历代志上 4 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

历代志上 4:1-43

复述犹大的后裔

1犹大的儿子是法勒斯希斯仑迦米户珥朔巴2朔巴的儿子利亚雅雅哈雅哈亚户买拉哈。他们都属于琐拉人的宗族。 3以坦的儿子4:3 儿子”希伯来文是“父亲”。耶斯列伊施玛伊得巴,女儿名叫哈悉勒玻尼4基多的父亲是毗努伊勒户沙的父亲是以谢珥。这些人都是伯利恒的父亲、以法她的长子户珥的后代。 5提哥亚的父亲亚施户有两个妻子,一个名叫希拉,一个名叫拿拉6拿拉给他生了亚户撒希弗提米尼哈辖斯他利。这些都是拿拉的儿子。 7希拉的儿子是洗列琐辖伊提南8哥斯亚诺琐比巴,他也是哈伦的儿子亚哈黑宗族的祖先。 9雅比斯比他的众弟兄尊贵,他母亲给他取名叫雅比斯,意思是:“我生他时非常痛苦”。 10雅比斯以色列的上帝祷告说:“愿你赐福给我,扩大我的疆土,与我同在,使我远离患难和痛苦。”上帝答应了他的祈求。

11书哈的弟兄基绿米黑米黑伊施屯的父亲。 12伊施屯伯拉巴巴西亚提欣拿提欣拿珥拿辖的父亲。这些都是利迦人。 13基纳斯的儿子是俄陀聂西莱雅俄陀聂的儿子是哈塔悯挪太14悯挪太俄弗拉西莱雅革·夏纳欣人的祖先约押。他们都是工匠。 15耶孚尼的儿子是迦勒迦勒的儿子是以路以拉拿安以拉的儿子是基纳斯16耶哈利勒的儿子是西弗西法提利亚撒列17以斯拉的儿子是益帖米列以弗雅伦米列娶了法老的女儿比提雅为妻,她给米列生了米利暗沙迈以实提摩的父亲益巴18米列还娶了一个犹大人为妻,她生了基多的父亲雅列梭哥的父亲希伯撒挪亚的父亲耶古铁19荷第雅的妻子是拿含的妹妹,她的儿子们是迦米基伊拉玛迦以实提摩的父亲。 20示门的儿子是暗嫩林拿便·哈南提伦以示的儿子是梭黑便·梭黑

21犹大有个儿子名叫示拉示拉的后代是利迦的父亲玛利沙的父亲拉大、在亚实比织细麻布的各家族、 22约敬哥西巴人、约阿施以及统治摩押雅叔比利恒萨拉。这都是古代的记录。 23他们都是住在尼他英基低拉的陶匠,他们在那里为王效力。

西缅的后裔

24西缅的儿子是尼姆利雅悯雅立谢拉扫罗25扫罗的儿子是沙龙沙龙的儿子是米比衫米比衫的儿子是米施玛26米施玛的儿子是哈姆利哈姆利的儿子是撒刻撒刻的儿子是示每27示每有十六个儿子和六个女儿,他弟兄的儿女不多。他们整个宗族的人不如犹大宗族的人多。 28西缅人住在别示巴摩拉大哈萨·书亚29辟拉以森陀腊30彼土利何珥玛洗革拉31伯·玛嘉博哈萨·苏撒伯·比利沙拉音。在大卫做王以前,这些都是西缅人的城邑。 32他们还有五座城邑:以坦亚因临门陀健亚珊33以及这些城附近的村庄,远至巴力。这些都是他们的住处。他们有自己的家谱。

34西缅的后代还有米所巴雅米勒亚玛谢的儿子约沙35约珥约示比的儿子耶户约示比西莱雅的儿子,西莱雅亚薛的儿子。 36西缅的后代还有以利约乃雅哥巴约朔海亚帅雅亚底业耶西篾比拿雅37示非的儿子细撒示非亚龙的儿子,亚龙耶大雅的儿子,耶大雅申利的儿子,申利示玛雅的儿子。 38以上所提的这些人都是族长,各宗族都人丁兴旺。 39他们前往平原东边的基多谷寻找牧羊的草场, 40找到了一片肥沃的草场,又辽阔又安静。从前族人在那里居住。 41犹大希西迦执政期间,以上这些西缅人的族长来攻打族人的驻地和那里所有的米乌尼人,消灭了他们,占据了那里,一直住到今天,因为那里有可以牧羊的草场。 42有五百个西缅人在以示的儿子毗拉提尼利雅利法雅乌薛的带领下前往西珥山, 43铲除了残余的亚玛力人,从此定居在那里,直到今日。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 4:1-43

Mabanja Ena a Yuda

1Ana a Yuda anali awa:

Perezi, Hezironi, Karimi, Huri ndi Sobali.

2Reaya mwana wa Sobala anabereka Yahati, ndipo Yahati anabereka Ahumai ndi Lahadi. Awa anali mabanja a Azorati.

3Ana a Etamu anali awa:

Yezireeli, Isima ndi Idibasi. Dzina la mlongo wawo linali Hazeleliponi. 4Penueli anabereka Gedori, ndipo Ezeri anabereka Husa.

Awa anali ana a Huri, mwana wachisamba wa Efurata ndi abambo a Betelehemu.

5Asihuri abambo a Tekowa anali ndi akazi awiri, Hela ndi Naara.

6Naara anamuberekera Ahuzamu, Heferi, Temani ndi Haahasitari. Awa ndiwo anali ana a Naara.

7Ana a Hela:

Zereti, Zohari, Etinani, 8ndi Kozi, amene anali abambo ake a Anubi ndi Hazo-Beba ndi mabanja a Ahariheli mwana wa Harumi.

9Yabesi anali munthu wolemekezeka kwambiri kuposa abale ake. Amayi ake anamutcha Yabesi kutanthauza kuti, “Chifukwa ndinamubala ndi ululu wambiri.” 10Yabesi analira kwa Mulungu wa Israeli kuti, “Mundidalitse ndipo mukulitse dziko langa! Dzanja lanu likhale pa ine ndipo mundisunge kuti choyipa chisandigwere ndi kundisautsa.” Ndipo Mulungu anamupatsa chopempha chakecho.

11Kelubi, mʼbale wa Suha, anabereka Mehiri, amene anabereka Esitoni. 12Esitoni anabereka Beti-Rafa, Paseya ndi Tehina amene anabereka Iri Nahasi. Amenewa ndiwo anthu a ku Reka.

13Ana a Kenazi anali awa:

Otanieli ndi Seraya.

Ana a Otanieli anali awa:

Hatati ndi Meonotai. 14Meonotai anabereka Ofura.

Seraya anabereka Yowabu,

amene anabereka Ge-Harasimu. Anawatcha dzina ili chifukwa anthu ake anali amisiri.

15Ana a Kalebe mwana wa Yefune anali awa:

Iru, Ela ndi Naama.

Mwana wa Ela anali

Kenazi.

16Ana a Yehaleleli anali awa:

Zifi, Zifa, Tiriya ndi Asareli.

17Ana a Ezara anali awa:

Yeteri, Meredi, Eferi ndi Yaloni. Mmodzi mwa akazi a Meredi anabereka Miriamu, Samai ndi Isiba abambo ake a Esitemowa. 18(Mkazi wake wa Chiyuda anabereka Yaredi abambo ake a Gedori, Heberi abambo ake a Soko ndi Yekutieli abambo a Zanowa). Awa anali ana a mwana wamkazi wa Farao, Bitia, amene Meredi anakwatira.

19Ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wa Nahamu anali awa:

abambo ake a Keila wa ku Garimi ndi Esitemowa wa ku Maaka.

20Ana a Simeoni anali awa:

Amnoni, Rina, Beni-Hanani ndi Tiloni.

Ana a Isi anali awa:

Zoheti ndi Beni-Zoheti.

21Ana a Sela mwana wa Yuda anali awa:

Eri amene anabereka Leka, Laada amene anabereka Maresa ndi mabanja a anthu owomba nsalu zofewa ndi zosalala a ku Beti-Asibeya, 22Yokimu, anthu a ku Kozeba, ndiponso Yowasi ndi Sarafi, amene ankalamulira Mowabu ndi Yasibu-Lehemu. (Nkhani zimenezi ndi zakalekale). 23Iwo anali owumba mbiya amene ankakhala ku Netaimu ndi Gederi. Ankakhala kumeneko ndi kumatumikira mfumu.

Simeoni

24Ana a Simeoni anali awa:

Nemueli, Yamini, Yaribu, Zera ndi Sauli;

25Salumu anali mwana wa Sauli, Mibisamu anali mwana wa Salumu ndipo Misima anali mwana wa Mibisamu.

26Zidzukulu za Misima zinali izi:

Hamueli, Zakuri ndi Simei.

27Simei anali ndi ana aamuna 16 ndi ana aakazi 6, koma abale ake sanabereke ana ambiri; kotero banja lawo silinakule ngati anthu ena a ku Yuda. 28Iwo amakhala ku Beeriseba, Molada, Hazari-Suwali, 29Biliha, Ezemu, Toladi, 30Betueli, Horima, Zikilagi, 31Beti-Marikaboti, Hazari-Susimu, Beti-Biri ndi Saaraimu. Iyi inali mizinda yawo mpaka pa nthawi ya ulamuliro wa Davide. 32Midzi yowazungulira inali Etamu, Aini, Rimoni, Tokeni ndi Asani, midzi isanu 33ndi midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka ku Baala. Awa anali malo awo okhalapo. Ndipo anasunga mbiri ya makolo awo.

34Mesobabu, Yamuleki, Yosa mwana wa Amaziya, 35Yoweli, Yehu mwana wa Yosibiya, mwana wa Seraya, mwana wa Asieli, 36komanso Eliyoenai, Yaakoba, Yesohaya, Asaya, Adieli, Yesimieli, Benaya, 37ndiponso Ziza mwana wa Sifi, mwana wa Aloni, mwana wa Yedaya, mwana wa Simiri, mwana wa Semaya.

38Anthu amene atchulidwawa anali atsogoleri a mabanja awo. Mabanja awo anakula kwambiri 39ndipo anakafika ku malire a Gedori ku chigwa cha kummawa kufuna msipu wodyetsa ziweto zawo. 40Anapeza msipu wobiriwira ndi wabwino ndipo dziko linali lalikulu, la mtendere ndi bata. Kumeneko kunkakhala fuko la Hamu poyamba.

41Anthu amene mayina awowa alembedwa, anabwera pa nthawi ya Hezekiya mfumu ya Yuda. Iwo anathira nkhondo fuko la Hamu mʼmalo awo amene amakhala komanso Ameuni amene anali kumeneko ndipo anawononga onsewo kotero kuti mbiri yawo simvekanso mpaka lero lino. Kotero iwo anakhala mʼmalo awo chifukwa kunali msipu wa ziweto zawo. 42Ndipo anthu 500 a fuko la Simeoni, motsogozedwa ndi Pelatiya, Neariya, Refaya ndi Uzieli, ana a Isi, analanda dziko lamapiri la Seiri. 43Iwo anapha Aamaleki otsala amene anali atapulumuka ndipo akukhala kumeneko mpaka lero lino.