申命记 11 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

申命记 11:1-32

要听从耶和华

1“你们要爱你们的上帝耶和华,时刻遵守祂的吩咐、律例、典章和诫命。 2要记住,我现在是对你们,而不是对你们的孩子说话。他们没有亲身经历、亲眼见过你们上帝耶和华的管教、威严、大能的手和伸出的臂膀; 3祂怎样在埃及行神迹奇事对付法老及其国家; 4怎样使红海淹没追赶你们的埃及军队和车马,将他们永远毁灭; 5怎样在旷野一路看顾你们,一直来到这里; 6怎样对付吕便以利押的儿子大坍亚比兰,使大地在以色列人当中裂开,吞没了他们及其家人、帐篷和所有随从。 7你们亲眼目睹了耶和华的这些伟大作为。

8“因此,你们要遵守我今天吩咐你们的诫命,以便有力量过河攻取你们将要攻取的土地, 9长久居住在耶和华起誓赐给你们祖先及其后裔的奶蜜之乡。 10那片土地不像你们离开的埃及。在埃及你们撒种后,要像浇菜园一样辛勤灌溉11:10 辛勤灌溉”希伯来文是“用脚灌溉”。11而你们将要占领的那片土地却有山有谷,雨水充足, 12你们的上帝耶和华从岁首到年终时时看顾那里。

13“如果你们谨遵我今天吩咐你们的诫命,全心全意地爱你们的上帝耶和华,事奉祂, 14祂就会按时降下秋雨和春雨,使你们收获谷物、新酒和油, 15有草场饲养牲畜,丰衣足食。 16你们要谨慎,免得被迷惑,转而祭拜、供奉其他神明。 17否则,耶和华必向你们发怒,使天不下雨、地无出产,以致你们在祂赐给你们的佳美之地上迅速灭亡。

18“所以,你们要把我的这些吩咐铭记在心,系在手上,戴在额上作记号; 19要用这些话教导你们的儿女,无论在家在外、或起或卧,都要讲论; 20也要写在城门上和自家的门框上。 21这样,你们及子孙就可以生活在耶和华起誓赐给你们祖先的土地上,与天地同长。 22如果你们谨遵我吩咐你们的这一切诫命——爱你们的上帝耶和华,遵行祂的旨意,依靠祂, 23耶和华就会为你们赶走那些比你们强大的民族,你们也必占领他们的土地。 24你们脚掌踏过的地方都要归你们。你们的疆界南到旷野,北到黎巴嫩,东到幼发拉底河,西到地中海。 25所到之处无人能抵挡你们,因为你们的上帝耶和华会使那些地方的人对你们充满惧怕,正如祂对你们的应许。

26“看啊,我今天把祝福和咒诅摆在你们面前。 27你们若遵行我今天吩咐你们的诫命,就会得到祝福。 28你们若不遵行你们的上帝耶和华的诫命,偏离我今天吩咐你们当走的道路,随从不认识的神明,必受咒诅。 29你们的上帝耶和华带领你们进入并占领那片土地时,你们要在基利心山上宣告祝福,在以巴路山上宣告咒诅。 30基利心山和以巴路山属于住在亚拉巴迦南人,位于约旦河西岸的日落之处,在吉甲对面,靠近摩利橡树。 31你们穿过约旦河,占领耶和华赐给你们的土地,定居下来以后, 32要谨遵我今天颁布给你们的一切律例和典章。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 11:1-32

Kukonda ndi Kumvera Yehova

1Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndipo nthawi zonse muzitsata zimene Iyeyo anakulamulani, malangizo, zikhazikitso ndi malamulo ake. 2Lero kumbukirani kuti si ana anu amene anaona ndi kulawa chilango cha Yehova Mulungu wanu: ukulu wake, dzanja lake lamphamvu, mkono wake wotambasuka; 3zizindikiro zozizwitsa zimene anazionetsa ndi zinthu zimene anazichita mʼkati mwa Igupto, Farao mfumu ya Igupto ndi kwa dziko lake lonse; 4zimene Iye anachita kwa gulu lankhondo la Aigupto, kwa akavalo ndi magaleta awo, mmene Iye anawamizira ndi madzi a mu Nyanja Yofiira pamene amakuthamangitsani, ndi mmene Yehova anawagonjetsera kufikira lero. 5Si ana anu amene anaona zimene Iye anakuchitirani mʼchipululu kufikira pamene munafika pa malo anu, 6ndi zimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana aamuna a Eliabu mwana wa Rubeni, pamene nthaka inatsekula pakamwa pake pakati pa Aisraeli onse ndi kuwameza pamodzi ndi katundu wawo, matenti awo ndi chilichonse chawo. 7Koma ndinuyo amene munaona ntchito zonse zikuluzikulu zimenezi Yehova anakuchitirani.

8Tsono muzisunga malamulo onse amene ndikukupatsani lero kuti mukhale ndi mphamvu ndi kuti mupite kukalanda mʼdziko limene mwakhala pangʼono kulowamo mukawoloka Yorodani, 9ndiponso kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova analumbira kupatsa makolo anu ndi zidzukulu zawo, lomwe ndi dziko loyenda mkaka ndi uchi. 10Dziko limene mukukalanda ndi kulowamo silokhala ngati dziko la ku Igupto kumene mukuchokera ayi, kuja mumadzala mbewu ndi kumathirira ndi mapazi anu ngati ku dimba. 11Koma dziko limene mukalande mukawoloka Yorodani ndi dziko la mapiri ndi zigwa, dziko limene limalandira mvula kuchokera kumwamba. 12Ili ndi dziko limene Yehova Mulungu wanu amalisamalira. Maso a Yehova Mulungu wanu amaliyangʼanira nthawi zonse kuchokera ku mayambiriro a chaka mpaka kumapeto kwake.

13Choncho mukasunga mokhulupirika malamulo amene ndikukupatsani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iyeyo ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, 14pamenepo ndidzatumiza mvula mʼdziko mwanu pa nthawi yake mʼnyengo ya dzinja ndi chilimwe, kuti mudzakolole tirigu wambiri ndi kuti mudzakhale ndi vinyo watsopano ndi mafuta. 15Ndidzakupatsani udzu mʼminda mwanu woti muzidzadyetsera ngʼombe zanu ndipo inuyo mudzadya ndi kukhuta.

16Dzisamalireni nokha, kuopa kuti mungakopeke mtima ndi kubwerera mʼmbuyo kuyamba kutumikira milungu ina ndi kumayigwadira. 17Mukatero Yehova Mulungu wanu adzakukwiyirani kwambiri, nadzaletsa thambo kuti lisabweretsenso mvula ndipo dziko silidzapereka zokolola. Choncho mudzawonongeka msanga mʼdziko limene Yehova akukupatsani. 18Sungani mawu amenewa mu mtima mwanu ndi mʼmaganizo mwanu, muwamangirire pa mikono yanu ndipo muwayike pamphumi panu. 19Mawuwa muziphunzitsa ana anu, muzikamba za iwo pamene mukhala pansi mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mugona ndi pamene mukudzuka. 20Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu, 21kuti inu ndi ana anu mukhale mʼdziko limene Yehova analumbira kupatsa makolo anu mpaka kalekale monga umakhalira mlengalenga pamwamba pa dziko.

22Mukatsatira mosamalitsa malamulo amene ndikukupatsaniwa, kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda mʼnjira zake zonse ndi kumugwiritsitsa Iye 23Yehova adzapirikitsa mitundu ina yonseyi inu musanafike ndipo mudzagonjetsa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa inu. 24Malo aliwonse amene mudzaponda adzakhala anu: dziko lanu lidzachokera ku chipululu mpaka ku Lebanoni, ndi ku Mtsinje wa Yufurate mpaka ku nyanja ya kumadzulo. 25Palibe munthu amene adzalimbana nanu. Monga analonjezera, Yehova adzachititsa kuti anthu onse mʼdziko limene mukupitalo adzachite nanu mantha ndi kukuopani.

26Taonani, lero ndikuyika dalitso ndi temberero pakati panu, 27dalitso ngati mumvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani lero. 28Temberero ngati simumvera malamulo a Yehova Mulungu wanu ndi kupatuka pa njira imene ndikulamulirani lero potsata milungu ina imene simunayidziwe. 29Yehova Mulungu wanu akakakufikitsani mʼdziko mukukalandalo kuti mulowemo mukanene za madalitso pa Phiri la Gerizimu, ndi za matemberero pa Phiri la Ebala. 30Monga mudziwa, mapiriwa ali kutsidya kwa Yorodani, kumadzulo kolowera dzuwa, kufupi ndi mitengo ya thundu ya More, mʼdziko la Akanaani aja okhala ku Araba moyangʼanana ndi Giligala. 31Mwatsala pangʼono kuwoloka Yorodani kuti mulowe ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. Mukadzalitenga dzikolo ndi kukhalamo, 32mudzaonetsetse kuti mukumvera malangizo ndi malamulo amene ndikukuwuzani lero.