出埃及记 25 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

出埃及记 25:1-40

奉献的条例

1耶和华对摩西说: 2“你去告诉以色列百姓要献礼物给我。你们要为我收下所有甘愿献上的礼物。 3你们要收的礼物是金,银,铜, 4细麻线,山羊毛,蓝色、紫色和朱红色的线, 5染成红色的公羊皮,海狗皮,皂荚木, 6灯油,制作膏油和香的香料, 7用来镶嵌在以弗得和胸牌上的红玛瑙及其他宝石。 8要为我造一座圣所,我好住在他们中间。 9你们要照我的指示去造圣幕和里面各样的器具。

造约柜的条例

10“要用皂荚木做一个柜,长一点一米,宽六十六厘米,高六十六厘米, 11里外都要包上纯金,要用金子镶柜边。 12再造四个金环,安在柜的四个脚上,每边两个环。 13用皂荚木造两根横杠,外面要包上金, 14然后把横杠穿过柜旁的金环,便于抬柜。 15横杠穿进环以后,不可再抽出来。 16把我将要赐给你的两块约版放在柜里。 17要用纯金造一个施恩25:17 施恩”或译“赎罪”。座,长一点一米,宽六十六厘米。 18用纯金在施恩座的两端打造两个基路伯天使, 19跟施恩座连在一起,一端一个。 20两个基路伯天使要面对面朝向施恩座,向上展开翅膀,遮盖施恩座。 21要把施恩座放在柜上面,把我赐给你的约版放在柜里。 22我就在那里跟你会面,从两个基路伯天使中间的施恩座上,把要传给以色列百姓的一切诫命告诉你。

造供桌的条例

23“要用皂荚木造一张桌子,长八十八厘米,宽四十四厘米,高六十六厘米。 24整张桌子都要包上纯金,四周镶上金边, 25在桌子四周造一个八厘米宽的外框,上面也镶上金边。 26要造四个金环,安在桌子四角的桌腿上, 27金环要靠近外框,以便穿横杠抬桌子。 28两根横杠要用皂荚木制作,外面包金,用来抬桌子。 29你们要用纯金造桌子上的盘、碟和献酒用的杯和瓶。 30桌子上要一直摆着供饼,献在我面前。

造灯台的条例

31“要用纯金造一个灯台,灯台的灯座、灯柱、油杯、花瓣和花苞要用一块纯金打造。 32灯台的两边要各伸出三个分枝,共六个分枝。 33每个分枝要伸出三个杏花形状、有花瓣和花苞的杯,六个分枝都是这样。 34灯台上要有四个杏花形状、有花瓣和花苞的杯。 35灯台上每一对分枝的相连处要有花苞,三对都是这样。 36整座灯台,包括一切装饰,都要用一块纯金打造。 37此外,要为灯台造七个灯盏,放在灯台上面,照亮前面的地方。 38灯台用的灯剪和灯花盘都要用纯金造。 39造整座灯台和灯台的器具要用三十四公斤纯金。 40你务要照着在山上指示你的样式造这些器具。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 25:1-40

Zopereka Zomangira Chihema

1Yehova ananena kwa Mose kuti, 2“Uza Aisraeli kuti abweretse chopereka kwa Ine. Iwe ulandire choperekacho mʼmalo mwanga kuchokera kwa munthu amene akupereka mwakufuna kwake. 3Zopereka zimene ulandire kwa anthuwo ndi izi: Golide, siliva ndi mkuwa. 4Nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa, ubweya wambuzi; 5zikopa za nkhosa zazimuna za utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu; matabwa amtengo wa mkesha; 6mafuta anyale a olivi, zonunkhiritsa mafuta odzozera ndi zopangira lubani wonunkhira; 7miyala yokongola ya mtundu wa onikisi ndi ina yabwino yoyika pa efodi ndi pa chovala cha pachifuwa.

8“Iwo andipangire malo wopatulika, ndipo Ine ndidzakhala pakati pawo. 9Umange chihema ndiponso ziwiya zamʼkatimo monga momwe Ine ndidzakuonetsere.

Bokosi la Chipangano

10“Tsono apange bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha, ndipo kutalika kwake kukhale masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. 11Bokosilo ulikute ndi golide wabwino kwambiri, mʼkati mwake ndi kunja komwe, ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira bokosilo. 12Upange mphete zinayi zagolide ndipo uzimangirire ku miyendo yake inayi ya bokosilo, mbali ina ziwiri ndi mbali inanso ziwiri. 13Kenaka upange mizati yamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide. 14Ndipo ulowetse nsichizo mʼmphete zija za mbali zonse ziwiri za bokosilo kuti azinyamulira. 15Nsichizo zizikhala mʼmphete za bokosilo nthawi zonse, zisamachotsedwe. 16Ndipo udzayike mʼbokosilo miyala iwiri yolembedwapo malamulo imene Ine ndidzakupatse.

17“Upange chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69. 18Ndipo upange Akerubi awiri agolide osula ndi nyundo, uwayike mbali ziwiri za chivundikirocho, 19kerubi mmodzi mbali ina ndi wina mbali inayo. Akerubiwa uwapangire limodzi ndi chivundikirocho mʼmapeto mwa mbali ziwirizo. 20Mapiko a Akerubiwo adzatambasukire pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo kuti achiphimbe. Akerubiwo adzakhale choyangʼanana, aliyense kuyangʼana chivundikirocho. 21Uyike chivundikirocho pamwamba pa bokosi ndipo mʼbokosilo uyikemo miyala ya malamulo, imene ndidzakupatse. 22Ndizidzakumana nawe pamenepo, pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo, pakati pa Akerubi awiriwo, ndikumadzakupatsa malamulo onse okhudzana ndi Aisraeli.

Tebulo la Buledi Woperekedwa kwa Mulungu

23“Upange tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69. 24Tebulolo ulikute ndi golide wabwino kwambiri ndipo upange mkombero wagolide mʼmbali mwake. 25Upange feremu yozungulira tebulo, mulifupi mwake ngati chikhatho cha dzanja, ndipo uyike mkombero wagolide kuzungulira feremuyo. 26Upange mphete zinayi zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya zake zinayi, kumene kuli miyendo yake inayi. 27Mphetezo uziyike kufupi ndi feremu kuti azikolowekamo nsichi zonyamulira tebuloyo. 28Upange nsichi zamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide kuti azinyamulira tebulolo. 29Upange mbale ndi zipande zagolide wabwino, pamodzinso ndi mitsuko ndi mabeseni zogwiritsa ntchito popereka nsembe. 30Pa tebulopo uyikepo buledi woperekedwa kosalekeza, kuti azikhala pamaso panga nthawi zonse.

Choyikapo Nyale

31“Upange choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zikhale zosulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zipangidwire kumodzi. 32Mʼmbali mwake mukhale mphanda zisanu ndi imodzi, zitatu mbali iliyonse. 33Zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa zikhale pa mphanda yoyamba. Pa mphanda yachiwiri pakhalenso zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa. Ndipo mphanda zonse zisanu ndi imodzi zikhale chimodzimodzi ndipo zituluke mʼchoyikapo nyalecho. 34Pa choyikapo nyalecho pakhale zikho zinayi zopangidwa ngati maluwa amtowo ali ndi mphukira ndi maluwa. 35Mphukira yoyamba ikhale mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zoyamba za pa choyikapo nyale. Mphukira yachiwiri ikhale mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zinazo. Ndipo mphukira yachitatu ikhale mʼmunsi mwa nthambi zina ziwirinso. Zonse pamodzi zikhale nthambi zisanu ndi imodzi 36Mphukira ndi nthambi zonse zisulidwe kumodzi ndi choyikapo nyalecho ndi golide wabwino kwambiri.

37“Ndipo upange nyale zisanu ndi ziwiri ndi kuziyika pa choyikapo nyalecho kuti ziwunikire kutsogolo. 38Mbaniro ndi zowolera phulusa zikhale zagolide wabwino kwambiri. 39Choyikapo nyale ndi zipangizo zonse zipangidwe ndi golide wabwino kwambiri wolemera makilogalamu 34. 40Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.”