箴言 28 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

箴言 28:1-28

1恶人未被追赶也逃窜,

义人坦然无惧如雄狮。

2国中有罪,君王常换;

国有哲士,长治久安。

3穷人28:3 穷人”有些抄本作“暴君”。欺压贫民,

如暴雨冲毁粮食。

4背弃律法的称赞恶人,

遵守律法的抗拒恶人。

5邪恶之人不明白公义,

寻求耶和华的全然明白。

6行为正直的穷人,

胜过行事邪僻的富人。

7遵守律法的是智慧之子,

与贪食者为伍令父蒙羞。

8人放高利贷牟利,

等于为扶贫者积财。

9人若不听从律法,

他的祷告也可憎。

10引诱正直人走邪道,

必掉进自己设的陷阱;

但纯全无过的人必承受福分。

11富人自以为有智慧,

却被明智的穷人看透。

12义人得胜,遍地欢腾;

恶人当道,人人躲藏。

13自掩其罪,必不亨通;

痛改前非,必蒙怜悯。

14敬畏上帝必蒙福,

顽固不化必遭祸。

15暴虐的君王辖制穷人,

如咆哮的狮、觅食的熊。

16昏庸的君王残暴不仁,

恨不义之财的享长寿。

17背负血债者必终生逃亡,

谁也不要帮他。

18纯全无过的必蒙拯救,

行为邪僻的转眼灭亡。

19勤奋耕耘,丰衣足食;

追求虚荣,穷困潦倒。

20忠信的人必大蒙祝福,

急于发财的难免受罚。

21徇私偏袒实不可取,

人却为一饼而枉法。

22贪婪的人急于发财,

却不知贫穷即将临到。

23责备人的至终比谄媚者更受爱戴。

24窃取父母之财而不知罪者与匪类无异。

25贪得无厌的人挑起纷争,

信靠耶和华的富足昌盛。

26愚人心中自以为是,

凭智慧行事的平安稳妥。

27周济穷人的一无所缺,

视而不见的多受咒诅。

28恶人当道,人人躲藏;

恶人灭亡,义人增多。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 28:1-28

1Munthu woyipa amathawa ngakhale palibe wina womuthamangitsa,

koma wolungama ndi wolimba mtima ngati mkango.

2Pamene mʼdziko muli kuwukirana, dzikolo limakhala ndi olamulira ambiri,

koma anthu omvetsa ndi odziwa zinthu bwino ndiwo angakhazikitse bata mʼdzikolo nthawi yayitali.

3Munthu wosauka amene amapondereza osauka anzake

ali ngati mvula yamkuntho imene imawononga mbewu mʼmunda.

4Amene amakana malamulo amatamanda anthu oyipa,

koma amene amasunga malamulo amatsutsana nawo.

5Anthu oyipa samvetsa za chiweruzo cholungama,

koma amene amafuna kuchita zimene Yehova afuna amachimvetsetsa bwino.

6Munthu wosauka wa makhalidwe abwino

aposa munthu wolemera wa makhalidwe okhotakhota.

7Amene amasunga malamulo ndi mwana wozindikira zinthu,

koma amene amayenda ndi anthu adyera amachititsa manyazi abambo ake.

8Amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja chochuluka

amakundikira chumacho anthu ena, amene adzachitira chifundo anthu osauka.

9Wokana kumvera malamulo

ngakhale pemphero lake lomwe limamunyansa Yehova.

10Amene amatsogolera anthu olungama kuti ayende mʼnjira yoyipa

adzagwera mu msampha wake womwe,

koma anthu opanda cholakwa adzalandira cholowa chabwino.

11Munthu wolemera amadziyesa kuti ndi wanzeru,

koma munthu wosauka amene ali ndi nzeru zodziwa zinthu amamutulukira.

12Pamene olungama apambana pamakhala chikondwerero chachikulu;

koma pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro, anthu amabisala.

13Wobisa machimo ake sadzaona mwayi,

koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo.

14Ndi wodala munthu amene amaopa Yehova nthawi zonse,

koma amene aumitsa mtima wake adzagwa mʼmavuto.

15Ngati mkango wobuma kapena chimbalangondo cholusa

ndi mmenenso amakhalira munthu woyipa akamalamulira anthu osauka.

16Wolamulira amene samvetsa zinthu ndiye amakhala wankhanza

koma amene amadana ndi phindu lopeza mwachinyengo adzakhala ndi moyo wautali.

17Munthu amene wapalamula mlandu wopha munthu

adzakhala wothawathawa mpaka imfa yake;

wina aliyense asamuthandize.

18Amene amayenda mokhulupirika adzapulumutsidwa

koma amene njira zake ndi zokhotakhota adzagwa mʼdzenje.

19Amene amalima mʼmunda mwake adzakhala ndi chakudya chochuluka,

koma amene amangosewera adzakhala mʼmphawi.

20Munthu wokhulupirika adzadalitsika kwambiri,

koma wofuna kulemera mofulumira adzalangidwa.

21Kukondera si kwabwino,

ena amachita zolakwazo chifukwa cha kachidutswa ka buledi.

22Munthu wowumira amafunitsitsa kulemera

koma sazindikira kuti umphawi udzamugwera.

23Amene amadzudzula mnzake potsiriza pake

mnzakeyo adzamukonda kwambiri, kupambana amene amanena mawu oshashalika.

24Amene amabera abambo ake kapena amayi ake

namanena kuti “kumeneko sikulakwa,”

ndi mnzake wa munthu amene amasakaza.

25Munthu wadyera amayambitsa mikangano,

koma amene amadalira Yehova adzalemera.

26Amene amadzidalira yekha ndi chitsiru,

koma amene amatsata nzeru za ena adzapulumuka.

27Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu,

koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri.

28Pamene anthu oyipa apatsidwa ulamuliro anthu amabisala,

koma anthu oyipa akawonongeka olungama amapeza bwino.