使徒行传 22 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

使徒行传 22:1-30

1“各位父老兄弟,请听我解释!” 2在场的人听见保罗讲的是希伯来话,更加安静了。保罗说: 3“我是犹太人,生于基利迦大数,在耶路撒冷长大,曾在迦玛列门下严格地按着我们祖先的律法接受教育,像你们今日一样热心事奉上帝。 4我曾经把信奉这道的男女信徒抓进监狱,迫害他们,置他们于死地。 5大祭司和众长老都可以为我作证。我还拿着他们写给大马士革犹太人的信去拘捕那里的信徒,押回耶路撒冷受刑。

6“当我快到大马士革的时候,大约中午时分,突然从天上有一道强光四面照着我。 7我就扑倒在地,听见有声音对我说,‘扫罗扫罗!你为什么迫害我?’ 8我回答说,‘主啊,你是谁?’他说,‘我就是你迫害的拿撒勒人耶稣!’ 9我的同伴虽然也看见那道强光,却听不懂那位说话者的声音。 10接着我又问,‘主啊!我该怎么办?’主说,‘起来,到大马士革去,那里会有人将指派给你的事告诉你。’

11“那道耀眼的光照得我双眼失明,于是同行的人拉着我的手,带我进了大马士革12那里有一个严守律法的虔诚人名叫亚拿尼亚,深受当地所有犹太人的尊敬。 13他来探望我,站在我身边说,‘扫罗弟兄,重见光明吧!’就在那一刻,我抬头看见了他。 14他又说,‘我们祖先的上帝拣选了你,要你明白祂的旨意,又让你亲自看见那位公义者、听到祂的声音。 15因为你将做祂的见证人,把所见所闻告诉万民。 16现在你还等什么呢?起来求告祂的名,接受洗礼,洗净你的罪。’

17“后来,我回到耶路撒冷,在圣殿里祷告的时候,进入异象, 18看见主对我说,‘赶快离开耶路撒冷,因为这里的人不会接受你为我做的见证。’ 19我说,‘主啊!他们都知道我从前搜遍各会堂,逮捕、毒打信你的人。 20当你的见证人司提凡为你流血殉道时,我自己也站在旁边赞同杀他的人,还替他们保管衣服。’ 21主却对我说,‘去吧!我要差遣你到遥远的外族人那里。’”

因罗马公民身份而免刑

22众人一听到这里,就高喊:“从世上除掉这样的人!他不配活着!” 23百姓咆哮着脱掉外衣,扬起尘土。 24千夫长下令把保罗押回营房,预备鞭打拷问他,要查出众人向他咆哮的缘由。 25他们把保罗绑起来正要鞭打,保罗问旁边的百夫长:“未经定罪就拷打罗马公民合法吗?”

26百夫长一听,立刻去禀告千夫长说:“你看该怎么办?这人是罗马公民。”

27千夫长就来问保罗:“告诉我,你是罗马公民吗?”

保罗说:“是的。”

28千夫长说:“我花了很多钱才当上罗马公民!”

保罗说:“我生来就是。”

29那些准备拷问保罗的士兵立刻退下了。千夫长也害怕起来,因为发现保罗罗马公民,他却下令捆绑了保罗

保罗在公会申辩

30第二天,千夫长想知道保罗犹太人指控的真相,就为保罗松了绑,并招聚了祭司长和全公会的人,然后将保罗带来,让他站在众人面前。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 22:1-30

1Iye anati, “Inu abale anga ndi makolo anga, tamvani mawu akudziteteza kwanga.” 2Atamva iye akuyankhula Chihebri, anakhala chete.

Kenaka Paulo anati, 3“Ine ndine Myuda, wobadwira ku Tarisisi wa ku Kilikiya, koma ndinaleredwa mu mzinda muno, ndinaphunzitsidwa mwatsatanetsatane kusunga malamulo a makolo athu ndi Gamalieli ndipo ndinali wodzipereka pa za Mulungu monga mmene inu mulili lero. 4Ine ndinkazunza anthu otsatira Njirayi mpaka kuwapha. Ndinkagwira amuna ndi amayi ndi kuwayika mʼndende. 5Mkulu wa ansembe ndiponso akuluakulu a Ayuda angathe kundichitira umboni. Iwowa anandipatsa makalata opita nawo kwa abale awo ku Damasiko. Ndipo ndinapita kumeneko kuti ndikawagwire anthu amenewa ndi kubwera nawo ku Yerusalemu kuti adzalangidwe.

6“Nthawi ya masana, nditayandikira ku Damasiko, mwadzidzidzi kuwala kwakukulu kochokera kumwamba kunandizungulira. 7Ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akuti, ‘Saulo! Saulo! Ukundizunziranji?’ ”

8Ine ndinafunsa kuti, “Ndinu ndani Ambuye?”

Iye anayankha kuti, “Ndine Yesu wa ku Nazareti, amene iwe ukumuzunza.” 9Anzanga a paulendo anaona kuwalako, koma sanamve mawuwo, a Iye amene amayankhula nane.

10Ine ndinafunsa kuti, “Kodi ndichite chiyani Ambuye?”

Ambuye anati, “Imirira ndipo pita ku Damasiko. Kumeneko adzakuwuza zonse zimene ukuyenera kuchita.” 11Anzanga anandigwira dzanja kupita nane ku Damasiko, popeza kuwala kunja kunandichititsa khungu.

12“Munthu wina dzina lake Hananiya anabwera kudzandiona. Iyeyu anali munthu woopa Mulungu ndi wosunga Malamulo. Ayuda onse okhala kumeneko amamupatsa ulemu waukulu. 13Iye anayimirira pafupi nane nati, ‘Mʼbale Saulo, penyanso!’ Ndipo nthawi yomweyo ndinapenya ndikumuona iyeyo.

14“Ndipo iye anati, ‘Mulungu wa makolo athu wakusankha iwe kuti udziwe chifuniro chake ndi kuona Wolungamayo ndi kumva mawu ochokera pakamwa pake. 15Iwe udzakhala mboni yake kwa anthu onse pa zimene waziona ndi kuzimva. 16Ndipo tsopano ukudikira chiyani? Dzuka ndi kutama dzina la Ambuye mopemba, ubatizidwe ndi kuchotsa machimo ako.’

17“Nditabwerera ku Yerusalemu, ndikupemphera mʼNyumba ya Mulungu, ndinachita ngati ndakomoka. 18Ndinaona Ambuye akundiwuza kuti, ‘Fulumira! Tuluka mu Yerusalemu msangamsanga, chifukwa anthuwa sadzavomereza umboni wako wonena za Ine.’ ”

19Ine ndinayankha Ambuye kuti, “Anthu awa akudziwa kuti ine ndinkapita ku sunagoge iliyonse ndipo ndinkawaponya mʼndende ndi kuwakwapula amene ankakhulupirira inu. 20Ndipo pamene ankapha Stefano, ine ndinali pomwepo kuvomereza ndi kusunga zovala za amene amamupha.”

21Pamenepo Ambuye anandiwuza kuti, “Nyamuka; Ine ndidzakutuma kutali kwa anthu a mitundu ina.”

Paulo Nzika ya Chiroma

22Gulu la anthu linamvetsera mawu a Paulo mpaka pamene ananena izi, kenaka anakweza mawu awo nafuwula kuti, “Ameneyo aphedwe basi! Ngosayenera kukhala moyo!”

23Akufuwula ndi kuponya zovala zawo ndi kuwaza fumbi kumwamba, 24mkulu wa asilikali analamulira kuti amutenge Paulo kupita naye ku malo a asilikali. Iye analamula kuti Paulo akwapulidwe kwambiri ndi kumufunsa kuti apeze chimene anthu ankafuwulira chotere. 25Atamumanga kuti amukwapule, Paulo anati kwa msilikali wolamulira asilikali 100 amene anayima pamenepo, “Kodi malamulo amalola kukwapula nzika ya Chiroma imene sinapezedwe yolakwa?”

26Wolamulira asilikali 100 uja atamva zimenezi, anapita kwa mkulu wa asilikali ndi kumufotokozera. Iye anafunsa kuti, “Kodi mukuchita chiyani ndi munthuyu amene ndi nzika ya Chiroma?”

27Mkulu wa asilikali uja anapita kwa Paulo ndipo anamufunsa kuti, “Tandiwuze, kodi ndiwe nzika ya Chiroma?”

Paulo anayankha kuti, “Inde.”

28Kenaka mkulu wa asilikaliyo anati, “Ine ndinapereka ndalama zambiri kuti ndikhale nzika.”

Paulo anayankha kuti, “Koma ine ndinabadwa nzika.”

29Iwo amene anati amufunse analeka nthawi yomweyo. Mkulu wa asilikali uja anachita mantha atazindikira kuti wamanga Paulo amene ndi nzika ya Chiroma.

Paulo ku Bwalo Lalikulu la Ayuda

30Mmawa mwake, mkulu wa asilikali pofuna kupeza chifukwa chenicheni chimene Ayuda amamunenera Paulo, anamumasula ndipo analamula kuti akulu a ansembe ndi onse akuluakulu a Bwalo Lalikulu asonkhane. Ndipo iye anabweretsa Paulo namuyimiritsa patsogolo pawo.