Chinese Contemporary Bible (Simplified)

士师记 17:1-13

米迦的神像

1以法莲山区住了一个名叫米迦的人。 2他对母亲说:“你那一千一百块银子丢了,我还听见你咒诅小偷。看啊,银子在我这里,是我拿去的。”他母亲说:“我儿啊,愿耶和华赐福给你!” 3米迦把一千一百块银子还给母亲。他母亲说:“我要为你把这些银子献给耶和华,用来雕刻、铸造神像。现在这银子还是你的。” 4米迦把银子还给母亲后,他母亲拿出二百块银子交给银匠雕刻、铸造神像,放在米迦的房子里。 5米迦有一个神庙,他制造了一件以弗得和一些家庭神像,并指派他的一个儿子做祭司。 6那时,以色列没有王,人人各行其是。

7犹大伯利恒住着一个年轻的利未人。 8他离开伯利恒想到别的地方居住,一路走到以法莲山区米迦的家。 9米迦问他:“你从哪里来?”他回答说:“我是从犹大伯利恒来的利未人,我要找一个住的地方。” 10米迦说:“你就住在我这里吧,做我的师父和祭司。我每年给你十块银子,还为你提供衣服和膳食。”利未人就进了米迦的家, 11住了下来。米迦待他就像待自己的儿子一样。 12这样,米迦派他做祭司,让他住在自己家里。 13米迦说:“现在我有一个利未人做我的祭司,耶和华一定会赐福给我。”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 17:1-13

Mafuno a Mika

1Munthu wina dzina lake Mika wochokera ku dziko la mapiri la Efereimu anawuza amayi ake kuti 2“Ndinamva inu mukutemberera munthu amene anaba ndalama zanu zasiliva 1,100. Ndalamazo zili ndi ine, ndinatenga ndine.”

Pamenepo amayi akewo anati, “Yehova akudalitse mwana wanga!”

3Choncho Mika anabweza ndalama 1,100 za siliva kwa amayi ake, ndipo amayi akewo anati, “Ine ndapatulira Yehova ndalama za silivazi kuti mwana wanga aseme fano ndi kulikuta ndi siliva. Ndiye tsopano ndikubwezera ndalamazo.”

4Tsono Mika atabweza ndalama zija kwa amayi ake, iwo anatengapo ndalama za siliva 200 namupatsa mmisiri wosula siliva. Iye anakonza fano, nasungunula siliva uja ndi kulikutira fano lija. Ndipo Mika anayika fanolo mʼnyumba mwake.

5Mikayu anali ndi kachisi, ndipo anapanga efodi ndi mafano otchedwa terafimu. Anapatula mwana wake mmodzi kuti akhale wansembe. 6Masiku amenewo kunalibe mfumu ku Israeli. Aliyense amachita zomwe zinamukomera.

7Ku Betelehemu mʼdziko la Yuda kunali mnyamata wina amene anali wa fuko la Levi. 8Iyeyu anachoka mu mzinda wa Betelehemu uja ku Yuda kukafuna malo ena okhala. Akuyenda, anafika ku dziko la mapiri la Efereimu ku nyumba ya Mika.

9Tsono Mika anamufunsa kuti, “Mukuchokera kuti?”

Ndipo iye anayakha kuti, “Ndine Mlevi wochokera ku Betelehemu mʼdziko la Yuda. Ndikufunafuna malo okhala.”

10Tsono Mika anati kwa iye, “Khalani ndi ine. Mukhale ngati mlangizi wanga ndi wansembe, ndipo ine ndizikupatsani ndalama za siliva khumi pa chaka komanso zovala ndi zakudya.” 11Choncho Mleviyo anavomera kuti azikhala naye, ndipo mnyamatayo anakhala ngati mmodzi mwa ana ake aamuna. 12Pambuyo pake Mika anapatula Mleviyo ndipo mnyamatayu anakhala wansembe. Tsono ankakhala mʼnyumba ya Mika. 13Ndipo Mika anati, “Tsopano ndadziwa kuti Yehova adzandikomera mtima chifukwa Mleviyu ndiye wakhala wansembe wanga.”