诗篇 65 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

诗篇 65:1-13

第 65 篇

赞美和感恩

大卫作的诗,交给乐长。

1上帝啊,

人们在锡安赞美你,

向你履行誓言。

2你垂听祷告,

世人都来到你面前。

3虽然我们深陷罪中,

你却赦免了我们。

4蒙你拣选、

能住在你圣所的人有福了!

我们在你美好的居所,

你圣洁的殿中心满意足。

5拯救我们的上帝啊,

你凭公义、行可畏之事来应允我们的祈求。

你是普天下的盼望。

6你充满力量,以大能创造群山,

7又平息怒海狂涛,

止息列邦的喧嚣。

8你奇妙的作为使远在地极的人心生敬畏,

你使日出之地和日落之处都传来欢呼声。

9你眷顾大地,降下沛雨,

使土地肥沃富饶。

上帝啊,你使江河涌流不息,

浇灌大地,为世人预备五谷。

10你降下甘霖,浇透垄沟,

滋润垄背,使地松软、

长出庄稼。

11你赐下丰年福月,

你的脚踪恩泽满溢。

12旷野的草地生机盎然,

山岭间充满欢乐,

13草场遍布羊群,

谷中长满庄稼,

处处欢歌笑语。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 65:1-13

Salimo 65

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Nyimbo.

1Matamando akudikira Inu Mulungu mu Ziyoni;

kwa inu malumbiro athu adzakwaniritsidwa.

2Inu amene mumamva pemphero,

kwa inu anthu onse adzafika.

3Pamene tinathedwa nzeru ndi machimo,

Inu munakhululukira mphulupulu zathu.

4Odala iwo amene inu muwasankha

ndi kuwabweretsa pafupi kukhala mʼmabwalo anu!

Ife tadzazidwa ndi zinthu zabwino za mʼNyumba mwanu,

za mʼNyumba yanu yoyera.

5Mumatiyankha ife ndi ntchito zodabwitsa zachilungamo,

Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,

chiyembekezo cha mathero onse a dziko lapansi

ndi cha nyanja zomwe zili kutali kwambiri,

6amene munapanga mapiri ndi mphamvu zanu,

mutadziveka nokha ndi mphamvu.

7Amene munakhalitsa bata nyanja

kukokoma kwa mafunde ake,

ndi phokoso la anthu a mitundu ina.

8Iwo amene akukhala kutali amaopa zizindikiro zozizwitsa zanu;

kumene dzuwa limatulukira ndi kumene dzuwa limalowera.

Inu mumafuna nyimbo zachimwemwe.

9Inu mumasamalira dziko lapansi ndi kulithirira;

Inuyo mumalilemeretsa kwambiri.

Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi

kuti upereke tirigu kwa anthu,

pakuti Inu munakhazikitsa zimenezi.

10Mwadzaza nthaka yake ndi madzi ndi kusalaza migula yake,

mwayifewetsa ndi mvula yamawawa ndi kudalitsa mbewu zake.

11Inu mumaveka chaka ndi zinthu zochuluka,

ndipo ngolo zanu zimasefukira ndi zinthu zochuluka.

12Malo a udzu a mʼchipululu amasefukira;

mapiri avekedwa ndi chisangalalo.

13Madambo akutidwa ndi zoweta

ndi zigwa zavekedwa ndi tirigu;

izo pamodzi zikufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe.