西番雅书 1 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

西番雅书 1:1-18

1犹大亚们的儿子约西亚执政期间,耶和华对希西迦的玄孙、亚玛利亚的曾孙、基大利的孙子、古示的儿子西番雅说:

耶和华审判的日子

2“我必毁灭地上的一切。

这是耶和华说的。

3我必毁灭人类、兽类、

天上的鸟和海里的鱼。

我必使恶人倒毙,

我必铲除地上的人类。

这是耶和华说的。

4“我必伸手攻击犹大

以及所有住在耶路撒冷的人,

铲除巴力的余迹及拜偶像之祭司的名号。

5我必铲除那些在屋顶祭拜天上万象的人,

铲除敬拜我、凭我起誓又凭米勒公起誓的人,

6铲除离弃我、不寻求我、不求问我的人。”

7要在主耶和华面前肃静,

因为耶和华的日子近了。

耶和华已准备好祭物,

洁净了祂邀请的人。

8耶和华说:“在我献祭的日子,

我必惩罚首领和王子,

以及所有穿外族服装的人。

9到那日,我必惩罚所有跳过门槛1:9 跳过门槛……的人”指祭拜偶像的人,参见撒母耳记上5:5

使主人的家充满暴力和欺诈的人。

10到那日,鱼门必传出哭喊声,

新区必响起哀号声,

山陵必发出崩裂的巨响。

这是耶和华说的。

11市场区的居民啊,哀哭吧!

因为所有的商人必灭亡,

所有做买卖的必被铲除。

12那时,我必提着灯巡查耶路撒冷

惩罚那些安于罪中的人。

他们心想,‘耶和华不赐福也不降祸。’

13他们的财物必遭抢掠,

家园必沦为废墟。

他们建造房屋,却不能住在里面;

栽种葡萄园,却喝不到葡萄酒。

14“耶和华的大日子近了,

近了,很快就到了。

那将是痛苦的日子,

勇士也必凄声哀号。

15那是降烈怒的日子,

是困苦艰难的日子,

是摧残毁坏的日子,

是黑暗幽冥的日子,

是阴霾密布的日子,

16是吹号呐喊、

攻打坚城高垒的日子。

17“我要使人们灾难临头,

以致他们行路像瞎子,

因为他们得罪了我。

他们的血必被倒出,如同灰尘;

他们的尸体必被丢弃,如同粪便。

18在耶和华发怒的日子,

他们的金银救不了他们。

祂的怒火必吞噬大地,

祂必骤然毁灭一切世人。”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zefaniya 1:1-18

1Yehova anayankhula ndi Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya pa nthawi ya Yosiya, mwana wa Amoni, mfumu ya Yuda.

Yehova Adzaweruza Dziko Lapansi

2“Ndidzawononga kotheratu zinthu zonse

pa dziko lapansi,”

akutero Yehova.

3“Ndidzawononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe;

ndidzawononga mbalame zamlengalenga

ndi nsomba za mʼnyanja.

Ndidzawononga anthu oyipa,

ndipo ndidzafafaniza mtundu wa anthu pa dziko lonse lapansi,”

akutero Yehova.

Chenjezo kwa Yuda

4Ndidzatambasula dzanja langa pa Yuda

ndi onse okhala mu Yerusalemu.

Ndidzawononga pamalo pano otsalira opembedza Baala,

mayina a anthu osapembedza pamodzi ndi ansembe a mafano:

5amene amagwada pa madenga a nyumba zawo

kupembedza zolengedwa zamumlengalenga,

amene amagwada ndi kulumbira mʼdzina la Yehova,

komanso mʼdzina la Moleki,

6amene abwerera mʼmbuyo osatsata Yehova,

osafunafuna kapena kupempha nzeru kwa Yehova.

7Khalani chete pamaso pa Ambuye Yehova,

chifukwa tsiku la Yehova layandikira.

Yehova wakonzekera kupereka nsembe;

wapatula iwo amene wawayitana.

8Pa tsiku la nsembe ya Yehova

ndidzalanga akalonga

ndi ana aamuna a mfumu

ndi onse amene amavala

zovala zachilendo.

9Pa tsiku limenelo ndidzalanga

onse amene safuna kuponda pa chiwundo,

amene amadzaza nyumba ya ambuye awo

ndi chiwawa ndi chinyengo.

10“Pa tsiku limenelo,” akutero Yehova,

“Kufuwula kwakukulu kudzamveka pa Chipata cha Nsomba,

kulira kwa chisoni kuchokera mʼChigawo Chatsopano,

ndi phokoso la kugumuka kochokera ku mapiri.

11Lirani mwachisoni, inu amene mumakhala kumene kuli msika;

a malonda anu onse adzapululidwa,

ndiponso onse amene ali ndi siliva adzawonongedwa.

12Pa nthawi imeneyo ndidzafufuzafufuza mu Yerusalemu ndi nyale

ndi kulanga onse amene sakulabadira,

amene ali ngati vinyo wosakhutchumulidwa,

amene amaganiza kuti, ‘Yehova sadzachita chilichonse,

chabwino kaya choyipa.’

13Chuma chawo chidzafunkhidwa,

nyumba zawo zidzagwetsedwa.

Adzamanga nyumba,

koma osakhalamo;

adzadzala minda ya mpesa

koma sadzamwako vinyo wake.”

Tsiku Lalikulu la Yehova

14Tsiku lalikulu la Yehova layandikira,

layandikira ndipo lifika msanga.

Tamverani! Kulira kwa pa tsiku la Yehova kudzakhala kowawa,

ngakhale munthu wolimba mtima adzalira kwambiri.

15Tsiku limenelo lidzakhala la ukali,

tsiku losautsa ndi lomvetsa chisoni,

tsiku la mavuto ndi la chiwonongeko,

tsiku la mdima ndi lachisoni,

tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani.

16Tsiku loliza lipenga ndi la mfuwu wankhondo,

tsiku la kugwa kwa mizinda yotetezedwa

ndi nsanja za pa ngodya.

17Ndidzabweretsa msautso pa anthu

ndipo adzayenda ngati anthu osaona,

chifukwa achimwira Yehova,

magazi awo adzamwazika ngati fumbi

ndi mnofu wawo ngati ndowe.

18Ngakhale siliva wawo kapena golide wawo

sadzatha kuwapulumutsa

pa tsiku la ukali wa Yehova.

Dziko lonse lapansi lidzanyeka

mʼmoto wa nsanje yake

chifukwa adzakantha modzidzimutsa

onse okhala pa dziko lapansi.