耶利米书 7 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

耶利米书 7:1-34

圣殿讲道

1耶和华对耶利米说: 2“你站在耶和华殿的门口这样宣告,‘从这些门进殿敬拜耶和华的犹大人啊,你们要听耶和华的话。 3以色列的上帝——万军之耶和华说,你们改过自新,我便让你们在这里安居。 4你们不要相信那些谎言,说这是耶和华的殿,这是耶和华的殿,这是耶和华的殿。

5“‘如果你们真正改过自新,彼此公平相待, 6不欺压异乡人和孤儿寡妇,不在这地方滥杀无辜,不拜其他神明自取毁灭, 7我便让你们在这块我永远赐给你们祖先的土地上安居。

8“‘然而,你们竟相信那些空洞的谎言。 9你们偷盗、谋杀、通奸、起假誓、向巴力献祭、拜素不认识的神明, 10然后来到这用来敬拜我的殿,站在我面前说自己安全了,以为可以继续做可憎之事。 11难道这用来敬拜我的殿在你们眼中竟成了贼窝?这些事,我都看在眼里。这是耶和华说的。

12“‘你们去我曾选为我名所在之地的示罗,看看我是怎样因我以色列子民的罪而惩罚那地方的。 13我对你们的所作所为一再提出警告,你们却充耳不闻;我呼唤你们,你们却不回应。这是耶和华说的。 14因此,我要像对付示罗一样对付你们所倚靠的这用来敬拜我的殿,对付我赐给你们和你们祖先的土地。 15我要把你们从我面前赶走,好像从前赶走你们的弟兄以法莲7:15 以法莲”此处指“北国以色列”。人一样。’”

16耶和华说:“耶利米啊,不要为这些百姓祷告,不要替他们哀求,不要为他们向我祈求,因为我必不听。 17你没有看见他们在犹大各城和耶路撒冷街道上所做的事吗? 18孩子拾柴,父亲点火,妇人揉面做饼向天后献祭,向别的神明奠酒,惹我发怒。 19耶和华说,‘难道他们是在惹我发怒吗?难道他们不是自害己身,自取羞辱吗?’ 20主耶和华说,‘我要向这地方的人、牲畜、田野的树木和地里的出产发怒,发烈怒,如无法熄灭的火。’”

21以色列的上帝——万军之耶和华说:“你们把平安祭连同燔祭都拿去吃吧! 22因为我把你们祖先带出埃及的时候,并没有吩咐他们献燔祭或其他祭物, 23只吩咐他们,‘你们要听从我的话,我就做你们的上帝,你们做我的子民;你们遵行我的吩咐,就必蒙福。’ 24他们却掩耳不听,一意孤行,任意行恶,越来越坏。 25从你们的祖先离开埃及那天起,一直到今天,我日复一日地差遣我的仆人——众先知到你们那里, 26但你们掩耳不听,顽固不化,比你们的祖先更邪恶。 27耶利米啊,你将这番话告诉他们,他们也不会听;你向他们呼吁,他们也不会回应。 28你要对他们说,‘你们这些国民不听你们上帝耶和华的话,不肯受管教,口中毫无真理。

29“‘你们要剪掉头发,

在光秃的山上哀哭,

因为耶和华已弃绝这惹祂发怒的百姓。’”

30耶和华说:“犹大人做了我视为邪恶的事,把可憎的偶像放在用来敬拜我的圣殿中,玷污了圣殿。 31他们在欣嫩子谷的陀斐特建造丘坛,焚烧自己的儿女。我从未吩咐他们这样做,连想都没想过。这不是我的吩咐,我也从未这样想过。 32因此,看啊,时候将到,那地方必不再叫陀斐特欣嫩子谷,而要叫杀戮谷。那里要埋葬死人,直到无处可埋。这是耶和华说的。 33飞鸟和走兽必吃这百姓的尸体,无人驱赶它们。 34我要使犹大各城和耶路撒冷街上的欢乐声、新郎和新娘的欢笑声全部消失,因为大地必荒凉。”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 7:1-34

Chipembedzo Chabodza Nʼchopanda Phindu

1Mawu amene Yehova anayankhula kwa Yeremiya ndi awa, 2“Ima pa chipata cha Nyumba ya Yehova ndipo kumeneko ukalalikire uthenga uwu:

“ ‘Imvani mawu a Yehova, inu nonse anthu a ku Yuda amene mumalowa pa chipata ichi kudzapembedza Yehova. 3Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu, ndipo ndidzakulolani kukhala pa malo ano. 4Musamakhulupirire mawu anu achinyengo onena kuti, ‘Ino ndi Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova!’ 5Ngati mutasinthadi makhalidwe anu ndi zochita zanu, ndi kumachitirana zolungama, 6ngati mutaleka kuzunza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye ndi kuleka kupha anthu osalakwa pa malo ano, ndipo ngati muleka kutsatira milungu ina, kuti ingakuwonongeni, 7Ine ndidzakulolani kukhala pa malo ano, mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu mpaka muyaya. 8Koma onani, inu mukudalira mawu abodza amene alibe phindu.

9“Kodi inu muziba ndi kupha, kuchita chigololo ndi kulumbira monama, kufukiza lubani kwa Baala ndi kutsatira milungu ina imene simunayidziwe, 10ndipo kenaka nʼkubwera kudzayima pamaso panga mʼNyumba ino, Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langa, inu nʼkumati, ‘Tapulumuka.’ Mwapulumuka kuti muzichitabe zonyansazi? 11Kodi Nyumba ino imene imadziwika ndi Dzina langa, yasanduka phanga la anthu olanda zinthu anzawo mwachifwamba inu mukuona? Komatu ndakhala ndi kuziona zonsezi! akutero Yehova.”

12“ ‘Pitani tsopano ku malo anga ku Silo, malo amene poyamba ankadziwika ndi Dzina langa, ndipo mukaone zimene ndinachita kumeneko chifukwa cha kuyipa kwa anthu anga Aisraeli. 13Tsono popeza munkachita zonsezi, ngakhale Ine kukuyankhulani koma inu osamvera, kukuyitanani koma inu osayankha, 14choncho ndidzachita pa Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langayi, Nyumba ya Yehova imene mumayidalira, malo amene ndinapereka kwa inu ndi makolo anu, zomwe ndinachita ku Silo. 15Ndidzakuthamangitsani pamaso panga, ngati momwe ndinachitira abale anu onse, anthu a Efereimu.’ ”

16“Choncho iwe Yeremiya usawapempherere anthu awa ngakhale kuwapepesera kapenanso kuwapembedzera; usandidandaulire, chifukwa Ine sindidzakumvera. 17Kodi sukuona zimene akuchita mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu? 18Ana akutorera nkhuni, abambo akusonkha moto, ndipo amayi akukanda ufa kuti aphike makeke oti akapereke nsembe kwa mfumukazi yazakumwamba. Iwo amathira nsembe ya zakumwa kwa milungu ina kuti andipsetse mtima. 19Koma kodi akuvutitsa Ine? Kodi sakungodzivuta okha, ndi kudzichititsa manyazi? akutero Yehova.”

20“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Ndidzatsanulira mkwiyo wanga pa Nyumba yangayi, anthu, nyama, mitengo ndi zipatso zomwe. Mkwiyowo udzakhala ngati moto wosazimitsika.

21“Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Wonjezerani nsembe zanu zopsereza pa nsembe zanu zinazo ndipo mudye nyama yakeyo! 22Pakuti pamene ndinatulutsa makolo anu ku Igupto ndi kuyankhula nawo, sindinawalamulire kuti azipereka nsembe zopsereza kapena nsembe zinazo, 23koma ndinawalamula kuti: Mverani Ine, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata zonse zimene ndakulamulirani, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino. 24Koma anthuwo sanamvere kapena kulabadira; mʼmalo mwake anapitirira kusamvera ndi mitima yawo yoyipa. Iwo anabwerera mʼmbuyo mʼmalo mopita patsogolo. 25Kuyambira tsiku limene makolo awo anachoka ku Igupto mpaka lero lino, ndakhala ndikuwatumizira atumiki anga, aneneri. 26Koma anthuwo sanandimvere kapena kusamalira. Anawumitsa mitima yawo ndi kuchita zoyipa kuposa makolo awo.

27“Ngakhale iwe uwawuze zonsezi koma sadzakumvera. Ngakhale uwayitane koma sadzakuyankha. 28Nʼchifukwa chake udzawawuze kuti, ‘Uwu ndi mtundu wa anthu umene sunamvere Yehova Mulungu wake, wosalola kulangizidwa. Choonadi chatha; chazimirira pa milomo yawo.’

29“Tsono meta tsitsi lako ndi kulitaya. Ulire kwambiri pa zitunda zopanda zomera, pakuti Yehova waukana ndi kuwusiya mʼbado umene wamukwiyitsawu.”

Chigwa cha Imfa

30“Anthu a ku Yuda achita zoyipa pamaso panga, akutero Yehova. Ayimika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imadziwika ndi Dzina langa ndipo ayipitsa. 31Amanga nsanja yopembedzera Tofeti mʼChigwa cha Hinomu kuti apserezereko ana awo aamuna ndi aakazi. Zimenezi Ine sindinawalamulire ngakhale kuziganizira nʼkomwe. 32Nʼchifukwa chake masiku akubwera, akutero Yehova, pamene anthu sadzawatchulanso malowo Tofeti kapena Chigwa cha Hinomu, koma adzawatchula Chigwa cha Imfa, chifukwa adzakwirira anthu akufa ku Tofeti mpaka osapezekanso malo owayika. 33Ndipo mitembo ya anthu amenewa idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo zakuthengo, ndipo palibe wina amene adzazipirikitse. 34Ndidzathetsa nyimbo zonse zachisangalalo ndi zachikondwerero mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu. Sikudzamvekanso mawu a chikondwerero a mkwatibwi ndi mkwati pakuti dzikolo lidzasanduka chipululu.”