撒母耳记上 5 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

撒母耳记上 5:1-12

约柜在非利士人手中

1非利士人将掳来的上帝的约柜从以便以谢抬到亚实突城, 2把它抬进大衮庙,放在大衮神像旁边。 3第二天早上,亚实突人起来,发现大衮神像倒在耶和华的约柜前,面伏于地,他们就把大衮神像扶起来,放回原处。 4次日早上起来,他们又发现大衮神像倒在耶和华的约柜前,面伏于地,头和双手都在门槛处折断了,只剩下躯干。 5因此,大衮的祭司和所有进亚实突大衮庙的人至今都不踏庙的门槛。 6耶和华重重地惩罚亚实突及附近村庄的居民,使他们都患上毒疮。 7亚实突人见此情形,就说:“以色列上帝的约柜不能留在我们这里,因为上帝重重地惩罚我们和我们的大衮神。” 8亚实突人召集了非利士所有的首领,问他们:“我们如何处理以色列上帝的约柜?”他们答道:“把它送到迦特去。”于是,众人把以色列上帝的约柜送到迦特9约柜抵达迦特的时候,耶和华攻击那城,使那里的男女老少都患了毒疮,全城惊恐不已。 10于是,他们把约柜送往以革伦以革伦的人看见上帝的约柜到了,就惊叫道:“他们把以色列上帝的约柜带来是要害死我们和我们的人民!” 11他们派人召集非利士的首领,说:“把以色列上帝的约柜送回原处吧,免得它杀害我们和我们的人民。”因为上帝重重地惩罚他们,全城都笼罩在死亡的恐惧中。 12那些没有死的人都饱受毒疮的折磨,城中的哭喊声上达于天。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Samueli 5:1-12

Bokosi la Chipangano Pakati pa Afilisti

1Afilisti atalanda Bokosi la Mulungu lija, analitenga kuchoka ku Ebenezeri kupita ku Asidodi. 2Kenaka anatenga Bokosi la Chipanganolo nabwera nalo ku nyumba ya Dagoni ndi kuliyika pambali pa Dagoni. 3Anthu a ku Asidodi atadzuka mmawa mwake, anangoona Dagoni atagwa pansi chafufumimba pamaso pa Bokosi la Yehova! Iwo anatenga Dagoni ndi kumuyimika pamalo pake. 4Koma mmawa mwakenso atadzuka, anaona Dagoni atagwa chafufumimba pamaso pa Bokosi la Yehova. Mutu wake ndi manja ake zinali zitaduka ndi kugwera pa khonde polowera, thunthu lake lokha ndilo linatsala. 5Nʼchifukwa chake mpaka lero ansembe a Dagoni kapena wina aliyense amene amalowa mʼkachisi wa Dagoni ku Asidodi saponda pa khonde.

6Yehova analanga koopsa anthu a ku Asidodi. Yehova anawawononga ndi kuwazunza ndi zithupsa Asidoniwa pamodzi ndi anthu a madera ozungulira. 7Anthu a ku Asidodi ataona zimene zimachitika anati, “Bokosi la Mulungu wa Israeli lisakhale kuno chifukwa akutizunza ife pamodzi ndi mulungu wathu Dagoni.” 8Choncho anayitana atsogoleri onse a Afilisti kuti asonkhane ndipo anawafunsa kuti, “Kodi Bokosi la Mulungu wa Israeli tichite nalo chiyani?”

Iwo anayankha kuti, “Bokosi la Mulungu wa Israeli lipite ku Gati.” Kotero analichotsa Bokosi la Mulungu wa Israelilo.

9Koma atafika nalo ku Gati, Yehova analanga mzindawo, ndipo anthu anachita mantha aakulu. Iye anazunza anthu a mu mzindawo, ana ndi akulu omwe, ndi zithupsa. 10Choncho anatumiza Bokosi la Mulungu ku Ekroni.

Koma Bokosi la Mulungu lija litangofika ku Ekroni, anthu a ku Ekroni analira kuti, “Abwera nalo Bokosi la Mulungu wa Israeli kwa ife kuti atiphe pamodzi ndi anthu athu.” 11Kotero iwo anayitana atsogoleri onse a Afilisti kuti asonkhane ndipo anati, “Chotsani Bokosi la Mulungu wa Israeli, libwerere ku malo ake. Tikapanda kutero lidzatipha ife ndi anthu athu.” Pakuti mu mzinda monse munali mantha aakulu kwambiri ndipo Mulungu ankawalanga kwambiri anthu a kumeneko. 12Anthu amene sanafe anavutika ndi zithupsa, ndipo kulira kwa anthu a mu mzindamo kunamveka kumwamba.