历代志上 18 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

历代志上 18:1-17

大卫的胜利

1后来,大卫打败并征服了非利士人,夺取了迦特及其周围的村庄。 2他又打败了摩押人,使他们称臣、进贡。 3琐巴哈大底谢出来要巩固他在幼发拉底河一带的权势,大卫打败了他,一直攻到哈马4俘获一千辆战车、七千骑兵、两万步兵,砍断拉战车的马匹的蹄筋,只留下够拉一百辆战车的马匹。 5大马士革亚兰人前来支援琐巴哈大底谢大卫杀了他们两万二千人, 6还派军驻守亚兰国的大马士革亚兰人臣服大卫,向他进贡。耶和华使大卫无往而不胜。 7大卫夺走哈大底谢侍从的金盾牌,带回耶路撒冷8又从哈大底谢统治的提巴两座城中夺走大量的铜。后来所罗门用这些铜制造铜海、铜柱及各种铜器。

9哈马陀乌听说大卫打败琐巴哈大底谢全军, 10就派儿子哈多兰带着许多金银铜器去朝见大卫王,向他请安,祝贺他打败了哈大底谢。因为陀乌常常和哈大底谢交战。 11于是,大卫把这些器皿和他从以东摩押亚扪非利士亚玛力各国夺来的金银都分别出来,奉献给耶和华。

12洗鲁雅的儿子亚比筛在盐谷击杀了一万八千名以东人。 13大卫以东驻兵,以东人都臣服他。耶和华使他无往而不胜。

14大卫在全以色列秉公行义,治理百姓。 15那时,洗鲁雅的儿子约押做元帅,亚希律的儿子约沙法做史官, 16亚希突的儿子撒督亚比亚他的儿子亚希米勒做祭司长,沙威沙做书记, 17耶何耶大的儿子比拿雅统管基利提人和比利提人。大卫王的众子都在他左右做首领。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 18:1-17

Nkhondo za Davide ndi Kupambana Kwake

1Patapita nthawi, Davide anagonjetsa Afilisti ndipo anakhala pansi pa ulamuliro wake. Iye analanda Gati ndi midzi yake yozungulira mʼmanja mwa Afilistiwo.

2Davide anagonjetsanso Amowabu, nakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho kwa iye.

3Komanso Davide anagonjetsa Hadadezeri mfumu ya Zoba, mpaka ku Hamati, pamene anapita kukakhazikitsa ulamuliro wake mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate. 4Davide analanda magaleta 1,000, anthu okwera magaleta 7,000 pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha.

5Aramu wa ku Damasiko atabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya ku Zoba, Davide anakantha asilikali 22,000. 6Iye anakhazikitsa maboma mu ufumu wa Aramu wa ku Damasiko, ndipo Aaramu anakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho. Yehova ankamupatsa chipambano Davide kulikonse kumene ankapita.

7Davide anatenga zishango zagolide zimene ankanyamula akuluakulu ankhondo a Hadadezeri ndi kubwera nazo ku Yerusalemu. 8Kuchokera ku Teba ndi Kuni, mizinda ya Hadadezeri, Davide anatengako mkuwa wambiri umene Solomoni anapangira chimbiya, zipilala ndi zida zosiyanasiyana zamkuwa.

9Tou, mfumu ya Hamati atamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezeri mfumu ya Zoba, 10anatumiza mwana wake Hadoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Hadoramu anabweretsa ziwiya zosiyanasiyana zagolide, zasiliva ndi zamkuwa.

11Mfumu Davide inapereka zinthu zimenezi kwa Yehova, monga anachitira ndi siliva ndi golide zochokera ku mayiko ena onse monga Edomu ndi Mowabu, Aamoni ndi Afilisti, ndi Aamaleki.

12Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu 18,000 mu Chigwa cha Mchere. 13Iye anayika maboma ku Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala pansi pa Davide. Yehova ankapambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.

Akuluakulu a Davide

14Davide analamulira dziko lonse la Israeli ndipo ankachita zonse mwachilungamo ndi molondola pamaso pa anthu ake onse. 15Yowabu, mwana wa Zeruya anali mkulu wa ankhondo; Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika; 16Zadoki, mwana wa Ahitubi ndi Ahimeleki mwana wa Abiatara anali ansembe; Savisa anali mlembi; 17Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti ndi Apeleti, ndipo ana a Davide anali alangizi a mfumu.