出埃及记 29 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

出埃及记 29:1-46

立祭司的条例

1“你要使亚伦父子们分别出来,做圣洁的祭司事奉我。你要选一头公牛犊和两只毫无残疾的公绵羊, 2用细面粉预备无酵饼、调上油的无酵饼和涂上油的无酵薄饼。 3所有的饼都要用一个篮子盛,连同公牛和绵羊一起带到会幕那里。 4你要先让亚伦父子们在会幕门前沐浴, 5然后给亚伦穿上内袍、以弗得和以弗得的外袍,戴上胸牌,束上精致的以弗得带子, 6戴上礼冠,把圣冠29:6 圣冠”应指28提到的金牌。系在礼冠上。 7之后,把膏油倒在他的头上,立他为祭司。 8接着轮到亚伦的儿子们,要给他们穿上内袍, 9为他们束上腰带,戴上帽子,他们就按永远的条例得到祭司的职分。你要这样把圣职授予他们。

10“要把公牛牵到会幕前面,亚伦父子们要把手按在公牛头上, 11在会幕门前,在耶和华面前宰牛。 12然后,把血带到祭坛那里,用手指把血涂在坛的四个角上,剩下的血倒在坛脚。 13再把遮盖内脏的脂肪、肝、两个肾脏和附在上面的脂肪都放在祭坛上烧掉。 14但牛皮、肉和粪要拿到营外焚烧。这是赎罪祭。

15“要把一只公绵羊牵来,亚伦父子们要把手按在羊头上, 16然后宰羊,把血洒在祭坛的四周。 17再把羊切成块状,用水洗净所有的内脏和腿,跟肉块和头放在一起。 18然后,把整只羊放在祭坛上焚烧,这是献给耶和华的燔祭,是蒙耶和华悦纳的馨香火祭。

19“你要把另一只公绵羊牵来,亚伦父子们要把手按在羊头上, 20然后宰羊,取一点血涂在亚伦和他儿子们的右耳垂、右手的大拇指和右脚的大脚趾上,余下的血就洒在祭坛的四周。 21再从祭坛上取一点血,与膏油一起洒在亚伦父子及其衣服上。这样,他们和他们的衣服就被分别出来,变得圣洁。

22“你要取出羊的脂肪、肥尾巴、遮盖内脏的脂肪、肝叶、两个肾脏和附在上面的脂肪以及右腿,因为这是授圣职时所献的羊。 23再从耶和华面前的篮子里取一个无酵饼、一个调油的无酵饼和一个薄饼。 24把这些祭物都放在亚伦和他儿子的手中,作为摇祭在耶和华面前摇一摇。 25然后,你要把这些祭物接过来,放在祭坛上焚烧献给耶和华,成为蒙耶和华悦纳的馨香火祭。 26你要拿起亚伦承受圣职时所献的那头公羊的胸肉,作为摇祭在耶和华面前摇一摇。之后,这份祭肉就归你。

27“要将属于亚伦父子们、授圣职时所献的摇祭胸肉和举祭腿肉分别出来,使之圣洁。 28这些祭物要从以色列人所献的平安祭中取出来,归给亚伦父子们,作为永远的定例。这是以色列人当向耶和华献的祭物。

29亚伦的圣衣要留给他的子孙,他们可以穿上这圣衣受膏,承受圣职。 30接替亚伦做祭司的那位后裔,每次进会幕的圣所供职时,都要一连七天穿着圣衣。

31“要在圣洁的地方煮授圣职时所用的公绵羊肉。 32亚伦父子们可以在会幕的门前吃这些祭肉和篮内的饼。 33他们要吃这些在授圣职时用来赎罪、使他们圣洁的祭物。但普通人不能吃,因为这些是圣物。 34若有授圣职时的肉或饼留到早上,就要烧掉,不可再吃,因为这些都是圣物。

35“你要照我的吩咐,为亚伦父子们举行授圣职礼,历时七天。 36每天要献一头公牛作赎罪祭洁净祭坛,然后用膏油抹祭坛,使祭坛圣洁。 37你们连续七天都要这样做,这样祭坛便完全圣洁,凡是碰到祭坛的都变得圣洁。

38“你们每天要献上两只一岁的羊羔作燔祭。 39一只在早晨献上,另一只在黄昏献上。 40要用一公斤细面粉调一升橄榄油做成素祭,与早晨献的羊羔一同献上,再献上一升酒作奠祭。 41另一只羊要在黄昏的时候献上,所献的素祭和奠祭要跟早晨的一样,作为蒙耶和华悦纳的馨香火祭。

42“你们世世代代要不断地在我面前献上燔祭,祭礼要在会幕门前举行,这会幕就是我跟你们会面和交谈的地方。 43我要在那里和以色列人相会,我的荣耀将使整座会幕圣洁。

44“我要使会幕和祭坛圣洁,也要使亚伦父子们圣洁,做祭司事奉我。 45我要住在以色列人中间,做他们的上帝。 46他们必知道我是他们的上帝耶和华。我带领他们离开埃及,就是为了要住在他们中间。我是他们的上帝耶和华。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 29:1-46

Mwambo Wopatula Ansembe

1“Pofuna kumupatula Aaroni ndi ana ake kuti akhale ansembe onditumikira Ine, uchite izi: Utenge ngʼombe yayingʼono yayimuna ndi nkhosa ziwiri zazimuna zopanda chilema. 2Utengenso buledi wopanda yisiti, makeke wopanda yisiti wopakidwa mafuta. Zonsezi uzipange ndi ufa wosalala wa tirigu. 3Uziyike mʼdengu ndipo ubwere nazo kwa Ine pamodzi ndi ngʼombe yayimuna ija ndi nkhosa ziwiri zazimuna zija. 4Kenaka ubwere naye Aaroni ndi ana ake pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo uwasambitse ndi madzi. 5Tenga zovala ndipo umuveke Aaroni mwinjiro, mkanjo wa efodi, efodiyo ndi chovala chapachifuwa. Umumange mʼchiwuno lamba wa efodi wolukidwa mwaluso uja. 6Umuveke nduwira kumutu, ndiponso uyike chizindikiro chopatulika chija pa nduwirayo. 7Utenge mafuta wodzozera ndipo uwatsanulire pamutu pake kumudzoza. 8Ubwere ndi ana ake aamuna ndipo uwavekenso minjiro 9ndi nduwira. Kenaka umange malamba Aaroniyo pamodzi ndi ana ake ndi kuwaveka nduwira. Motero unsembe udzakhala wawo malingana ndi lamulo ili losatha.

“Umu ndi mmene udzadzozere Aaroni ndi ana ake aamuna.

10“Ubwere ndi ngʼombe yayimuna pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo Aaroni ndi ana ake asanjike manja awo pamutu pake. 11Uphe ngʼombeyo pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. 12Utenge magazi ena angʼombeyo ndi kupaka ndi chala chako pa nyanga zaguwa lansembe ndipo magazi otsalawo uwakhutulire pa tsinde laguwalo. 13Kenaka utenge mafuta onse okuta matumbo, mafuta ophimba chiwindi ndiponso impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta ake. Zonsezi uzitenthe pa guwapo. 14Koma nyama yangʼombeyo, chikopa chake ndi matumbo ake uziwotche kunja kwa msasa. Iyi ndi nsembe yopepesera machimo.

15“Utenge nkhosa yayimuna imodzi ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna asanjike manja awo pamutu pake. 16Uyiphe ndipo utenge magazi ake ndi kuwaza mbali zonse zaguwalo. 17Uyidule nkhosayo nthulinthuli, kutsuka matumbo ake ndi miyendo yake. Ukatero, pamodzi ndi mutu wake, uziyike pamwamba pa nthulizo. 18Ndipo uwotche nkhosa yonseyo pa guwa lansembe. Iyi ndi nsembe yopsereza ya kwa Yehova. Ili ndi fungo lokoma, loperekedwa pa moto kwa Yehova.

19“Utenge nkhosa yayimuna ina ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna asanjike manja awo pamutu pake. 20Uyiphe ndipo utenge magazi ake ena ndi kupaka ndewere za makutu a kudzanja lamanja la Aaroni ndi ana ake aamuna. Upakenso pa zala zawo zazikulu za kudzanja lawo lamanja, ndi zala zazikulu za kuphazi lakudzanja lawo lamanja. Kenaka uwaze magazi otsalawo mbali zonse za guwalo. 21Ndipo utenge magazi ena amene ali pa guwa lansembe komanso pa mafuta ena odzozera ndipo uwawaze pa Aaroni ndi zovala zake ndi ana ake ndi zovala zawo. Ndiye kuti iyeyo ndi ana ake aamuna adzakhala opatulika pamodzi ndi zovala zawo.

22“Pa nkhosa yayimuna ija utengepo mafuta ake, mafuta a ku mchira wake, mafuta okuta matumbo, mafuta okuta chiwindi, impsyo zonse ziwiri ndi mafuta ake, ndiponso ntchafu yakumanja. Iyi ndi nkhosa ya mwambo wodzoza. 23Utengenso mʼdengu la buledi wopanda yisiti limene lili pamaso pa Yehova, buledi mmodzi, buledi wokhala ndi mafuta a olivi, ndi buledi wopyapyala mmodzi. 24Izi zonse uzipereke mʼmanja mwa Aaroni ndi ana ake, ndipo iwo aziweyule pamaso pa Yehova kuti zikhale nsembe yoweyula. 25Kenaka uzitenge mʼmanja mwawo ndipo uzipsereze pa guwa lansembe, pamwamba penipeni pamodzi ndi nsembe yopsereza kuti ipereke fungo lokoma kwa Yehova. Ichi ndiye chopereka chachakudya kwa Yehova. 26Kenaka utenge chidale cha nkhosa yayimuna imene inaperekedwa pamwambo wodzoza Aaroni, uchiweyule kuti chikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova ndipo chidzakhala gawo lako.

27“Uzipatule ziwalo zonse za nkhosa ya pa mwambo wodzoza Aaroni ndi ana ake. Chidale chimene unaweyula chija ndiponso ntchafu imene inaperekedwa ija. 28Nsembe izi ndi zimene Aisraeli azipereka kwa Aaroni ndi ana ake mwa zonse zimene azipereka nthawi zonse. Mwa zopereka za mtendere zimene ana a Aisraeli adzapereka kwa Yehova, zimenezi zikhale gawo lawo.

29“Zovala zopatulika za Aaroni zidzakhala za ana ake aamuna iye atafa kuti adzavale podzozedwa ndi polandira udindo wawo. 30Mwana amene adzalowa mʼmalo mwake monga wansembe pamene adzabwerera kudzalowa mu tenti ya msonkhano kudzatumikira ku malo wopatulika, adzavala zovala zimenezi masiku asanu ndi awiri.

31“Utenge nkhosa yayimuna ya pamwambo wodzoza ansembe ndipo uyiphike pamalo opatulika. 32Aaroni ndi ana ake adye nyama ya nkhosa yayimunayi pamodzi ndi buledi amene ali mʼdengu pa khomo la tenti ya msonkhano. 33Adye zonse zimene anazipereka kwa Yehova pamwambo wopepesera machimo powadzoza ndi kuwapatula. Munthu wamba asadye chifukwa ndi zopatulika. 34Ndipo ngati nyama ina ya nkhosa ya pamwambo wodzoza ansembe kapena buledi zatsala mpaka mmawa, muziwotche, asazidye chifukwa ndi zopatulika.

35“Uchitire Aaroni ndi ana ake aamuna zonse zimene ndakulamulazi. Uchite mwambo wowapatula kukhala ansembe masiku asanu ndi awiri. 36Tsiku lililonse uzipereka ngʼombe yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo kuti machimowo akhululukidwe. Ndiponso upatule guwalo popereka nsembe yopepesera ndi kulidzoza mafuta kuti likhale lopatulika. 37Pa masiku asanu ndi awiri uzipereka pa guwapo nsembe zoyeretsera guwalo, ukatero ndiye kuti uzilipatula. Ndipo guwa lansembelo lidzakhala loyera kwambiri, ndipo chilichonse chimene chidzakhudza guwalo chidzayeretsedwa.

38“Tsiku ndi tsiku pa guwa lansembe uzipereka izi: Ana ankhosa a chaka chimodzi awiri. 39Mmawa muzipereka mwana wankhosa mmodzi ndipo winayo madzulo. 40Pamodzi ndi mwana wankhosa woyambayo, muzipereka kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi lita imodzi ya mafuta a olivi pamodzi ndi lita imodzi ya vinyo ngati chopereka chachakumwa. 41Upereke mwana wankhosa winayo madzulo pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa kuti ikhale fungo lokoma la chopereka chachakudya kwa Yehova.

42“Zopereka zopsereza zimenezi ziziperekedwa nthawi zonse, pa mibado yonse. Muzidzazipereka pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. Pa guwa lansembe, Yehova adzakumana nanu ndi kuyankhula nanu. 43Pameneponso Ine ndidzakumana ndi Aisraeli, ndipo guwalo lidzakhala lopatulika chifukwa cha ulemerero wanga.

44“Tsono Ine ndidzapatula tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe. Ndidzapatulanso Aaroni pamodzi ndi ana ake kuti akhale ansembe anga onditumikira. 45Ndidzakhala pakati pa Aisraeli ndikukhala Mulungu wawo. 46Adzadziwa kuti ine ndine Mulungu wawo amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto kuti ndikhale pakati pawo. Ine ndine Yehova, Mulungu wawo.”