以斯帖记 9 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以斯帖记 9:1-32

犹太人的反击

1十二月,即亚达月十三日,是执行王谕旨的日子。那天,犹太人的仇敌原本想辖制他们,却反而被他们辖制。 2犹太人在亚哈随鲁王的各省各城聚集起来,攻击那些要害他们的人,无人能抵挡他们,因为各族都惧怕他们。 3各省的官员、总督、省长和为王办事的人因惧怕末底改,就都帮助犹太人。 4因为末底改已是王宫要员,他的名声传遍各省,权势日盛。 5犹太人用刀击杀所有敌人,任意消灭恨他们的人。 6犹太人单在书珊城就杀了五百人。 7他们还杀了巴珊大他达分亚斯帕他8坡拉他亚大利雅亚利大他9帕玛斯他亚利赛亚利代瓦耶撒他10这十人是犹太人的仇敌哈曼的儿子、哈米大他的孙子。但犹太人没有动他们的财物。

11当天,王获悉在书珊城被杀的人数, 12便对以斯帖王后说:“犹太人在书珊城杀了五百人,还杀了哈曼的十个儿子,在其余各省就更不知怎样了!现在你要什么?必赐给你。你还有何要求?必为你成就。” 13以斯帖回答说:“王若愿意,就请恩准书珊城的犹太人明天仍执行今天的谕旨,并把哈曼十个儿子的尸体吊在木架上。” 14王允准了,便在书珊城颁布谕旨,哈曼十个儿子的尸体便被吊了起来。 15亚达月十四日,书珊城的犹太人再次聚集起来,在城中杀了三百人,但没有动他们的财物。

16王其他各省的犹太人也都聚集起来自卫,得以脱离仇敌。他们杀了七万五千个仇敌,但没有动他们的财物。 17这事发生在亚达月十三日。十四日,犹太人休息,并以此日为设宴欢庆的日子。 18书珊城的犹太人在十三、十四日聚集杀敌,十五日才休息,并以此日为设宴欢庆的日子。 19因此,住在乡村的犹太人都以亚达月十四日为设宴欢庆的节日,并互赠礼物。

普珥节

20末底改把这些事记录下来,写信给亚哈随鲁王国内远近各省的犹太人, 21吩咐他们每年在亚达月十四、十五日守节期, 22设宴欢庆,互赠礼物,周济穷人,以纪念犹太人在此月此日得以脱离仇敌,化忧为乐,转悲为喜。

23犹太人接受了末底改写给他们的信,同意每年庆祝这个节日。 24因为犹太人的仇敌亚甲哈米大他的儿子哈曼曾经阴谋毁灭犹太人,曾经抽普珥,即抽签,要杀戮、灭绝他们。 25但王知道这阴谋后,便降旨使哈曼谋害犹太人的恶计落到他自己头上,将他及其众子吊在木架上。 26他们借用普珥这个词,称这两天为普珥节。犹太人因这信上的一切话,又因所看见、所经历的事, 27就为自己、自己的后代和归属他们的人定下规矩:每年必按时守这两天为节日,永不废弃。 28各省各城、家家户户、世世代代都要纪念、遵守这节日,使犹太人永不中断过普珥节,他们的后代也不可忘记。

29亚比孩的女儿以斯帖王后和犹太末底改以全权写第二封信,嘱咐犹太人守这普珥节, 30用和善、真诚的话写信给亚哈随鲁王国一百二十七省的所有犹太人, 31嘱咐他们照犹太末底改以斯帖王后的指示,按他们为自己及其后代所规定的,按时守普珥节,禁食哀哭。 32以斯帖的命令确定了普珥节,这命令被记载下来。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Estere 9:1-32

Chigonjetso cha Ayuda

1Pa mwezi wa 12, mwezi wa Adara pa tsiku la 13 la mwezi womwewo, tsiku limene lamulo loyamba lija la mfumu linayembekezereka kuti litsatidwe, pamene adani a Ayuda anati awononge Ayudawo, zinthu zinasintha. Ayuda ndiwo anawononga adani awo. 2Ayuda anasonkhana mʼmizinda ya zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero kuthira nkhondo onse amene anafuna kuwawononga. Palibe amene akanalimbana nawo chifukwa anthu onse a mitundu ina anachita nawo mantha. 3Ndipo akuluakulu onse a zigawo, akalonga, akazembe ndi ogwira ntchito za mfumu anathandiza Ayuda, chifukwa anachita mantha ndi Mordekai. 4Pajatu Mordekai anali munthu wamkulu mʼnyumba ya ufumu. Mbiri yake inafalikira zigawo zonse, ndipo mphamvu zake zinakulirakulirabe.

5Motero Ayuda anakantha adani awo onse ndi lupanga, kuwapha ndi kuwawononga, ndipo anachita chimene chinawakomera kwa adani awo. 6Ku likulu la mzinda wa Susa, Ayuda anapha ndi kuwononga anthu 500. 7Ayuda anaphanso Parisandata, Dalifoni, Asipata, 8Porata, Adaliya, Aridata, 9Parimasita, Arisai, Aridai ndi Vaisata, 10ana khumi a Hamani, mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalande katundu wawo.

11Tsiku lomwelo anawuza mfumu chiwerengero cha anthu amene anaphedwa mu likulu la mzinda wa Susa. 12Mfumu inati kwa mfumukazi Estere, “Ayuda apha ndi kuwononga anthu 500 ndi ana khumi a Hamani mu likulu la mzinda wa Susa. Nanga ku zigawo zina zonse za mfumu achitako chiyani? Kodi tsopano ukupemphanso chiyani? Chimene ukupempha ndidzakupatsa. Kodi ukufuna chiyani? Chimene ukufuna ndidzakupatsa.”

13Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni mfumu, apatseni chilolezo Ayuda okhala mu Susa kuti achitenso zimene achita lerozi mawa, potsata lamulo ndipo mulole kuti ana khumi a Hamani aja mitembo yawo ipachikidwe pa mtanda.”

14Choncho mfumu inalamula kuti izi zichitike. Anapereka lamulo mu Susa ndipo mitembo ya ana khumi a Hamani anayipachika pa mtanda. 15Ayuda a mu mzinda wa Susa anasonkhana pamodzi pa tsiku la 14 la mwezi wa Adara ndipo anapha anthu 300 mu Susa, koma sanatenge katundu wawo.

16Tsono Ayuda ena onse amene anali mu zigawo za mfumu anasonkhananso kudziteteza ndipo sanasautsidwenso ndi adani popeza anapha anthu 75,000 koma sanalande zofunkha zawo. 17Zonsezi zinachitika pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara ndipo pa tsiku la 14 anapumula ndi kupanga tsikuli kuti likhale la madyerero ndi chikondwerero.

Kukondwerera Purimu

18Koma Ayuda okhala mu Susa anasonkhana pa tsiku la 13 ndi la 14 ndipo anakonza tsiku la 15 kuti likhale tsiku la madyerero ndi chikondwerero.

19Ichi ndi chifukwa chake Ayuda a ku midzi, amene amakhala mʼzithando amasunga tsiku la 14 la mwezi wa Adara ngati la madyerero ndi chikondwerero, tsiku lopatsana mphatso.

20Mordekai analemba mawu awa mʼmakalata ndipo anawatumiza kwa Ayuda onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero, a pafupi ndi a kutali: 21Anati chaka chilichonse, Ayudawo azisunga tsiku la 14 ndi 15 la mwezi wa Adara, 22ngati masiku amene Ayuda anapulumutsidwa kwa adani awo, ndiponso ngati mwezi umene chisoni chawo chinasandulika chimwemwe ndi kulira kwawo kunasandulika chikondwerero. Anawalembera kuti azisunga masikuwa ngati masiku a madyerero ndi chikondwerero, masiku opatsana mphatso zachakudya kwa wina ndi mnzake komanso opereka mphatso kwa osauka.

23Choncho Ayuda anavomereza kusunga masikuwa ngati a chikondwerero monga analembera Mordekai. 24Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, mdani wa Ayuda onse, anakonza chiwembu chakupha ndi kuwononga Ayuda ndipo anachita maere otchedwa Purimu kuti awaphe ndi kuwawononga. 25Koma mfumu itazindikira za chiwembuchi, inalamula kuti zilembedwe mʼmakalata kuti chiwembu chimene Hamani anakonzera Ayuda chigwere pa iye mwini, ndi kuti iye pamodzi ndi ana ake apachikidwe pa mtanda. 26Ndi chifukwa chake masiku amenewa amatchedwa masiku a Purimu potsata dzina lakuti Purimu. Chifukwa cha kalata ya Mordekai ndiponso chifukwa cha zimene anaziona ndi kuwachitikira, 27Ayuda onse anagwirizana kukhazikitsa lamulo lokhudza iwo, zidzukulu zawo ndi onse amene adzapanga nawo ubale kuti asalephere kusunga masiku awiri amenewa chaka chilichonse monga zinalembedweramo ndiponso potsata nthawi imene anayika. 28Azisunga ndi kukumbukira masiku amenewa mu mʼbado uliwonse ndi banja lililonse, mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse. Ndipo Ayuda asadzasiye kukondwerera masiku a Purimuwa ndiponso zidzukulu zawo zisadzaleke kuwakumbukira.

29Choncho mfumukazi Estere, mwana wa mkazi wa Abihaili, pamodzi ndi Mordekai Myuda analemba ndi ulamuliro onse kutsimikizira kalata iyi yachiwiri yokhudza Purimu. 30Ndipo Mordekai anatumiza makalata kwa Ayuda onse ku zigawo 127 za ufumu wa Ahasiwero. Kalatayi inali ya mawu a mtendere ndiponso a kukhulupirika 31kuti azisunga masiku a Purimu pa nyengo imene inavomerezeka monga mmene Mordekai Myuda ndi mfumukazi Estere anawalamulira ndiponso monga anadziyikira eni okha ndi zidzukulu zawo zonena za nthawi zawo za kusala zakudya ndi kulira. 32Lamulo la Estere linakhazikitsa mwambo wa Purimuwu ndipo zinalembedwa mʼmabuku.