历代志下 31 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

历代志下 31:1-21

希西迦的改革

1当一切都办妥后,所有在场的以色列人就前往犹大各城邑,打碎神柱,砍倒亚舍拉神像,又拆毁犹大便雅悯以法莲玛拿西境内所有的丘坛和祭坛,然后各自返回自己的城邑和家园。

2希西迦分派祭司和利未人的班次,使他们各司其职,献上燔祭和平安祭,在耶和华殿门内事奉,称谢、颂赞耶和华。 3王又从自己的产业中划分出一部分作为早晚的燔祭,以及安息日、朔日及耶和华律法规定的其他节期的燔祭。

4他又吩咐耶路撒冷的居民将祭司和利未人当得的份交给他们,好使他们专心执行耶和华的律法。 5谕旨一出,以色列人就献出许多初熟的五谷、新酒、新油、蜂蜜、田间的出产及各样物品的十分之一,数量极多。 6住在犹大各城的以色列人和犹大人也送来牛羊的十分之一,以及献给他们的上帝耶和华的圣物,就是十一奉献,把它们堆积成堆。 7他们从三月开始堆积,到七月才结束。 8希西迦与众官员来了,看见堆积起来的供物,就称颂耶和华,又为耶和华的以色列子民祝福。 9希西迦向祭司和利未人询问这些供物的事, 10撒督家族的亚撒利雅大祭司回答说:“自从民众把这些供物送到耶和华的殿里以来,我们不但吃得饱,还剩下许多。因为耶和华赐福给祂的子民,所以才有这么多剩余。”

11于是,希西迦下令在耶和华的殿里预备库房。他们预备好后, 12便忠心地把供物、十一奉献和圣物放进库房。利未歌楠雅总管这事,他的兄弟示每做助手。 13耶歇亚撒细雅拿哈亚撒黑耶利末约撒拔以列伊斯玛基雅玛哈比拿雅做监督协助歌楠雅和他兄弟示每,他们都是希西迦王和管理上帝殿的亚撒利雅指派的。 14看守东门的利未人音拿的儿子可利,负责管理民众自愿献给上帝的礼物,以及分发献给耶和华的供物和至圣之物。 15伊甸珉雅珉耶书亚示玛雅亚玛利雅示迦尼雅在祭司所在的各城忠心地协助可利,按照班次,不分老幼,将物品分给他们的弟兄。 16此外,他们还分给三岁及三岁以上、姓名记在家谱上、每天在耶和华的殿中按班次供职的男子, 17并分给按宗族登记在家谱上的祭司,按班次和职任分给二十岁及二十岁以上的利未人, 18也按照家谱分给他们的妻子儿女,因为他们诚心洁净自己。 19至于住在各城郊野做祭司的亚伦子孙,各城都有指定的人把应得之份分给祭司中所有的男子和登记在家谱上的利未人。

20希西迦犹大全境都如此行,做他的上帝耶和华视为良善、正直和忠心的事。 21无论是在上帝的殿中事奉,还是遵行律法和诫命,他都寻求他的上帝,尽心去做。因此,他行事顺利。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 31:1-21

1Zonse zitatha, Aisraeli onse amene anali kumeneko anapita ku mizinda ya ku Yuda, nakaphwanya miyala yachipembedzo ndi kudula mitengo ya mafano a Asera. Iwo anakawononga malo achipembedzo ndi maguwa ansembe amene anali mʼdziko lonse la Yuda, Benjamini, Efereimu ndi Manase. Atawononga zonsezi, Aisraeli anabwerera ku mizinda yawo ndi ku malo awo.

Zopereka ku Ntchito ya Chipembedzo

2Hezekiya anakhazikitsa magulu a ansembe ndi Alevi, gulu lililonse monga mwa ntchito zawo ngati ansembe kapena Alevi, kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, kutumikira, kuyamikira ndi kuyimba matamando pa zipata za ku malo okhala Yehova. 3Kuchokera pa chuma chake, mfumu inapereka nsembe zopsereza za mmawa ndi madzulo ndiponso nsembe zopsereza za pa Chikondwerero cha Masabata, Chikondwerero cha Mwezi Watsopano ndipo inakhazikitsa zikondwerero monga zinalembedwera mʼmalamulo a Yehova. 4Iyo inalamula anthu amene amakhala mu Yerusalemu kupereka gawo lawo kwa ansembe ndi Alevi kuti iwowo adzipereke ku malamulo a Yehova. 5Lamuloli atangolilengeza, Aisraeli anapereka mowolowamanja zipatso zoyamba kucha za tirigu, vinyo watsopano, mafuta ndi uchi ndi zonse zomwe nthaka yawo inabereka. Anabweretsa zochuluka kwambiri, chakhumi cha chilichonse. 6Aisraeli ndi Ayuda amene amakhala mʼmizinda ya Yuda anabweretsanso chakhumi cha ngʼombe zawo ndi nkhosa ndi chakhumi cha zinthu zoyera zoperekedwa kwa Yehova Mulungu wawo, ndipo anaziyika mʼmilumilu. 7Anayamba kuchita izi mwezi wachitatu ndipo anatsiriza mwezi wachisanu ndi chiwiri. 8Hezekiya ndi akuluakulu ake atabwera ndi kuona miluyo, anatamanda Yehova ndi kudalitsa anthu ake, Aisraeli.

9Hezekiya anafunsa ansembe ndi Alevi za miluyi; 10ndipo Azariya, mkulu wa ansembe, ochokera ku banja la Zadoki anayankha kuti, “Kuyambira pamene anthu anayamba kubweretsa zopereka zawo ku Nyumba ya Yehova ife takhala ndi zokwanira kudya ndi zina zambiri zosunga, chifukwa Yehova wadalitsa anthu ake, ndipo mulu umenewu ndiye zotsala.”

11Hezekiya analamula kuti akonze zipinda zosungiramo za mʼNyumba ya Yehova, ndipo izi zinachitika. 12Ndipo iwo mokhulupirika anabweretsa zopereka, chakhumi ndi mphatso zopatulika. Konaniya Mlevi ndiye amayangʼanira zinthu zimenezi ndipo mʼbale wake Simei ndiye anali wachiwiri wake. 13Yehieli, Azaziya, Nahati, Asaheli, Yerimoti, Yozabadi, Elieli, Isimakiya, Mahati ndi Benaya anali oyangʼanira motsogozedwa ndi Konaniya ndi Simei, mʼbale wake. Iwowa anasankhidwa ndi mfumu Hezekiya ndi Azariya mkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu.

14Kore mwana wa Imuna Mlevi, mlonda wa Chipata Chakummawa, amayangʼanira zopereka zaufulu kwa Mulungu, ankagawa zopereka za kwa Yehova ndiponso mphatso zopatulika. 15Edeni, Miniyamini, Yesuwa, Semaya, Amariya, Sekaniya amamuthandiza mokhulupirika mʼmizinda yonse a ansembe kugawira kwa ansembe anzawo monga mwa magulu awo, aakulu ndi aangʼono omwe.

16Kuwonjezera apa, amagawira ana aamuna a zaka zitatu kapena kupitirira amene mayina awo anali mʼmbiri ya mibado yawo, amene adzalowe mʼNyumba ya Yehova kugwira ntchito za tsiku ndi tsiku za magulu awo, molingana ndi udindo ndi magulu awo. 17Ndipo anazigawa kwa ansembe amene analembetsa mayina awo mwa mbiri ya mabanja awo, chimodzimodzinso Alevi amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirira molingana ndi udindo wawo ndi magulu awo. 18Iwo anaphatikizanso ana onse aangʼono, akazi ndiponso ana aamuna ndi ana aakazi a gulu lonse amene analembedwa mʼmbiri ya mibado yawo iyi, pakuti anakhulupirika pa kudzipatula okha.

19Kunena za ansembe, zidzukulu za Aaroni, amene amakhala mʼminda yozungulira mizinda yawo kapena mzinda wina uliwonse, anthu anasankhidwa mowatchula mayina kuti azipereka magawo kwa munthu wamwamuna aliyense pakati pawo ndiponso kwa onse amene analembedwa mʼmbiri ya mibado ya Alevi.

20Izi ndi zimene Hezekiya anachita mu Yuda monse, kuchita zabwino, zolungama ndi zokhulupirika pamaso pa Yehova Mulungu wake. 21Pa chilichonse chimene anachita pa ntchito ya Nyumba ya Mulungu ndi pa kumvera malangizo ndi malamulo, iye anafunafuna Mulungu wake ndipo anagwira ntchito ndi mtima wake wonse. Ndipo zinthu zimamuyendera bwino.