民数记 9 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

民数记 9:1-23

逾越节

1以色列人离开埃及后第二年的一月,耶和华在西奈旷野对摩西说: 2以色列人要在指定的时间守逾越节, 3就是在一月十四日黄昏按照有关的律例和典章守逾越节。” 4于是,摩西吩咐以色列人守逾越节。 5一月十四日黄昏,以色列人照耶和华对摩西的吩咐,在西奈山守逾越节。

6可是,有几个人因碰到死尸而不洁净,不能在那天守逾越节,他们就来见摩西亚伦7说:“我们不过因碰到死尸而不洁净,为什么不准我们跟其他以色列人一起在指定的时间向耶和华献供物?” 8摩西说:“你们等一下,我要去听听耶和华对这事有什么吩咐。”

9耶和华对摩西说: 10“你把以下条例告诉以色列人。

“如果你们或你们的子孙中有人因为碰了死尸而不洁净,或是出了远门,可以改期为耶和华守逾越节。 11他们可以在二月十四日黄昏守逾越节,要配无酵饼和苦菜一起吃逾越节的羊羔。 12食物不可留到天明,也不可折断羊羔的一根骨头。要遵守逾越节的一切律例。 13如果有人是洁净的,又没有出远门,却不守逾越节,要将他从民中铲除。他不在指定的时间向耶和华献供物,就必须自负罪责。 14如果寄居在你们中间的外族人也想为耶和华守逾越节,他们也要遵守这些律例和典章。不论是外族人还是以色列人,都要遵守同样的律例。”

云彩遮盖会幕

15安放约柜的圣幕支起来那天,云彩遮盖了它。当晚,云彩整夜像火焰一般。 16之后,每天如此:白天云彩遮盖圣幕,晚上云彩像火。 17云彩什么时候从圣幕上升起,以色列人就启行;云彩在哪里停下来,以色列人就在哪里安营。 18他们无论启行还是安营,都遵照耶和华的吩咐。云彩在圣幕上停留多久,他们就安营多久。 19有时云彩在圣幕上停留多日,他们就遵照耶和华的吩咐安营多日。 20有时云彩在圣幕上只停留几天,他们就遵照耶和华的吩咐只安营几天。随后再照耶和华的吩咐启行。 21有时云彩整夜停留在圣幕上,到早晨才升起,他们就早晨才启行。不管白天黑夜,云彩一升起,他们就启行。 22不管是两天、一个月或是一年,只要云彩停留在圣幕上,以色列人就安营不动;云彩一升起,他们就启行。 23他们遵照耶和华的吩咐安营,也遵照耶和华的吩咐启行。他们遵行耶和华借摩西吩咐的话。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 9:1-23

Paska

1Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai pa mwezi woyamba wa chaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, nati, 2“Aisraeli azichita Paska pa nthawi yake yoyikika. 3Muzichita Paska pa nthawi yake yoyikika, madzulo a tsiku la 14 la mwezi uno, potsata malamulo ndi malangizo ake.”

4Choncho Mose anawuza Aisraeli kuti azichita Paska, 5ndipo anachitadi Paskayo mʼchipululu cha Sinai madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose.

6Koma ena a iwo sanathe kuchita nawo Paska pa tsiku limenelo chifukwa anali odetsedwa chifukwa chokhudza mtembo. Choncho anabwera kwa Mose ndi Aaroni tsiku lomwelo, 7ndipo anawuza Moseyo kuti, “Ife tadetsedwa chifukwa cha mtembo wa munthu. Nʼchifukwa chiyani taletsedwa kupereka nsembe kwa Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena pa nthawi yake?”

8Mose anawayankha kuti, “Dikirani mpaka nditamva zimene Yehova walamula zokhudza Inu.”

9Ndipo Yehova anawuza Mose kuti, 10“Uza Aisraeli kuti, ‘Pamene wina mwa inu kapena zidzukulu zanu adetsedwa chifukwa chokhudza mtembo wa munthu, kapena akakhala pa ulendo, akhoza kuchita nawo Paska ya Yehova. 11Azichita chikondwererochi madzulo a pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Azidya mwana wankhosa wamwamuna pamodzi ndi buledi wopanda yisiti ndi ndiwo zowawa zamasamba. 12Iwo asasiye nyama ina iliyonse mpaka mmawa. Asaswe mafupa aliwonse. Pamene akuchita chikondwerero cha Paska, atsate malangizo onse. 13Koma ngati munthu wina ali woyeretsedwa ndipo sali pa ulendo koma alephera kuchita Paska, munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake chifukwa sanabweretse chopereka cha Yehova pa nthawi yake. Munthu ameneyo adzalangidwa chifukwa cha tchimo lake.

14“ ‘Mlendo amene akukhala pakati panu, nafuna kuchita nawo Paska ya Yehova, achite nawo motsata malamulo ndi malangizo ake. Muzikhala ndi malangizo ofanana a Paska; mbadwa kapena mlendo.’ ”

Mtambo Pamwamba pa Chihema

15Pa tsiku limene anayimika chihema, tenti ya umboni, mtambo unaphimba chihemacho. Kuyambira madzulo mpaka mmawa, mtambo umene unali pamwamba pa chihemacho unkaoneka ngati moto. 16Zinkachitika motere mosalekeza: mtambo unkakhala pamwamba pa chihema, ndipo usiku unkaoneka ngati moto. 17Nthawi ina iliyonse mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso, ndipo paliponse pamene mtambo wayima, Aisraeli ankamangapo misasa. 18Aisraeli ankasamuka pamalopo Yehova akawalamula, ndipo ankamanganso misasa Iyeyo akawalamula. Nthawi yonse imene mtambowo wayima pa chihema, ankakhalabe mʼmisasa yawo. 19Mtambowo ukakhala pa chihema nthawi yayitali, Aisraeli ankasungabe lamulo la Yehova ndipo iwo sankasamukanso. 20Nthawi zina mtambowo unkakhala pa chihemapo masiku owerengeka. Aisraeli ankamanga misasa molamulidwa ndi Yehova ndipo ankasamukanso molamulidwa ndi Iyeyo. 21Nthawi zina mtambo unkakhala kuyambira madzulo mpaka mmawa ndipo unkachoka mmawa mwake, ankasamuka. Kaya ndi masana kapena usiku, pamene mtambo wachoka, ankasamuka. 22Ngakhale mtambo ukhale pa chihema masiku awiri kapena mwezi kapena chaka, Aisraeli ankakhalabe pa msasa osachoka. Koma ukachoka, ankasamuka. 23Molamulidwa ndi Yehova ankamanga misasa yawo ndipo ankasamukanso Yehova akawalamula. Ankamvera lamulo la Yehova kudzera mwa Mose.