民数记 6 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

民数记 6:1-27

拿细耳人的条例

1耶和华对摩西说: 2“你把以下条例告诉以色列人。

“无论男女,如果许愿做拿细耳人,把自己献给耶和华, 3就要禁戒淡酒和烈酒、淡酒或烈酒做的醋、葡萄汁、葡萄和葡萄干。 4在做拿细耳人期间,葡萄树所结的,包括葡萄核和葡萄皮,都不可吃。 5在许愿做拿细耳人期间,不可用剃刀剃头,要任由头发生长,要保持圣洁,一直到献给耶和华的日期满了。 6在献给耶和华期间,不可挨近死尸, 7即使父母或是兄弟姊妹死了,也不可挨近,以免沾染不洁,因为他头上有将自己奉献给上帝的记号。 8在做拿细耳人期间,他是奉献给耶和华的人。 9如果有人在他身边暴毙,使他的头发沾染不洁,他要等到第七天洁净的日子剃掉头发。 10第八天,他要带两只斑鸠或雏鸽到会幕门口交给祭司。 11祭司要献一只作赎罪祭,另一只作燔祭,为他碰过死尸赎罪。他要在当日使头圣洁, 12重新开始过奉献给耶和华的日子,还要带一只一岁的公羊羔作赎过祭。他以前做拿细耳人的日子无效,因为他沾染了不洁之物。

13“献给耶和华的日子期满后,拿细耳人要遵行以下条例。他要被带到会幕门口, 14在那里献给耶和华一只毫无残疾、一岁的公羊羔作燔祭,一只毫无残疾、一岁母羊羔作赎罪祭,一只毫无残疾的公绵羊作平安祭, 15一篮调油的无酵细面饼和涂油的无酵薄饼,以及素祭和奠祭。 16祭司要把这些祭物带到耶和华面前,为他献上赎罪祭和燔祭, 17然后把公绵羊和无酵饼献给耶和华作平安祭,再献上素祭和奠祭。 18拿细耳人要在会幕门口剃掉作为奉献记号的头发,把头发放在平安祭的火里烧掉。 19拿细耳人剃头以后,祭司要取出一条煮好的公绵羊前腿,再从篮中拿出一块无酵饼和一块无酵薄饼,放在拿细耳人手中。 20然后,祭司要把这些祭物作为摇祭在耶和华面前摇一摇。这些祭物与作摇祭的胸肉和作举祭的腿肉一样,都是归给祭司的圣物。此后,拿细耳人便可以喝酒。

21“以上是许愿献供物给耶和华的拿细耳人当守的条例和当献的祭物。但如果他额外许愿献上力所能及之物,就必须还所许的愿。”

祭司的祝福

22耶和华对摩西说: 23“你告诉亚伦父子们要这样为以色列人祝福, 24‘愿耶和华赐福给你,保护你; 25愿耶和华笑颜垂顾你,施恩给你; 26愿耶和华恩待你,赐你平安。’ 27他们要奉我的名为以色列人祝福,我必赐福给他们。”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 6:1-27

Za Mnaziri

1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati mwamuna kapena mkazi afuna kuchita lonjezo lapadera, lonjezo lodzipatula yekha kwa Yehova ngati Mnaziri, 3sayenera kumwa vinyo kapena zakumwa zosasa ndipo asamamwe chakumwa chilichonse cha mphesa. Asamamwe madzi a mphesa kapena kudya mphesa zaziwisi kapena zowuma. 4Pa nthawi yonse imene ali Mnaziri, asamadye chilichonse chopangidwa kuchokera ku mphesa ngakhale mbewu zake kapena makungu ake.’

5“ ‘Pa nthawi yonse ya lonjezo lodzipatula yekhalo, asamete kumutu kwake ndi lumo. Akhale wopatulika mpaka nthawi yake yonse ya kudzipatula yekha kwa Yehova itatha. Alileke tsitsi la pamutu pake kuti likule.’ 6Pa nthawi yonse imene munthuyo wadzipatula yekha kwa Yehova asayandikire mtembo. 7Ngakhale abambo ake kapena amayi ake kapena mchimwene wake kaya mchemwali wake atamwalira, asadzidetse pokhudza mitembo yawo chifukwa kulumbira kwake kwa kudzipatula yekha kwa Yehova kuli pamutu pake. 8Munthuyo ndi wopatulika masiku onse odzipereka kwake kwa Yehova.

9“Ngati munthu wina afa mwadzidzidzi pafupi naye ndi kudetsa tsitsi lake loperekedwalo, amete mutu wake pa tsiku lodziyeretsa, tsiku lachisanu ndi chiwiri. 10Tsono pa tsiku lachisanu ndi chitatu abweretse nkhunda ziwiri kapena mawunda awiri anjiwa kwa wansembe pa khomo lolowera ku tenti ya msonkhano. 11Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yauchimo ndi ina nsembe yopsereza yotetezera tchimo chifukwa anachimwa popezeka pafupi ndi mtembo. Ndipo tsiku lomwelo apatulenso tsitsi la pamutu pake. 12Adzipereke kwa Yehova pa nthawi yodzipatula ndipo abweretse nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi ngati nsembe yopepesera. Masiku akale sawerengedwanso chifukwa anadzidetsa pa nthawi yodzipatulira kwake.

13“Tsono ili ndi lamulo la Mnaziri pamene nthawi yodzipatula kwake yatha: Abwere naye pa khomo la tenti ya msonkhano. 14Pamenepo apereke chopereka chake kwa Yehova: Nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi yopanda chilema kuti ikhale nsembe yopsereza, mwana wankhosa wamkazi mmodzi wopanda chilema kuti ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa imodzi yayikulu yayimuna kuti ikhale nsembe yachiyanjano, 15ndipo abwere pamodzi ndi nsembe yachakudya ndi nsembe yachakumwa ndi dengu la buledi wopanda yisiti, makeke opangidwa ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda ta buledi topakidwa mafuta.

16“Wansembe apereke zimenezi pamaso pa Yehova ndi kuchita nsembe ya uchimo ndi nsembe yopsereza. 17Apereke dengu la buledi wopanda yisiti ndiponso nsembe yachiyanjano kwa Yehova ya nkhosa yayimuna, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi chopereka cha chakumwa.

18“Mnaziriyo amete tsitsi limene analipereka lija pa khomo la tenti ya msonkhano. Atenge tsitsilo ndi kuliyika pa moto umene uli pansi pa nsembe yachiyanjano.

19“Mnaziriyo atatha kumeta tsitsi analiperekalo, wansembe ayike mʼmanja mwake mwendo wa mmwamba wankhosa yayimuna umene waphikidwa ndipo atengenso keke ndi kamtanda ka buledi, zonse zopanda yisiti zomwe zili mʼdengu lija. 20Wansembe aziweyule pamaso pa Yehova ngati nsembe yoweyula. Zimenezi ndi zopatulika ndipo ndi za wansembe pamodzi ndi chidale chimene anachiweyula ndi ntchafu yomwe anayipereka ija. Zitatha izi, Mnaziri akhoza kumwa vinyo.

21“Ili ndi lamulo la Mnaziri yemwe walonjeza kudzipereka kwa Yehova podzipatula yekha kuphatikiza pa zomwe angathe kukwaniritsa. Ayenera kukwaniritsa lonjezo lomwe wachitalo potsata lamulo la Mnaziri.”

Kupereka Mdalitso

22Yehova anawuza Mose kuti, 23“Uza Aaroni ndi ana ake aamuna kuti, ‘Umu ndi mmene muzidalitsira Aisraeli. Muzinena kuti,

24“ ‘Yehova akudalitse

ndi kukusunga;

25Yehova awalitse nkhope yake pa iwe,

nakuchitira chisomo;

26Yehova akweze nkhope yake pa iwe,

nakupatse mtendere.’ ”

27Choncho akadzatchula dzina langa podalitsa Aisraeli, Ine ndidzawadalitsadi.