Chinese Contemporary Bible (Simplified)

创世记 45:1-28

约瑟与弟兄相认

1约瑟再也控制不住自己,于是令所有的随从都出去。这样,约瑟跟弟兄们相认时,没有外人在场。 2约瑟放声大哭,埃及人听见了他的哭声,法老家也听到了这个消息。 3约瑟对他的弟兄们说:“我是约瑟!我的父亲还健在吗?”他的弟兄们吓得一句话也说不出来。

4约瑟叫他们走近一点,等他们靠近了,便说:“我是你们卖到埃及的弟弟约瑟5现在,你们不要因为把我卖到这里而自怨自责。上帝差我先来这里,是为了保住大家的性命。 6地上的饥荒已经两年了,我们还有五年不能种、不能收。 7上帝差我先来,是要为你们保留后代,又要大施拯救,保住你们的性命。 8这样看来,不是你们,是上帝把我送到这里的。祂使我成为法老的宰相,管理他的家和整个埃及9你们快回去告诉父亲,他儿子约瑟说,‘上帝已经使我管理整个埃及,请他立刻来这里。 10他可以带着他的子孙、牛羊及一切所有住在歌珊。那里离我很近, 11我可以奉养他,以免他和全家老少及仆婢牲畜都陷入绝境,因为还有五年的饥荒。’ 12你们和我弟弟便雅悯都看见了,这是我亲口对你们说的。 13你们要把我在埃及享有的尊荣和你们见到的一切都告诉父亲,尽快把他接来。” 14约瑟和弟弟便雅悯抱头痛哭, 15然后又亲吻其他弟兄,抱着他们痛哭,弟兄们跟他交谈起来。

16约瑟弟兄们到来的消息传到法老的王宫,法老和他的臣仆都为约瑟感到高兴。 17法老对约瑟说:“你去吩咐你的弟兄备好驴回迦南18把你们的父亲和家眷都接到我这里。我要把埃及最好的土地赐给他们,让他们享受这里肥美的物产。 19吩咐你的弟兄从埃及带着车去把他们的妻子、儿女和你们的父亲接来。 20不要担心你们在迦南的产业,因为埃及全国的美物都是你们的。”

21以色列的儿子们答应了。约瑟遵照法老的吩咐,为他的弟兄们预备好车辆和路上需用的粮食, 22又给他们每人一套新衣服,但给了便雅悯五套新衣服和三百块银子。 23约瑟送给父亲十头公驴,驮着埃及的美物,还送了十头母驴,驮着粮食、饼和其他食物,让父亲路上用。 24约瑟送弟兄们回去,嘱咐他们路上不要争吵。

25于是,他们离开埃及回到在迦南的父亲雅各那里, 26对父亲说:“约瑟还活着,并且做了埃及的宰相。”雅各惊呆了,不敢相信他们的话。 27雅各听了他们转述约瑟的话,又看见约瑟派来接他的车,才回过神来。 28以色列说:“我信了!我儿约瑟还活着,我要在死之前去见他。”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 45:1-28

Yosefe Adziwulula kwa Abale Ake

1Tsono Yosefe sanathenso kuwugwira mtima kuti asalire pamaso pa antchito ake ndipo anafuwula kuti, “Aliyense achoke pamaso panga!” Motero panalibe wina aliyense pamene Yosefe anadziwulula kwa abale ake. 2Ndipo analira mokweza mwakuti Aigupto anamva. Onse a ku nyumba kwa Farao anamvanso za zimenezi.

3Yosefe anati kwa abale ake, “Ine ndine Yosefe! Kodi abambo anga akanali ndi moyo?” Koma abale ake sanathe kumuyankha chifukwa anali ndi mantha kwambiri pamaso pake.

4Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, “Senderani pafupi nane.” Atasendera iye anati, “Ine ndine mʼbale wanu Yosefe amene munamugulitsa ku Igupto! 5Ndipo tsopano, musawawidwe mtima kapena kudzipsera mtima chifukwa choti munandigulitsa ine kuno, popeza Mulungu ananditsogoza ine kuti adzapulumutse miyoyo yanu. 6Kwa zaka ziwiri tsopano, kwakhala kuli njala mʼdziko muno, ndipo kwa zaka zisanu zikubwerazi, anthu sadzalima kapena kukolola. 7Koma Mulungu ananditsogoza kuti adzakusungeni ndi moyo ndi kuti mudzakhale ndi zidzukulu pa dziko lapansi.

8“Motero, si inu amene munanditumiza kuno koma Mulungu. Iye anandisandutsa kukhala nduna yayikulu ya Farao, ndipo zonse za mʼnyumba mwake zili mʼmanja mwangamu. Komanso amene akulamulira dziko lonse la Igupto ndi ine. 9Tsono fulumirani mubwerere kwa abambo anga ndi kuwawuza kuti, ‘Mwana wanu Yosefe akuti, Mulungu anandisandutsa kukhala mbuye wa dziko lonse la Igupto. Ndiye bwerani kuno musachedwe. 10Ndipo inu, ana anu, zidzukulu zanu, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe zanu ndi antchito anu amene muli nawo muzidzakhala mʼdziko la Goseni pafupi ndi ine. 11Ine ndizidzakupatsani zakudya kumeneko chifukwa zaka zisanu za njala zikubwera ndithu. Kupanda kutero, inu ndi mabanja anu pamodzi ndi anthu anu onse mudzasowa chakudya.’

12“Tsono inu nonse pamodzi ndi mʼbale wangayu Benjamini, mukuona kuti ndi inedi amene ndikuyankhula nanu. 13Mukawawuze abambo anga kuti ndili pa ulemerero ku dziko la Igupto kuno ndi zonse zimene mwaziona. Tsopano fulumirani kuti mukabwere nawo kuno abambo anga.”

14Kenaka Yosefe anakhumbatira Benjamini, mngʼono wake uja nayamba kulira. Nayenso Benjamini anayamba kulira atamukumbatira. 15Atatero, Yosefe anapsompsona abale ake onse aja, akulira. Pambuyo pake abale ake aja anacheza ndi Yosefe.

16Akunyumba kwa Farao atamva kuti abale ake a Yosefe abwera, Farao pamodzi ndi nduna zake zonse anakondwera. 17Farao anati kwa Yosefe, “Uwawuze abale ako kuti, ‘Senzetsani nyama zanu katundu ndi kubwerera ku dziko la Kanaani. 18Mukabwere nawo abambo anu ndi mabanja anu kuno, ndipo ine ndidzakupatsani dera lachonde kwambiri mʼdziko la Igupto. Mudzadya zokoma za mʼdzikoli.’ ”

19“Uwawuzenso kuti, ‘Tengani ngolo zingapo za kuno ku Igupto kuti mukakwezepo ana anu, akazi anu pamodzi ndi abambo ako ndi kubwera nawo kuno. 20Musadandaule zosiya katundu komweko chifukwa dziko lachonde la kuno ku Igupto lidzakhala lanu.’ ”

21Choncho ana a Israeli anachita zimenezo. Yosefe anawapatsa ngolo monga Farao analamulira, ndipo anawapatsanso chakudya cha paulendo wawo. 22Anaperekanso kwa aliyense zovala zatsopano, koma kwa Benjamini anapereka siliva wolemera pafupifupi makilogalamu anayi ndi zovala zisanu. 23Ndipo abambo ake anawatumizira izi: abulu khumi osenza zinthu zabwino kwambiri za ku Igupto, ndi abulu aakazi khumi osenza tirigu, buledi ndi zakudya zina za pa ulendo wake. 24Kenaka anawalola abale ake aja kuti azipita, ndipo akunyamuka, iye anawawuza kuti, “Osakangana mʼnjira!”

25Ndipo anachoka ku Igupto nafika kwa abambo awo Yakobo mʼdziko la Kanaani. 26Iwo anawuza abambo awo kuti, “Yosefe akanali ndi moyo! Ndiponsotu, ndiye akulamulira dziko la Igupto.” Yakobo anangoti kakasi osankhulupirira. 27Komabe atamufotokozera zonse zimene Yosefe anawawuza ndipo ataona ngolo zimene Yosefe anatumiza kuti adzakweremo popita ku Igupto, mtima wa Yakobo, abambo awo unatsitsimuka. 28Ndipo Israeli anati, “Ndatsimikizadi! Mwana wanga Yosefe akanali ndi moyodi. Ndipita ndikamuone ndisanafe.”