传道书 2 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

传道书 2:1-26

1我心里想:“来吧,不如尽情享乐,好好享受!”唉!结果这也是虚空。 2我说:“欢笑只不过是一阵狂妄,享乐又有什么用!” 3于是,我决意用酒使自己快乐,在体验愚昧的同时仍然保持理智,直到我明白在短暂的人生岁月中做何事才有益。 4我大动工程,为自己建造房屋,栽种葡萄园, 5开垦花圃园囿,种植各种果树, 6开凿池塘,浇灌茂林。 7我买了仆婢,又有生在家中的仆婢,拥有的牛羊远超过有史以来耶路撒冷的任何人。 8我为自己积聚金银,搜罗列王和各省的奇珍异宝,得到男女歌优及许多妃嫔——都是世人所想望的。 9这样,我便财势日增,享誉盛名,超过耶路撒冷历来所有的人。然而,我仍然保持智慧。 10凡我眼睛爱看的、心里渴慕的,我都随心所欲,尽情享受。我的心从劳碌中得到欢乐,这是我劳碌所得的回报。 11然而,当我回顾双手辛勤经营的一切成就时,唉,却发现都是虚空,都是捕风;日光之下的一切都毫无益处。 12于是,我转念思考什么是智慧、狂妄和愚昧。其实以后接替君王的人除了重演历史之外,还能做什么呢? 13我领悟到智慧胜过愚昧,如同光明胜过黑暗。 14智者高瞻远瞩,愚人却在黑暗中摸索。但我知道两者终必有同样的命运。 15于是,我想:“既然愚人的命运也将是我的命运,我有智慧又怎么样呢?我只能说,‘这也是虚空。’” 16因为智者和愚人一样,不过被人记得一时,日后都会被遗忘。两者都难逃死亡。 17所以,我憎恶生命,因为在日光之下所做的一切都令我愁烦。唉!这一切都是虚空,都是捕风。 18我憎恶自己在日光之下劳碌得来的一切,因为这些必留给后人。 19谁知道那人是智者还是愚人呢?然而,他却要接管我在日光之下用智慧辛勤经营的产业。这也是虚空。 20因此,我对自己在日光之下一切的劳碌感到绝望。 21一个人用智慧、知识和技能所得来的一切,却要留给不劳而获的人享用,这也是虚空,是极大的不幸! 22世人在日光之下劳心劳力,究竟得到什么呢? 23他们一生充满痛苦,劳碌中尽是愁烦,即使夜间心里也不安宁。这也是虚空。 24对人而言,没有什么比吃喝并享受劳碌之乐更好,我看这也是出自上帝的手。 25离了上帝,谁还能吃喝享受呢? 26上帝把智慧、知识和喜乐赐给祂喜悦的人,却让罪人忙于积攒财富,然后把他们的财富赐给祂喜悦的人。这也是虚空,也是捕风。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mlaliki 2:1-26

Zosangalatsa Nʼzopandapake

1Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Tsopano ndiyese zosangalatsa kuti ndipeze zomwe ndi zabwino.” Koma izi zinaonekanso kuti ndi zopandapake. 2“Kuseka,” ndinati, “imeneyo ndi misala. Ndipo kodi chisangalalo chimabweretsa phindu lanji?” 3Ndinayesa kudzisangalatsa ndi vinyo, koma umenewu unali uchitsiru, pamenepo nʼkuti maganizo anga akutsogozedwa ndi nzeru. Ine ndinkati mwina kapena njira yotero nʼkukhala yopambana, imene anthu amatsata pofuna kusangalala pa masiku owerengeka a moyo wawo.

4Ndinagwira ntchito zikuluzikulu: Ndinadzimangira nyumba ndi kuwoka mipesa. 5Ndinalima madimba ndi minda yamitengo; ndipo ndinadzalamo mitengo ya zipatso za mitundu yonse. 6Ndinakumba mayiwe osungiramo madzi woti ndizithirira minda ya mitengo yodzalidwa ija. 7Ndinagula akapolo aamuna ndi akapolo aakazi, ndiponso ndinali ndi akapolo ena omwe anabadwira mʼnyumba mwanga. Ndinalinso ndi ngʼombe ndi nkhosa zambiri kupambana aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. 8Ndinadzikundikira siliva ndi golide, ndiponso chuma chochokera kwa mafumu ndi madera awo. Ndinali ndi amuna ndi akazi oyimba ndiponso azikazi; zinthu zokondweretsa mtima wa munthu. 9Ndinali munthu wotchuka kupambana wina aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. Mu zonsezi nzeru zanga zinali nane.

10Sindinadzimane chilichonse chimene maso anga anachifuna;

mtima wanga sindinawumane zokondweretsa.

Mtima wanga unakondwera ndi ntchito yanga yonse,

ndipo iyi ndiyo inali mphotho ya ntchito zanga zonse zolemetsa.

11Koma pamene ndinayamba kuyangʼanayangʼana zonse zimene ndinachita ndi manja anga,

ndi zimene ndinazivutikira kuti ndizipeze,

zonsezi zinali zopandapake; kungodzivuta chabe,

palibe chomwe ndinapindula pansi pano.

Nzeru ndi Uchitsiru Nʼzopandapake

12Kenaka maganizo anga anayamba kulingalira zakuti nzeru nʼchiyani,

komanso kuti misala ndi uchitsiru nʼchiyani.

Kodi munthu wodzalowa ufumu tsopanoyo angachite chiyani

choposa chimene chinachitidwa kale?

13Ndinaona kuti nzeru ndi yopambana uchitsiru,

monga momwe kuwala kumapambanira mdima.

14Munthu wanzeru amayenda maso ali patsogolo,

pamene chitsiru chimayenda mʼchimbulimbuli;

koma ndinazindikira kuti chomwe

chimawachitikira onsewo ndi chimodzi.

15Pamenepo ndinalingalira mu mtima mwanga,

“Zochitikira chitsiru zidzandichitikiranso ine.

Nanga tsono phindu langa nʼchiyani pakukhala wanzeru?”

Ndinati mu mtima mwanga,

“Ichinso ndi chopandapake.”

16Pakuti munthu wanzeru, pamodzinso ndi chitsiru sadzakumbukiridwa nthawi yayitali;

mʼmasiku amʼtsogolo awiriwo adzayiwalika.

Mmene chimafera chitsiru ndi mmenenso amafera wanzeru!

Kugwira Ntchito Nʼkopandapake

17Kotero ndinadana nawo moyo chifukwa ntchito zimene zimagwiridwa pansi pano ndi zosautsa kwa ine. Ntchito zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe. 18Ine ndinadana nazo ntchito zonse zimene ndinazigwira pansi pano, chifukwa ndinayenera kudzazisiyira wina amene adzalowa mʼmalo mwanga. 19Ndipo ndani amadziwa kuti munthu ameneyo adzakhala wanzeru kapena chitsiru? Komabe munthuyo adzakhala wolamulira zonse zimene ndinazichita pansi pano mwa nzeru zanga. Izinso ndi zopandapake. 20Motero ndinayamba kutaya mtima chifukwa cha ntchito zonse zimene ndinazivutikira pansi pano. 21Pakuti munthu atha kugwira ntchito yake mwanzeru, chidziwitso ndi luntha, ndipo kenaka nʼkusiyira wina amene sanakhetserepo thukuta. Izinso ndi zopandapake ndiponso tsoka lalikulu. 22Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhawa zimene amazichita pansi pano? 23Masiku ake onse amakhala achisoni, ntchito yake imakhala yovuta; ngakhale usiku womwe, mtima wake supumula. Izinso ndi zopandapake.

24Kwa munthu palibe chabwino china kuposa kudya, kumwa ndi kukondwerera ntchito zake. Izinso ndaona kuti ndi zochokera kwa Mulungu, 25pakuti popanda Iye, ndani angadye ndi kupeza chisangalalo? 26Munthu amene amakondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamusandutsa wanzeru, wozindikira ndi wachisangalalo, koma wochimwa, Mulungu amamupatsa ntchito yosonkhanitsa ndi kusunga chuma kuti adzachipereke kwa amene Mulunguyo amakondwera naye. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.