Chinese Contemporary Bible (Simplified)

创世记 50:1-26

安葬雅各

1约瑟伏在父亲身上痛哭,亲吻他, 2然后吩咐医生用香料保存父亲的遗体。医生遵命而行, 3按照常例花了四十天处理尸体。埃及人为他哀悼七十天。

4哀悼的日子完了,约瑟对法老宫中的人说:“如果你们恩待我, 5请告诉法老,我父亲死前要我起誓把他葬在迦南他自己预备好的坟地。请准许我到迦南去安葬我父亲,我办完丧事就回来。” 6法老说:“去按照你的誓言埋葬你父亲吧。” 7于是,约瑟启程去埋葬他的父亲,随行的有法老所有的臣仆和埃及所有的达官贵人, 8以及约瑟全家、他的众弟兄和雅各的家眷,只有他们的孩子和牛羊仍然留在歌珊9随行的还有大队车辆和兵马,人数众多。 10他们来到约旦河附近的亚达麦场,在那里痛哭哀悼。约瑟为父亲守丧七天。 11迦南人看见他们在亚达麦场痛哭,就说:“埃及人在痛哭哀悼。”因此,约旦河附近的那个地方叫亚伯·麦西50:11 亚伯·麦西”意思是“埃及人在哀哭”。12以色列的儿子们遵照父亲的遗言, 13把父亲的遗体带回迦南,安葬在幔利附近、麦比拉田间的洞里。洞和田地都是亚伯拉罕以弗仑买来作坟地的。 14葬礼之后,约瑟就跟众弟兄和一切随行的人返回埃及

上帝的美好旨意

15约瑟的哥哥们见父亲死了,就说:“约瑟会不会怀恨在心,因我们以前恶待他而报复我们呢?” 16于是,他们派人去对约瑟说:“你父亲临终时交待这样的话给你, 17‘从前你哥哥们恶待你,求你饶恕他们的罪恶和过犯。’我们是你父亲的上帝的仆人,求你饶恕我们的罪恶。”约瑟听见这些话,就哭了。 18约瑟的哥哥们来见他,俯伏在他面前,说:“我们是你的奴仆。” 19约瑟对他们说:“你们不要害怕,我岂能代替上帝? 20从前你们是要加害于我,但上帝有祂的美意,祂借此保全许多人的性命,正如今日的光景。 21因此,你们不要害怕,我会照顾你们和你们的儿女。”约瑟好言好语地宽慰他们。

约瑟去世

22约瑟和他父亲全家住在埃及约瑟享年一百一十岁。 23他看到了以法莲的孙子,也曾把玛拿西的儿子玛吉的孩子抱在膝上。 24一天,约瑟对他的弟兄们说:“我快要死了,但上帝必看顾你们,带你们离开这里,回到祂起誓应许给亚伯拉罕以撒雅各的地方。” 25约瑟以色列的子孙发誓把他的骸骨带回迦南,又说:“上帝必看顾你们。” 26约瑟享年一百一十岁。他们把他的遗体用香料保存好,放在棺材里,停放在埃及

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 50:1-26

1Kenaka Yosefe anadzigwetsa pa nkhope ya abambo ake, nawapsompsona kwinaku akulira. 2Ndipo Yosefe analamula antchito ake a chipatala kuti akonze thupi la Israeli ndi mankhwala kuti lisawole. Kotero antchitowo anakonzadi thupilo. 3Antchito aja zinawatengera masiku 40 kuti akonze mtembo uja popeza ntchito ngati imeneyi inafunikira masiku monga amenewa. Ndipo Aigupto anamulira Yakobo kwa masiku makumi asanu ndi awiri.

4Yosefe atatha kulira maliro a abambo ake, anayankhula kwa nduna za Farao nati, “Ngati mungandikomere mtima, chonde mundiyankhulire kwa Farao kumuwuza kuti, 5‘Abambo anga anandilumbiritsa ndipo anati, ‘Ndatsala pangʼono kumwalira, ukandiyike mʼmanda amene ndinakumba ndekha mʼdziko la Kanaani.’ Tsono mundilole ndikayike abambo anga, ndipo ndikabweranso.’ ”

6Farao anati, “Pita ukayike abambo ako monga anakulumbiritsa kuti uchite.”

7Kotero Yosefe anapita kukayika abambo ake. Nduna zonse za Farao, akuluakulu a bwalo lake ndi akuluakulu a ku Igupto, anapita naye pamodzi. 8Anapitanso onse a pa banja la Yosefe ndi abale ake ndi onse amene anali a pa banja la abambo ake. Ana awo okha, nkhosa ndi ngʼombe zinatsala ku Goseni 9Asilikali okwera pa magaleta ndi asilikali a pa akavalo anapita nayenso pamodzi. Linali gulu lalikulu.

10Atafika pa Goreni ha-Atadi, pafupi ndi Yorodani, anachita mwambo waukulu wa maliro. Choncho Yosefe analira maliro a abambo ake masiku asanu ndi awiri. 11Akanaani amene ankakhala ku Goreni ha-Atadi ataona mwambo wa maliro anati, “Aigupto ali ndi mwambo wa maliro a akulu.” Ndi chifukwa chake malo amenewo a pafupi ndi Yorodani amatchedwa Abeli-Mizraimu.

12Choncho ana a Yakobo anachita monga momwe abambo awo anawalamula: 13Ndiye kuti ana a Yakobo anamunyamula kupita naye ku Kanaani kuti akamuyike mʼphanga limene lili mʼmunda wa Makipela pafupi ndi Mamre. Abrahamu anagula mundawo kwa Efroni Mhiti kuti pakhale manda. 14Atatha kuyika abambo ake, Yosefe anabwerera ku Igupto, pamodzi ndi abale ake ndi onse amene anapita nawo kukayika abambo ake.

Yosefe Abwereza Kutsimikizira Abale Ake

15Abale ake a Yosefe ataona kuti abambo awo amwalira, anati, “Nanga tidzatani ngati Yosefe anatisungira mangawa nafuna kutibwezera pa zoyipa zonse zimene tinamuchitira?” 16Motero anatumiza mawu kwa Yosefe kuti, “Abambo anu anasiya malangizo asanafe nati: 17‘Zimene mudzayenera kunena kwa Yosefe ndi izi: Ndikukupempha kuti uwakhululukire abale ako cholakwa chawo ndi machimo awo, popeza anakuchitira zoyipa.’ Ndiye tsopano chonde tikhululukireni zolakwa zimene ife akapolo a Mulungu wa abambo anu tinachita.” Yosefe atangomva mawu amenewa anayamba kulira.

18Kenaka abale ake anabwera nadzigwetsa pansi pamaso pake, nati, “Ife ndife akapolo anu.”

19Koma Yosefe anawawuza kuti, “Musachite mantha. Kodi ine ndalowa mʼmalo mwa Mulungu? 20Inu munafuna kundichitira zoyipa, koma Mulungu anasandutsa zoyipazo kuti zikhale zabwino kuti zikwaniritsidwe zimene zikuchitika panozi, zopulumutsa miyoyo yambiri. 21Kotero, musachite mantha. Ine ndidzasamalira inu pamodzi ndi ana anu omwe.” Tsono iye anawalimbitsa mtima powayankhula moleza mtima.

Kumwalira kwa Yosefe

22Yosefe anakhala mu Igupto pamodzi ndi banja lonse la abambo ake. Anakhala ndi moyo zaka 110 23ndipo anaona mʼbado wachitatu wa ana a Efereimu. Yosefe anatenganso ana a Makiri, mwana wa Manase kukhala ngati ana a mʼbanja lake.

24Kenaka Yosefe anati kwa abale ake, “Ine ndatsala pangʼono kufa. Koma mosakayika Mulungu adzakuyangʼanirani nadzakutengani kukutulutsani mʼdziko lino kupita ku dziko limene Iye analonjeza kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.” 25Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israeli lumbiro nati, “Lonjezani kuti Mulungu akadzakusungani mudzanyamula mafupa anga kuwachotsa ku malo kuno.”

26Choncho Yosefe anafa ali ndi zaka 110. Motero iwo atakonza thupi lake ndi mankhwala kuti lisawole, analiyika mʼbokosi ku Igupto.