耶利米书 41 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

耶利米书 41:1-18

基大利被杀

1七月,王室宗亲、犹大王的大臣、以利沙玛的孙子、尼探雅的儿子以实玛利带着十个人去米斯巴亚希甘的儿子基大利。趁在米斯巴一同吃饭的时候, 2尼探雅的儿子以实玛利和同来的十个人突然起来拔刀杀了巴比伦王委任管理犹大沙番的孙子、亚希甘的儿子基大利3还杀了所有在米斯巴基大利在一起的犹大人和那里的迦勒底士兵。

4第二天,基大利被杀的事仍无人知道。 5当天,从示剑示罗撒玛利亚来了八十个人,他们剃了胡须,撕裂衣服,割破身体,手里拿着素祭和乳香要去耶和华的殿。 6以实玛利就从米斯巴出来迎接他们,边走边哭,见面后邀请他们去见亚希甘的儿子基大利7到了城中,以实玛利和部下便屠杀他们,弃尸于蓄水池中。 8其中有十个人对以实玛利说:“请不要杀我们,我们在田野里藏了许多大麦、小麦、油和蜜。”他就没有杀他们。 9以实玛利抛尸的地方是个很大的蓄水池,是从前亚撒王为抵御以色列巴沙而修建的。尼探雅的儿子以实玛利用被杀者的尸体填满了蓄水池。 10以实玛利还掳去了留在米斯巴的公主和其他人。护卫长尼布撒拉旦曾委任亚希甘的儿子基大利管理这些人。尼探雅的儿子以实玛利带着俘虏前往亚扪

11加利亚的儿子约哈难和其他将领听说尼探雅的儿子以实玛利的所作所为, 12便率领部下去攻打他,在基遍的大水池边追上了他。 13-14以实玛利米斯巴掳走的人看见约哈难和众将领,喜出望外,都转身投奔约哈难15尼探雅的儿子以实玛利带着八个人逃脱约哈难的追击,前往亚扪16加利亚的儿子约哈难和众将领从基遍救回了那些被掳走的士兵、妇孺和宫廷侍臣。 17他们启程前往埃及,途中在伯利恒附近的基罗特金罕住下。 18他们是害怕迦勒底人才逃往埃及的,因为尼探雅的儿子以实玛利杀了巴比伦王委任管理犹大亚希甘的儿子基大利

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 41:1-18

1Pa mwezi wachisanu ndi chiwiri Ismaeli mwana wa Netaniya, mdzukulu wa Elisama amene anali wa banja laufumu ndiponso mmodzi wa atsogoleri a ankhondo a mfumu, anabwera ku Mizipa kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ndi anthu khumi. Pamene ankadya naye kumeneko, 2Ismaeli mwana wa Netaniya pamodzi ndi anthu khumi aja anayimirira ndi kupha ndi lupanga Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani. Choncho anapha munthu amene mfumu ya ku Babuloni inamusankha kukhala bwanamkubwa wa dzikolo. 3Ismaeli anaphanso Ayuda onse amene anali pamodzi ndi Gedaliya ku Mizipa, kuphatikizanso asilikali a Ababuloni amene anali ku Mizipako.

4Mmawa mwake, anthu asanadziwe kuti Gedaliya waphedwa, 5kunafika anthu 80 ochekera ku Sekemu, Silo ndi Samariya, amene anali atameta ndevu zawo, atangʼamba zovala zawo ndi kudzichekacheka. Iwowa anatenga chopereka cha ufa ndi lubani kuti adzapereke ku Nyumba ya Yehova. 6Ismaeli mwana wa Netaniya anachoka ku Mizipa akulira kupita kukakumana nawo. Atakumana nawo, iye anati, “Bwerani mudzaonane ndi Gedaliya mwana wa Ahikamu.” 7Atafika pakati pa mzinda, Ismaeli mwana wa Netaniya pamodzi ndi anthu amene anali naye anawapha anthuwo ndi kuwaponya mʼchitsime. 8Koma anthu khumi a gululo anawuza Ismaeli kuti, “Musatiphe! Tili ndi tirigu ndi barele, mafuta ndi uchi, zimene tabisa mʼmunda.” Choncho anawasiya ndipo sanawaphere pamodzi ndi anzawo aja. 9Tsono chitsime chimene anaponyamo mitembo ya anthu amene anawaphawo pamodzi ndi mtembo wa Gedaliya chinali chimene mfumu Asa anachikumba poopsedwa ndi Baasa mfumu ya Israeli. Ismaeli mwana wa Netaliya anachidzaza ndi mitembo.

10Pambuyo pake Ismaeli anatenga ukapolo anthu ena onse amene anali ku Mizipa: ana aakazi a mfumu pamodzi ndi ena onse amene anatsalira kumeneko, amene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anapatsa Gedaliya mwana wa Ahikamu kuti akhale bwanamkubwa wawo. Ismaeli mwana wa Netaliya anatenga ukapolo anthuwa ndi kuwoloka nawo kumapita ku dziko la Aamoni.

11Pamene Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali naye pamodzi anamva zoyipa zonse zimene Ismaeli mwana wa Netaniya anachita, 12anatenga ankhondo awo onse kupita kukamenyana ndi Ismaeli mwana wa Netaniya. Anakamupeza kufupi ndi chidziwe chachikulu cha ku Gibiyoni. 13Pamene anthu onse amene Ismaeli anawagwira anaona Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo amene anali naye, anasangalala. 14Anthu onse amene Ismaeli anawagwira ukapolo ku Mizipa anabwerera ndi kupita kwa Yohanani mwana wa Kareya. 15Koma Ismaeli pamodzi ndi anthu ake asanu ndi atatu, anathawa Yohanani ndi kuthawira kwa Aamoni.

Kuthawira ku Igupto

16Kenaka Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali naye anatsogolera anthu onse otsala a ku Mizipa amene anawapulumutsa kwa Ismaeli mwana wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wa Ahikamu. Anthu amenewa anali: asilikali, akazi, ana ndi amuna ofulidwa otumikira mfumu amene anawatenga ku Gibiyoni. 17Ndipo ananyamuka nayima ku Geruti Kimuhamu pafupi ndi Betelehemu pa ulendo wawo wopita ku Igupto 18kuthawa Ababuloni. Iwo anaopa Ababuloniwo chifukwa Ismaeli mwana wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wa Ahikamu, amene mfumu ya ku Babuloni inamuyika kukhala bwanamkubwa wa dzikolo.