启示录 1 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

启示录 1:1-20

1以下是上帝赐给耶稣基督的启示,让祂把将来要发生的事指示祂的众奴仆。因此,祂差遣天使告诉祂的奴仆约翰2约翰便为自己所看见的一切——上帝的道和耶稣基督做见证。 3那位宣读这预言的人和那些听见并遵守其中内容的人有福了,因为日期近了。

问候七教会

4-5约翰写信给你们亚细亚的七间教会。愿昔在、今在、以后永在的上帝,祂宝座前的七灵1:4-5 七灵”指的就是圣灵,数字七代表完全,不是说有七个灵。和耶稣基督赐给你们恩典和平安。耶稣基督是忠心的见证人,是首先从死里复活的,是世上君王的首领。祂爱我们,用自己的血救我们脱离罪恶, 6使我们成为祭司的国度1:6 成为祭司的国度”或译“成为国度,做祭司”。来事奉祂的父上帝。愿祂得到一切荣耀和权柄,一直到永永远远。阿们!

7看啊!祂要驾云降临,世人都要看见祂,包括曾经刺祂的人。地上的万族都必因祂而哀哭。这事必定实现。阿们!

8主上帝说:“我是阿拉法,我是俄梅加1:8 阿拉法”和“俄梅加”分别是希腊文第一个和最后一个字母,故此句意即“我是始,我是终”。,我是昔在、今在、以后永在的全能者。”

基督的显现

9约翰是你们的弟兄,在耶稣里和你们患难与共、同享国度、一起忍耐。我因传扬上帝的道、为主耶稣做见证而到了拔摩海岛上。 10主日,我被圣灵感动,听见身后有号角般响亮的声音说: 11“把你所看见的写在书上,然后送给以弗所士每拿别迦摩推雅推喇撒狄非拉铁非老底嘉七间教会。”

12我转身看究竟是谁在对我说话,我看见七个金灯台, 13有一位好像人子耶稣的站在这些灯台中间。祂长袍垂脚,金带围胸, 14头与发白如羊毛、洁白如雪,眼睛像火焰, 15双脚像炉中冶炼过的铜一样光亮,声音如同洪涛之声。 16祂右手拿着七颗星,口中吐出一把两刃的利剑,面貌如烈日放光。

17我一看见祂,便扑倒在祂脚前,像死了一样。祂把右手按在我身上,说:“不要害怕!我是首先的,我是末后的, 18我是永活者。我曾经死过,但看啊,我永永远远活着。我掌握死亡和阴间的钥匙。 19所以,你要将所看见的一切——现在和将来要发生的事都记录下来。 20你所看见在我右手中的七颗星和七个金灯台的奥秘是,七颗星代表七间教会的天使1:20 天使”或译“信使”或“使者”,下同,可能指教会的守护天使,或者是教会的领袖。,七个灯台代表七间教会。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chivumbulutso 1:1-20

Mawu Oyamba

1Vumbulutso lochokera kwa Yesu Khristu, limene Mulungu anamupatsa kuti aonetse atumiki ake zimene zinayenera kuchitika posachedwa. Iye anatuma mngelo wake kuti adziwitse mtumiki wake Yohane, 2amene akuchitira umboni chilichonse chimene anachiona. Awa ndi Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu Khristu. 3Ngodala munthu amene awerenga mawu oneneratu zamʼtsogolo ndi iwo amene amamva ndi kusunga zolembedwa mʼbukuli pakuti nthawi yayandikira.

Malonje kwa Mipingo Isanu ndi Iwiri

4Ndine Yohane,

Kupita ku mipingo isanu ndi iwiri ya mʼchigawo cha Asiya.

Chisomo ndi mtendere kwa inu, kuchokera kwa Iye amene ali, amene analipo ndi amene akubwera ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala patsogolo pa mpando wake waufumu, 5ndiponso kuchokera kwa Yesu Khristu mboni yokhulupirika, woyamba kuukitsidwa, ndi wolamulira mafumu a dziko lapansi.

Kwa Iye amene amatikonda ndipo watimasula ku machimo athu ndi magazi ake, 6ndipo watisandutsa mafumu ndi ansembe kuti tizitumikira Mulungu ndi Atate ake. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu ku nthawi zosatha, Ameni.

7“Onani akubwera ndi mitambo,”

ndipo “Aliyense adzamuona,

ndi amene anamubaya omwe.”

Ndipo anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi “adzalira chingʼangʼadza chifukwa cha Iye.”

Zidzakhaladi momwemo, Ameni.

8“Ine ndine Alefa ndi Omega,” akutero Ambuye Mulungu Wamphamvuzonseyo “amene muli, amene munalipo, ndi amene mudzakhalapo.”

Wina Wokhala ngati Mwana wa Munthu

9Ine Yohane mʼbale wanu ndi mnzanu mʼmasautso ndi mu ufumu ndi mukupirira kwambiri, zomwe ndi zathu mwa Yesu, ndinali pa chilumba cha Patimo chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu. 10Pa tsiku la Ambuye ndinanyamulidwa ndi Mzimu ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mawu ofuwula ngati lipenga, 11amene anati, “Lemba mʼbuku zimene ukuziona ndipo uzitumize ku mipingo isanu ndi iwiri ya ku Efeso, Simurna, Pergamo, Tiyatira, Sarde, Filadefiya ndi ku Laodikaya.”

12Nditatembenuka kuti ndione amene amandiyankhulayo, ndinaona zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide. 13Pakati pa zoyikapo nyalezo ndinaona wina wooneka ngati Mwana wa Munthu atavala mkanjo wofika kumapazi ake ndipo anamangirira lamba wagolide pa chifuwa pake. 14Tsitsi lake linali loyera ngati thonje, kuyera ngati matalala, ndipo maso ake amawala ngati malawi amoto. 15Mapazi ake anali ngati chitsulo choti chili mʼngʼanjo yamoto, ndipo mawu ake anali ngati mkokomo wamadzi othamanga. 16Mʼdzanja lake lamanja ananyamula nyenyezi zisanu ndi ziwiri, ndipo mʼkamwa mwake munali lupanga lakuthwa konsekonse. Nkhope yake imawala ngati dzuwa lowala kwambiri.

17Nditamuona ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa. Kenaka Iye anasanjika dzanja lake lamanja pa ine nati, “Usachite mantha. Ndine Woyamba ndi Wotsiriza. 18Ine ndine Wamoyo; ndinali wakufa ndipo taona ndine wamoyo mpaka muyaya! Ndipo ndili ndi makiyi a imfa ndi Hade.

19“Chomwecho, lemba zimene waona, zimene zilipo panopa ndi zimene zidzachitike mʼtsogolo. 20Tanthauzo la nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene waziona mʼdzanja langa lamanja ndi la zoyikapo nyale zagolide zisanu ndi ziwiri ndi ili: Nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndi angelo a mipingo isanu ndi iwiri ija, ndipo zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zija ndi mipingo isanu ndi iwiri ija.”