiye

1Yesu atayangʼana, anaona olemera akuyika mphatso zawo mu chosungira ndalama za mʼNyumba ya Mulungu. 2Iye anaonanso mkazi wamasiye wosauka akuyikamo timakopala tiwiri. 3Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu wapereka zambiri kuposa ena onsewa. 4Anthu onsewa atapa mphatso zawo kuchokera pa zochuluka zimene ali nazo; koma uyu, mwa umphawi wake, wapereka zonse zimene ali nazo.”

Zizindikiro za Masiku Otsiriza

5Ena mwa ophunzira ake ankachita ndemanga za mmene Nyumba ya Mulungu anayikongoletsera ndi miyala yokongola ndiponso zinthu zina zomwe anthu anapereka kwa Mulungu. Koma Yesu anati, 6“Koma zimene mukuziona panozi, nthawi idzafika pamene ngakhale mwala umodzi omwe sudzakhala pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”

7Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi zonsezi zidzachitika liti? Ndipo tidzaonera chiyani kuti zili pafupi kuchitika?”

8Iye anayankha kuti, “Chenjerani kuti musanyengedwe. Pakuti ambiri adzabwera mʼdzina langa nadzati ‘Ine ndine Iye’ ndi kuti ‘Nthawi yayandikira.’ Musadzawatsate iwo. 9Mukadzamva zankhondo ndi zipolowe, musadzachite mantha. Zinthu izi ziyenera kuchitika poyamba, koma chimaliziro sichidzafika nthawi yomweyo.”

10Kenaka anawawuza kuti, “Mtundu wa anthu udzawukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu kuwukira ufumu wina. 11Kudzakhala zivomerezi zazikulu, njala ndi miliri mʼmalo osiyanasiyana, ndi zinthu zoopsa ndi zizindikiro zamphamvu kuchokera kumwamba.

12“Koma zonsezi zisanachitike, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzakuperekani ku masunagoge ndi ku ndende, ndipo adzakutengerani pamaso pa mafumu ndi olamulira, ndipo zonsezi zidzachitika chifukwa cha dzina langa. 13Umenewu udzakhala mwayi wanu ochitira umboni. 14Koma tsimikizani mtima kuti musadzade nkhawa za momwe mudzadzitchinjirizire. 15Pakuti Ine ndidzakupatsani mawu ndi nzeru kotero kuti palibe mmodzi wa adani anu adzathe kuwakana kapena kuwatsutsa. 16Inu mudzaperekedwa ndi makolo anu, abale, anansi ndi abwenzi anu ndipo ena mwa inu adzakuphani. 17Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine. 18Koma palibe tsitsi limodzi la mʼmutu mwanu lidzawonongeke. 19Mukadzalimbikira ndiye mudzapeze moyo.

Kuwonongedwa kwa Yerusalemu

20“Mukadzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu ankhondo, inu mudzadziwe kuti kuwonongeka kwake kuli pafupi. 21Pamenepo amene ali ku Yudeya adzathawire ku mapiri, amene ali mu mzinda adzatulukemo, ndi amene ali ku midzi asadzalowe mu mzinda. 22Pakuti iyi ndi nthawi yachilango pokwaniritsa zonse zimene zinalembedwa. 23Zidzakhala zoopsa nthawi imenewo kwa amayi oyembekezera ndi amayi oyamwitsa! Kudzakhala masautso aakulu mʼdziko ndipo anthu onse adzawakwiyira. 24Iwo adzaphedwa ndi lupanga ndi kutengedwa ukapolo kupita ku mayiko wonse. Yerusalemu adzaponderezedwa ndi anthu a mitundu ina mpaka nthawi ya a mitundu ina itakwaniritsidwa.

25“Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuwa, mwezi ndi nyenyezi. Pa dziko lapansi, mitundu ya anthu idzakhala mʼmasautso ndipo idzathedwa nzeru pakumva mkokomo ndi mafunde a mʼnyanja. 26Anthu adzakomoka chifukwa cha mantha, akadzamva za zimene zikubwera pa dziko lapansi, pakuti zinthu zamlengalenga zidzagwedezeka. 27Nthawi imeneyo adzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu. 28Zinthu izi zikadzayamba kuchitika, mudzayimirire ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira.”

Fanizo la Mtengo Wamkuyu

29Iye anawawuza fanizo ili, “Taonani mtengo wamkuyu ndi mitengo ina yonse. 30Ikamatulutsa masamba, mumakhoza kudzionera nokha ndi kudziwa kuti dzinja lili pafupi. 31Chimodzimodzinso, mukadzaona zinthu zonsezi, dziwani kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi.

32“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mʼbado uno sudzatha mpaka zinthu zonsezi zitachitika. 33Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”

Za Kukhala Tcheru

34“Samalani, kuti mitima yanu ingalemetsedwe ndi maphwando, kuledzera ndi kudera nkhawa za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingadzakupezeni modzidzimutsa ngati msampha. 35Pakuti lidzafika pa onse okhala pa dziko lonse lapansi. 36Khalani tcheru nthawi zonse ndi kupemphera kuti inu mudzathe kuthawa zonse zimene zili pafupi kuchitika, ndi kuti mudzathe kuyima pamaso pa Mwana wa Munthu.”

37Tsiku lililonse Yesu amaphunzitsa ku Nyumba ya Mulungu, ndi madzulo ali wonse Iye amachoka kukakhala pa phiri la Olivi usiku wonse. 38Ndipo anthu onse amabwera mmamawa kudzamumva Iye ku Nyumba ya Mulungu.