腓立比书 4 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

腓立比书 4:1-23

保罗的劝勉

1我所亲爱、所想念的弟兄姊妹,你们就是我的喜乐,我的冠冕。我亲爱的弟兄姊妹,你们要靠主坚定不移。 2我恳求友阿蝶循都姬要在主里同心。 3忠心的同工啊,请你帮助她们二人,因为她们曾与我、革利免和其他同工一起为福音辛劳,这些人的名字都记录在生命册上了。

4你们要靠主常常喜乐!我再说,你们要喜乐! 5要让众人都知道你们是谦和宽容的人。主快来了。 6你们应该一无挂虑,凡事要借着祷告和祈求,以感恩的心将你们的需要告诉上帝。 7这样,上帝那超越人所能理解的平安必在基督耶稣里保守你们的心思意念。

8最后,弟兄姊妹,你们要思想一切真实、可敬、公义、纯洁、可爱、有好名声、有美德和值得赞许的事情。 9你们从我身上学习、领受、看到和听到的,都要照着去行。这样,赐平安的上帝就必与你们同在。

致谢

10我在主里真是非常喜乐,因为你们现在又一次关心我。其实你们向来都很关心我,只是没有机会。 11我并非有缺乏才这样说,因为我已经学会在任何处境中都能知足。 12我知道如何过贫穷的日子,也知道如何过富足的日子。我学到了秘诀,不论饱足或饥饿,丰裕或缺乏,在任何情况下都可以处之泰然。 13靠着赐我力量的那位,我凡事都能做。

14然而,你们与我共患难,真是太好了。 15腓立比人啊!你们也知道,在我离开马其顿传福音的初期,除了你们以外,没有别的教会供应我的需要。 16即使我在帖撒罗尼迦的时候,你们也不止一次供应过我的需要。 17我不求得到你们的馈赠,只希望你们所做的会带给你们更大的赏赐。 18我现在样样都有,丰富有余。我从以巴弗提手上收到了你们送给我的礼物,已经充足了。这些馈赠是蒙上帝悦纳的馨香祭物。 19我的上帝必按照祂在基督耶稣里的荣耀,丰丰富富地赐给你们所需用的一切。

20愿荣耀归给我们的父上帝,直到永永远远。阿们!

问候

21请代我问候在基督耶稣里的众圣徒。我这里的弟兄姊妹也问候你们。 22所有的圣徒,特别是在凯撒宫里工作的人,都问候你们。

23愿主耶稣基督的恩典与你们的灵同在!

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Afilipi 4:1-23

1Tsono abale anga, ndimakukondani ndipo ndikukulakalakani. Ndinu chimwemwe changa ndi chipewa cha ulemerero wanga. Abwenzi okondedwa, chilimikani choncho mwa Ambuye.

2Ndikudandaulira Euodiya ndi Suntuke kuti akhale ndi mtima umodzi mwa Ambuye. 3Inde, ndikupempha iwe mnzanga pa ntchitoyi, thandiza amayiwa amene ndagwira nawo ntchito ya Uthenga Wabwino pamodzi ndi Klementonso ndi ena onse antchito anzanga amene mayina awo ali mʼbuku lamoyo.

Malangizo Otsiriza

4Nthawi zonse muzikondwa mwa Ambuye. Ndikubwerezanso; muzikondwa! 5Kufatsa kwanu kuzioneka pamaso pa anthu onse. Ambuye anu ali pafupi. 6Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu. 7Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

8Potsiriza, abale, muziyika mtima wanu pa zinthu zilizonse zabwino ndi zotamandika monga, zinthu zoona, zinthu zolemekezeka, zinthu zolungama, zinthu zoyera, zinthu zokongola ndi zinthu zosiririka. 9Muzichita chilichonse chimene mwaphunzira kapena kulandira kapena kumva kuchokera kwa ine kapena mwaona mwa ine. Ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu.

Kuthokoza Chifukwa cha Mphatso

10Ndikukondwa kwambiri mwa Ambuye kuti patapita nthawi tsopano mwayambanso kuonetsa kuti mumandiganizira. Zoonadi, mwakhala mukundikumbukira, koma munalibe mpata woti muonetsere zimenezi. 11Sindikunena izi chifukwa choti ndikusowa thandizo, poti ine ndaphunzira kukhala wokwaniritsidwa ndi zimene ndili nazo. 12Ndimadziwa kusauka nʼkutani, ndipo ndimadziwa kulemera nʼkutani. Ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhutitsidwa mwa njira ina iliyonse, kaya nʼkudya bwino kapena kukhala ndi njala, kaya kukhala ndi chuma kapena umphawi. 13Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.

14Komatu munachita bwino kundithandiza mʼmavuto anga. 15Ndipo inu Afilipi mukudziwa kuti masiku oyambirira olalikira Uthenga Wabwino, nditachoka ku Makedoniya, panalibe mpingo ndi umodzi omwe umene unagwirizana nane pa nkhani yopereka ndi kulandira, kupatula inu. 16Pakuti ngakhale pamene ndinali ku Tesalonika, munanditumizira kangapo zondithandiza pa zosowa zanga. 17Osati ndikufuna mphatso zanu, koma ndikufuna kuti pa zimene muli nazo pawonjezerekepo phindu. 18Ndalandira zonse ndipo ndili nazo zokwanira zoposa zosowa zanga popeza ndalandira kwa Epafrodito mphatso zochuluka zimene munatumiza. Ndizo zopereka za fungo labwino, nsembe zolandiridwa zokondweretsa Mulungu. 19Ndipo Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu monga mwa chuma chake chaulemerero mwa Khristu Yesu.

20Kwa Mulungu ndi Atate athu, kukhale ulemerero mpaka muyaya. Ameni.

Malonje Otsiriza

21Perekani moni kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu. Abale amene ali ndi ine akupereka moni wawo. 22Oyera mtima onse akupereka moni, makamaka iwo a ku nyumba ya Kaisara.

23Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu. Ameni.