撒迦利亚书 6 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

撒迦利亚书 6:1-15

四辆马车

1我又举目观看,见有四辆马车从两座铜山之间出来。 2第一辆车套着红马,第二辆车套着黑马, 3第三辆车套着白马,第四辆车套着斑点马,马都很雄壮。 4我问与我说话的天使:“主啊,这些马车是什么意思?” 5天使说:“他们是侍立在天下之主面前的四灵6:5 ”或译“风”。,正在出发。” 6套着黑马的车前往北方,套着白马的车前往西方6:6 前往西方”或译“跟在后面”。,套着斑点马的车前往南方。 7这些雄壮的马出来,迫不及待地要巡察大地。天使说:“你们去巡察大地吧!”它们便遵命而行。 8他又高声对我说:“看啊,那些到北方去的已在那里使我的心得到安慰。”

为约书亚加冕

9耶和华的话传给了我,说: 10“被掳到巴比伦黑玳多比雅耶大雅已经回来了,你要收集他们奉献的金银,并在当天去西番雅的儿子约西亚家。 11要用这些金银制作冠冕,戴在约撒答的儿子约书亚大祭司头上, 12告诉他,万军之耶和华说,‘看啊,那被称为大卫苗裔的要从自己的地方兴起,建造耶和华的殿。 13祂必建造耶和华的殿,带着王者的尊荣坐在宝座上掌权,宝座上也必坐着祭司6:13 宝座上也必坐着祭司”或译“并在宝座上做祭司”。,两者和谐共存。’ 14这冠冕要留在耶和华的殿中,作为对黑玳6:14 黑玳”希伯来文作“希连”。多比雅耶大雅西番雅的儿子约西亚6:14 约西亚”希伯来文作“贤”,意思是“恩慈者”。的纪念。”

15远方的人也要来建造耶和华的殿。那时你们便知道是万军之耶和华差遣我到你们这里来的。你们若全心遵从你们上帝耶和华的话,这事就必成就。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zekariya 6:1-15

Magaleta Anayi

1Ndinayangʼananso ndipo taonani ndinaona magaleta anayi akutuluka pakati pa mapiri awiri, mapiri amkuwa. 2Galeta loyamba limakokedwa ndi akavalo ofiira, lachiwiri ndi akavalo akuda, 3lachitatu ndi akavalo oyera, ndipo lachinayi ndi akavalo otuwa a mawanga ofiirira, onsewa anali akavalo amphamvu kwambiri. 4Ndinafunsa mngelo amene amayankhula nane uja kuti, “Kodi mbuye wanga chimenechi nʼchiyani?”

5Mngeloyo anandiyankha kuti, “Imeneyi ndi mizimu inayi yakumwamba, imene ikuchokera pamaso pa Ambuye wa dziko lonse. 6Galeta la akavalo akuda likupita ku dziko la kumpoto, galeta la akavalo oyera likutsatira, ndipo galeta la akavalo amawanga ofiirira likupita ku dziko la kummwera.”

7Pamene akavalo amphamvuwa ankapita, anali ndi changu chofuna kuyendera dziko lapansi. Ndipo iye anati, “Pitani, kayendereni dziko lapansi!”

8Pamenepo anandiyitana, “Taona, akavalo amene apita ku dziko la kumpoto apumulitsa Mzimu wanga kumeneko.”

Chipewa Chaufumu cha Yoswa

9Yehova anayankhula nane kuti, 10“Landira mphatso kuchokera kwa anthu amene abwera ku ukapolo, Helidai, Tobiya ndi Yedaya, amene achokera ku Babuloni. Tsiku lomwelo pita ku nyumba ya Yosiya mwana wa Zefaniya. 11Tenga siliva ndi golide upange chipewa chaufumu, ndipo uchiyike pamutu pa mkulu wa ansembe, Yoswa mwana wa Yehozadaki. 12Muwuze kuti zimene akunena Yehova Wamphamvuzonse ndi izi: ‘Taonani, munthu wotchedwa Nthambi ndi ameneyu, ndipo adzaphuka pomwe alipo ndi kumanga Nyumba ya Yehova. 13Ndiye amene adzamange Nyumba ya Yehova, adzalandira ulemerero waufumu ndipo adzalamulira pa mpando wake waufumu. Adzakhalanso wansembe pa mpando wake waufumu. Ndipo padzakhala mtendere.’ 14Chipewa cha ufumucho adzachipereka kwa Helemu, Tobiya, Yedaya, ndi kwa Heni mwana wa Zefaniya, kuti chikhale chikumbutso mʼNyumba ya Yehova. 15Anthu okhala kutali adzabwera kudzathandiza kumanga Nyumba ya Yehova, ndipo iwe udzadziwa kuti Yehova Wamphamvuzonse wandituma kwa iwe. Zimenezi zidzachitika ngati mudzamvera mwachangu Yehova Mulungu wanu.”