以西结书 40 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以西结书 40:1-49

新圣殿的异象

1在我们被掳的第二十五年,就是耶路撒冷沦陷的第十四年一月十日,耶和华的灵降在我身上。 2在异象中上帝把我带到以色列的一座高山上,山的南面仿佛有一座城。 3祂把我带到那里。城的入口站着一个面色如铜的人,手中拿着一条麻绳和一根量竿。 4那人对我说:“人子啊,你要留心用眼看,专心用耳听,注意我指示你的一切,因为我带你来这里正是为了要指示你。你要把所见到的一切告诉以色列人。”

外院的门

5我看见殿的四周有墙,那人拿了一根三米长的量竿测量这墙,量出墙厚一竿,高一竿。

6然后,他带我到殿的东门,走上石阶,来到门口。他量了门洞,宽一竿。 7门内有守卫室,长度和宽度都是一竿。室与室之间相距二点二米,通往圣殿的内门洞宽一竿, 8通往圣殿的门廊宽度也是一竿, 9连墙柱在内共四点二米宽,墙柱宽一点零五米。 10东门内共有六间守卫室,每边三间,大小面积都是一样,两边的墙尺寸也相同。 11通道尽头有一道门廊,宽五米,长六点五米。 12两边守卫室前面的矮墙高五十厘米,守卫室都是三米宽的正方形。 13他又量门廊的宽度,即这边守卫室的屋顶到对面守卫室的屋顶,是十二点五米。 14他从门口的墙量到外院的墙柱,是三十米。 15由门口到通道尽头的内廊共二十五米, 16守卫室、墙柱上和门廊周围都有格子窗,墙柱上刻着棕树。

外院

17他带我到外院,外院靠墙的四周是铺石地,上面共有三十间厢房。 18铺石地在门口的两边,比内院低,宽度与入口的长度一样。 19他从外院的内门口量到内院的门口,距离是五十米。

北门

20他又量了外院的北门, 21通道两边各有三间守卫室,墙和廊子长度和宽度跟东门一样,分别是二十五米和十二点五米。 22它的窗户、门廊、墙柱上雕刻的棕树都和东门的尺寸相同。登上七级石阶便到达门口,通道的尽头是门廊。 23内院的北门与外院的北门相对,正如它的东门和外院的东门相对,门与门之间的距离是五十米。

南门

24他又带我到南门,量了墙柱和门廊,都与其他门的尺寸相同, 25通道与门廊四周的窗户也和其他的门一样,通道长二十五米,宽十二点五米。 26登上七级石阶便到门廊,两边的墙柱也同样刻着棕树。 27内院也有南门,与外院南门之间的距离是五十米。

内院的门

28他带我从南门走进内院,量了南门,跟其他门的尺寸一样。 29守卫室、墙柱和门廊都和其他的尺寸一样,通道与门廊四周有窗户,通道长二十五米,宽十二点五米。 30内院周围的门廊都是长十二点五米,宽二点五米。 31这些门廊靠外院,两边的墙柱刻着棕树,上去的石阶共有八级。

32他又带我从东门进入内院,量了东门,跟其他门的尺寸一样, 33守卫室、墙柱、门廊和其他门的尺寸一样,通道与门廊的四周也有窗户,通道长二十五米,宽十二点五米。 34门廊靠外院,两边的墙柱刻着棕树,那里的石阶共有八级。

35他又带我到北门,量了北门,跟其他门的尺寸一样。 36守卫室、墙柱、门廊和其他门的尺寸一样,通道长二十五米,宽十二点五米,四周有窗户。 37门廊靠外院,两边的墙柱刻着棕树,那里的石阶共有八级。

厢房

38门口的墙柱旁边有一个房间,供祭司洗燔祭牲。 39门廊两边各有两张用来屠宰燔祭牲、赎罪祭牲和赎过祭牲的桌子。 40内院北门的两边各有两张桌子, 41即里外各有四张桌子,共八张,供祭司屠宰祭牲之用。 42另有四张用石头凿成的桌子用来预备燔祭牲,屠宰燔祭牲及其他祭牲的器具都放在桌上。桌子长宽各七十五厘米,高五十厘米。 43廊内四周挂着七点五厘米长的双钩。桌上放着祭肉。

44在内院有歌乐手用的厢房,一间向南,在北门旁,一间向北,在南门旁。 45他对我说:“向南的厢房是给殿内供职的祭司用的, 46向北的厢房是给坛前供职的祭司用的。他们都是撒督的子孙,利未的后裔,在耶和华面前专职事奉。” 47他量了殿前的院子,是五十米宽的正方形,祭坛在殿的前面。

圣殿

48他带我来到殿前通往圣所的门廊,量了两旁的墙柱,各二点五米宽,门两边的墙一点五米厚, 49门廊长十米,宽四点九米。上门廊靠近墙柱的石级两旁各有一根柱子。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 40:1-49

Malo Atsopano a Nyumba ya Mulungu

1Kumayambiriro a chaka cha 25, cha ukapolo wathu, tsiku la khumi lamwezi, patapita zaka khumi ndi zinayi mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa, pa tsiku lomwelo dzanja la Yehova linali pa ine ndipo Iye anapita nane ku Yerusalemu. 2Mʼmasomphenyawo Yehova ananditenga ndi kupita nane ku dziko la Israeli ndipo anandiyika pa phiri lalitali kwambiri, moti ndinaona ngati mzinda. 3Atandifikitsa kumeneko ndinaona munthu wonyezimira ngati mkuwa. Iye anali atayima pa chipata ndipo mʼdzanja lake munali chingwe cha nsalu yabafuta ndi ndodo yoyezera. 4Munthuyo anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, penyetsetsa ndipo umvetse bwinobwino. Uyikepo mtima wako pa zonse zimene ndikukuonetsa pakuti anakubweretsa kuno kuti uwone zimenezi. Tsono ukawawuze Aisraeli zonse zimene uzione.”

Chipata Chakummawa

5Ine ndinaona khoma litazungulira mbali zonse za Nyumba ya Mulungu. Mʼdzanja la munthuyo munali bango lopimira limene kutalika kwake kunali kwa mamita atatu. Atayeza chipupacho anapeza kuti kuchindikira kwake kunali mamita atatu, ndiponso kutalika kwake kunalinso mamita atatu.

6Anapita ku chipata chakummawa. Anakwera pa makwerero a nyumbayo, nayeza chiwundo choyamba cha chipatacho; kutalika kwake kunali mamita atatu. 7Kudutsa chiwundo choyambachi, panali zipinda za alonda zisanu ndi chimodzi, zitatu kudzanja lamanja, zitatu kudzanja lamanzere. Chilichonse chinali cha mamita atatu mulitali mwake, chimodzimodzinso mulifupi mwake. Mipata ya pakati pa zipindazo inali ya mamita awiri ndi theka. Ndipo chiwundo cha pa chipata pafupi ndi khonde lapachipata, chinali mamita atatu.

8Ndipo iye anayeza khonde la chipata ndipo chinali cha mamita atatu. 9Anayeza khonde ndipo linali mamita anayi. Mphuthu zake zinali mita imodzi kuchindikira kwake. Khonde lamʼkati lapachipata linali kumapeto kwenikweni pafupi ndi Nyumba ya Mulungu.

10Mʼkati mwa chipata chakummawa munali zipinda za alonda zitatu mbali iliyonse. Zitatu zonsezo zinali zofanana, ndipo khonde la pakati pa zipindazo linali lofanana. 11Kenaka anayeza chipata cholowera; mulifupi mwake munali mamita asanu ndipo mulitali mwake munali mamita asanu ndi limodzi ndi theka. 12Kutsogolo kwa chipinda chilichonse cha alonda kunali khoma lalifupi lotalika theka la mita, ndipo mbali iliyonse ya zipinda za alondazo inali yotalika mamita atatu. 13Ndipo anayeza kutalika kwa mulifupi mwa chipata cholowera, kuchokera ku khoma lakumbuyo la chipinda chimodzi mpaka ku khoma la chipinda china; kuchokera ku chitseko mpaka ku chitseko china. Kutalika kwake kunali mamita khumi ndi awiri ndi theka. 14Anayezanso khonde lamʼkati ndipo linali la mamita makumi atatu. Ndipo mozungulira khondelo munali bwalo. Muyesowu sukuphatikiza khonde loyangʼanana ndi bwalo. 15Kuchokera pa chipata cholowera mpaka ku mapeto a khonde la chipata, kutalika kwake kunali mamita 27. 16Makoma a zipinda ndiponso makoma a pakati pa zipindazo anali ndi mazenera. Khonde lamʼkati linalinso ndi mazenera mʼkati mwake. Pa makoma onsewo anajambulapo zithunzi za kanjedza.

Bwalo la Kunja

17Kenaka munthuyo anandilowetsa mʼbwalo lakunja, ndipo ndinaona zipinda zina ndi msewu wa miyala wozungulira bwalo lonse. Zipinda zonse zinali makumi atatu ndipo zinkayangʼana msewuwo. 18Utali wa mulifupi mwa msewuwo unkayenda mamita 27 kufanana ndi utali wa chipata cholowera. Uwu unali msewu wa mʼmunsi. 19Tsono, anayeza kutalika kwa bwalo kuyambira chipata cholowera choyamba mpaka polowera pa chipata chakunja cha bwalo la mʼkati. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.

Chipata Chakumpoto

20Kenaka munthuyo anayeza mulitali ndi mulifupi mwa chipata chimene chimayangʼana kumpoto, chotulukira kunja. 21Zipinda za alonda zimene zinalipo zitatu mbali iliyonse, makoma ake ndi khonde zinali ndi muyeso wofanana ndi wachipata choyamba chija. Kutalika kwake kunali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13. 22Mipata yake, khonde lake ndi zojambula za kanjedza zinali ndi miyeso yofanana ndi za chipata chakummawa. Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi awiri ndipo kotsirizira kwa chipatacho kunali khonde. 23Panalinso chipata cholowera ku bwalo lamʼkati chofanana ndi chakummawa chimene chimayangʼanana ndi chipata chakumpoto, chofanana ndi cha mbali ya kummawa. Anachiyeza kuchokera ku chipata china mpaka ku chipata china. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.

Chipata Chakummwera

24Ndipo munthuyo anapita nane ku mbali yakummwera ndipo ndinaona chipata chakummwera. Iye anayeza mphuthu zake ndi khonde ndipo zinali ndi miyeso yofanana ndi ya zina zija. 25Mʼzipinda za chipata cholowera chimenechi ndi mʼkhonde lake munali mipata yofanana ndi ya mʼzipinda zina. Mulitali mwake munali mamita 27, mulifupi mwake munali mamita 13. 26Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi awiri ndi khonde kotsirizira kwake. Chipindacho chinali ndi zojambula za kanjedza ku mbali zonse za makoma. 27Bwalo lamʼkati linalinso ndi chipata kummwera. Munthuyo analiyeza kuchokera ku chipata chimenechi mpaka ku chipata chakunja. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.

Zipata Zolowera ku Bwalo la Mʼkati

28Ndipo munthu uja anandilowetsa mʼbwalo lamʼkati kudzera ku chipata chakummwera. Anayeza chipatachi ndipo chinali chofanana ndi zinzake zija. 29Zipinda zake za alonda, makoma ake ndi khonde lake zinali zofanana ndi zina zija. Chipata cholowera ndi khonde lake zinali ndi mipata mʼmbali zonse. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi munali mamita 13. 30(Khonde lililonse la makonde atatu a zipata zolowera bwalo lamʼkati aja linali la mamita ozungulira mʼbwalo lamʼkati anali mamita 13 mulitali mwake, mamita awiri ndi theka mulifupi mwake). 31Khonde lake linayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu pake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.

32Kenaka munthuyo anapita nane ku bwalo la mʼkati mbali ya kummawa, ndipo anayeza chipata cholowera; chinali chofanana ndi zinzake zina zija. 33Zipinda zake za alonda, makoma ake ndi khonde lake zinali zofanana ndi zina zija. Chipata cholowera ndi khonde lake chinali ndi mipata mʼmbali zonse. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13. 34Khonde lake linayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu pake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.

35Kenaka anapita nane ku chipata chakumpoto ndipo anachiyeza. Chinali chofanana ndi zina zija. 36Zipinda zake za alonda, makoma ake ndiponso khonde lake zinali zofanana ndi zina zija, ndipo chinalinso ndi mipata mbali zonse ziwiri. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13. 37Khonde lake limayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu zake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.

Zipinda Zokonzeramo Nsembe

38Panali chipinda ndipo khomo lake linali pafupi ndi khonde la chipata cholowera chamʼkati. Mʼchipinda mʼmenemo ankatsukira nyama ya nsembe yopsereza. 39Pa khonde la chipatacho panali matebulo awiri, lina kuno lina uko. Ankapherapo nsembe zopsereza, nsembe zopepesera machimo ndi nsembe zopepesera kupalamula. 40Panali matebulo anayi, awiri a iwo anali kunja kwa khoma la khonde pafupi ndi makwerero olowera pa chipata chakumpoto ndi awiri enawo anali mbali inayo ya makwerero. 41Choncho ku mbali imodzi ya chipata kunali matebulo anayi, ndiponso ku mbali inayo kunali matebulo anayi. Onse pamodzi anali matebulo asanu ndi atatu. Pa matebulopo ankapherapo nyama za nsembe zopsereza. 42Matebulo anayiwa anali a miyala yosema. Lililonse mulitali mwake linali la masentimita 75, mulifupi mwake linali la masentimita 75, ndipo msinkhu wake unali wa masentimita makumi asanu. Pa matebulopo amayikapo zipangizo zophera nsembe zopsereza ndi nsembe zina. 43Choncho pa matebulopo ankayikapo nyama za nsembe zopsereza. Mbedza zitatu zazitali ngati chikhatho amazikoleka pa makoma pozungulira ponse.

Zipinda za Ansembe

44Munthu uja anapita nane mʼkati mwa bwalo ndipo ndinaona zipinda ziwiri. Chimodzi chinali pafupi ndi chipata chakumpoto kuyangʼana kummwera ndi china chinali pafupi ndi chipata chakummwera kuyangʼana kumpoto. 45Munthuyo anandiwuza kuti, “Chipinda chimene chikuyangʼana kummwera ndi cha ansembe amene amayangʼanira Nyumba ya Mulungu, 46ndipo chipinda chimene chikuyangʼana kumpoto ndi cha ansembe amene amayangʼanira guwa lansembe. Amenewa ndiwo ana a Zadoki, ndipo ndi okhawo mwa zidzukulu za Levi amene ayenera kutumikira pamaso pa Yehova mʼNyumba ya Mulungu.”

47Kenaka munthuyo anayeza bwalo; linali lofanana mbali zonse kutalika kwake, mulitali mwake munali mamita 53, ndipo mulifupi mwake munali mamita 53. Ndipo guwa lansembe linali kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu.

Nyumba ya Mulungu

48Munthuyo anapita nane pa khonde la Nyumba ya Mulunguyo. Anayeza mphuthu za khondelo ndipo zinali mamita awiri ndi theka mbali zonse. Mulifupi mwa chipatacho munali mamita asanu ndi awiri ndipo mulifupi mwa makoma ake munali mamita awiri mbali zonse. 49Mulitali mwa khonde munali mamita khumi, mulifupi mwake munali mamita asanu ndi limodzi kuchokera kutsogolo mpaka kumbuyo. Panali makwerero khumi, ndipo mbali zonse kunali nsanamira.