以弗所书 4 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

以弗所书 4:1-32

信徒同属一体

1所以,我这为主被囚禁的劝你们,既然蒙了上帝的呼召,就要过与所蒙的呼召相称的生活。 2凡事要谦虚、温柔、忍耐,用爱心互相宽容, 3以和平彼此联结,竭力持守圣灵所赐的合一。 4正如你们蒙召后有同一个盼望,你们同属一个身体,有同一位圣灵、 5同一位主、同一个信仰、同一种洗礼、 6同一位上帝,就是万物之父。祂超越万物,贯穿万物,且在万物之中。

7然而,我们各人都是按照基督所赐的分量领受恩典。 8因此圣经上说:

“祂升上高天时,

带着许多俘虏,

将恩赐赏给众人。”

9既然说“升上”,岂不表示祂曾经降到地上吗? 10降下的是祂,升到诸天之上的也是祂,祂充满万物。 11祂赐恩让一些人做使徒,一些人做先知,一些人做传福音的,一些人做牧师和教师, 12为要装备信徒,使他们各尽其职,建立基督的身体, 13直到我们对上帝的儿子有一致的信仰和认识,逐渐成熟,达到基督那样完美的生命。 14这样,我们就不再像小孩子,被各种异端邪说之风吹得飘来飘去,被人的阴谋诡计欺骗,随波逐流。 15相反,我们说话要凭爱心坚持真理,在各方面都要追求长进,更像元首基督。 16整个身体靠祂巧妙地结合在一起,筋骨相连,彼此供应,使各部位各尽其职,身体便渐渐长大,在爱中建立起来。

新人新生命

17因此,我奉主的名郑重地劝告各位,不要再像不信的外族人一样过着心灵空虚的日子。 18他们因为愚昧无知,顽固不化,理智受到蒙蔽,与上帝所赐的生命隔绝了。 19他们丧尽天良,放纵情欲,沉溺于各种污秽的事。 20但基督绝不是这样教导你们的。

21如果你们听过祂的事,领受了祂的教诲,就是在祂里面的真理, 22就应该与从前的生活方式一刀两断,脱去因私欲的迷惑而渐渐败坏的旧人, 23洗心革面, 24穿上照着上帝形象所造的新人。这新人有从真理而来的公义和圣洁。

25所以不要再说谎,大家都要彼此说真话,因为我们都是一个身体的肢体。 26不要因生气而犯罪,不要到日落时还怒气未消, 27不要让魔鬼有机可乘。 28从前偷窃的要改过自新,自食其力,做正当事,以便能够分给有需要的人。 29污言秽语一句都不可出口,要随时随地说造就人的好话,使听的人得益处。 30不要让上帝的圣灵担忧,你们已经盖上了圣灵的印记,将来必蒙救赎。 31要从你们当中除掉一切的苦毒、恼恨、怒气、争吵、毁谤和邪恶。 32总要以恩慈、怜悯的心彼此相待,要互相饶恕,正如上帝在基督里饶恕了你们一样。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Aefeso 4:1-32

Umodzi Mʼthupi la Khristu

1Ine monga wamʼndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukulimbikitsani kuti mukhale moyo woyenera mayitanidwe amene munalandira. 2Mukhale odzichepetsa kwathunthu ndi ofatsa; mukhale oleza mtima, ololerana wina ndi mnzake mwachikondi. 3Muyesetse kusunga umodzi wa Mzimu; umodzi umene umatimangirira pamodzi mu mtendere. 4Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene anakuyitanirani. 5Pali Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi; 6Mulungu mmodzi ndi Atate a onse, ndipo ali mwa onse.

7Koma aliyense wa ife wapatsidwa chisomo molingana ndi muyeso wa mphatso ya Khristu. 8Nʼchifukwa chake akunena kuti,

“Iye atakwera kumwamba,

anatenga chigulu cha a mʼndende

ndipo anapereka mphatso kwa anthu.”

9Kodi mawu akuti, “Iye anakwera” akutanthauza chiyani, ngati Iyeyo sanatsikire kunsi kwa dziko lapansi? 10Iye amene anatsika ndi yemweyo anakwera koposa mʼmayiko a kumwamba onse, ndi cholinga choti zinthu zonse zikhale zodzaza ndi Iye. 11Iye ndiye amene anapereka mphatso kwa ena kuti akhale atumwi ndi ena aneneri, ena alaliki, ndi ena abusa ndi aphunzitsi. 12Ntchito yawo ndi kukonza oyera mtima kuti agwire ntchito ya utumiki kuti thupi la Khristu lilimbikitsidwe. 13Izi zidzatifikitsa tonse ku umodzi wachikhulupiriro, kumudziwa Mwana wa Mulungu, kukhwima msinkhu ndi kufika pa muyeso wangwiro weniweni wopezeka mwa Khristu.

14Motero sitidzakhalanso makanda, ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso ndi kuchenjera kwa anthu achinyengo amene amasocheretsa anthu ndi kuchenjera kwawo. 15Mʼmalo mwake, poyankhula choonadi mwachikondi, tidzakula mu zinthu zonse ndi kukhala thupi la Khristu, amene ndi Mutu, omwe ndi mpingo. 16Mwa Iye thupi lonse lalumikizidwa ndi kugwirana pamodzi ndi mitsempha yothandizira. Likukula ndi kudzilimbitsa lokha mwachikondi, pomwe chiwalo chilichonse chikugwira ntchito yake.

Malangizo pa Makhalidwe a Chikhristu

17Tsono ine ndikukuwuzani izi, ndipo ndikunenetsa mwa Ambuye, kuti musayendenso monga amachitira anthu a mitundu ina potsata maganizo awo opanda pake. 18Maganizo awo ndi odetsedwa, ndi osiyanitsidwa ndi moyo wa Mulungu chifukwa cha umbuli umene uli mwa iwo chifukwa cha kuwuma mtima kwawo. 19Popeza sazindikiranso kanthu kalikonse, adzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite mtundu uliwonse wa zoyipa ndi zilakolako zosatha.

20Koma inu simunadziwe Khristu mʼnjira yotere. 21Zoonadi munamva za Iye ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye molingana ndi choonadi chimene chili mwa Yesu. 22Inu munaphunzitsidwa molingana ndi moyo wanu wakale, kuchotsa umunthu wakale, umene ukupitirira kuwonongeka ndi zilakolako zachinyengo; 23kuti mukonzedwe mwatsopano mʼmitima mwanu; 24ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero.

25Chifukwa chake, aliyense wa inu aleke kunama ndipo ayankhule zoona kwa mʼbale wake, pakuti ife tonse ndife ziwalo za thupi limodzi. 26Kwiyani koma musachimwe. Dzuwa lisalowe mukanali chikwiyire. 27Musamupatse mpata Satana. 28Iye amene wakhala akuba asabenso, koma agwire ntchito ndi kuchita kenakake kaphindu ndi manja ake, kuti akhale ndi kenakake kogawana ndi amene akusowa.

29Mʼkamwa mwanu musatuluke mawu aliwonse onyansa, koma okhawo amene ndi othandiza kulimbikitsa ena molingana ndi zosowa zawo, kuti athandize amene akawamve. 30Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu amene mwasindikizidwa naye chizindikiro cha tsiku la kuwomboledwa. 31Chotsani kuzondana, ukali ndi kupsa mtima, chiwawa ndi kuyankhula zachipongwe, pamodzi ndi choyipa chilichonse. 32Mukomerane mtima ndi kuchitirana chifundo wina ndi mnzake. Khululukiranani wina ndi mnzake, monga momwe Mulungu anakukhululukirani mwa Khristu.