1 Летопись 5 – CARST & CCL

Священное Писание (Восточный перевод), версия для Таджикистана

1 Летопись 5:1-26

Потомки Рувима

1Сыновья Рувима, первенца Исроила. (Он был первенцем, но когда он осквернил брачное ложе своего отца5:1 См. Нач. 35:22; 49:3-4., права его первородства были отданы сыновьям Юсуфа, сына Исроила, поэтому он и не упоминается в родословии по своему первородству; 2и хотя Иуда был сильнейшим среди своих братьев и от него произошёл правитель, права первородства отошли к Юсуфу.) 3Сыновья Рувима, первенца Якуба:

Ханох, Фаллу, Хецрон и Харми.

4Сыновья Иоиля:

его сын Шемая, сыном которого был Гог, сыном которого был Шимей, 5сыном которого был Миха, сыном которого был Реая, сыном которого был Баал, 6сыном которого был Беэра, которого увёл в плен Тиглатпаласар, царь Ассирии. Беэра был вождём рувимитов.

7Его родичи по кланам, исчисленные по их родословиям:

Иеил был главным, затем Закария 8и Бела, сын Азаза, внук Шема, правнук Иоиля. Они населяли земли от Ароера до Нево и Баал-Меона. 9К востоку же они занимали земли до самого края пустыни, которая тянется к реке Евфрат, потому что их стада умножились в Галааде.

10Во время царствования Шаула рувимиты вели войну с агритянами, которые пали от их рук. Они поселились в жилищах агритян по всем восточным землям Галаада.

Потомки Гада

11Гадиты жили рядом с ними в Бошоне до самой Салхи:

12Иоиль был главным, Шафам – вторым после него, потом Ианай и Шафат в Бошоне.

13Их родичей по семьям было семеро:

Микаил, Мешуллам, Шева, Иорай, Иакан, Зия и Евер.

14Это сыновья Авихаила, сына Хури, сына Иароаха, сына Галаада, сына Микаила, сына Иешишая, сына Иахдо, сына Буза.

15Ахи, сын Авдиила, внук Гуни, был главой своего семейства.

16Гадиты жили в Галааде, в Бошоне и в его городах и на всех пастбищах Шарона, до самых их пределов.

17Все они были внесены в родословные записи во время царствования Иотама, царя Иуды, и Иеровоама, царя Исроила.

18У родов Рувима, Гада и половины рода Манассы было сорок четыре тысячи семьсот шестьдесят мужчин, пригодных к военной службе, – крепких мужчин, которые умели обращаться с щитом и мечом, натягивать лук и сражаться. 19Они вели войну с агритянами, Иетуром, Нафишем и Нодавом. 20Всевышний помог им в их сражении и отдал агритян и всех их союзников в их руки, потому что они взывали к Нему во время битвы. Он ответил на их молитвы, потому что они верили Ему. 21Они захватили скот агритян – пятьдесят тысяч верблюдов, двести пятьдесят тысяч овец и две тысячи ослов. В плен они взяли сто тысяч человек, 22и ещё множество пало убитыми, потому что та война была по воле Всевышнего. Гадиты жили в их землях до плена.

Восточная половина рода Манассы

23Народ половины рода Манассы был многочислен. Они населяли страну от Бошона до Баал-Хермона, Сенира и горы Хермон.

24Вот главы их семейств:

Ефер, Иши, Элиил, Азриил, Иеремия, Годавия и Иахдиил – доблестные воины, прославленные мужи, главы своих семейств. 25Но они нарушили верность Богу их предков и распутничали с богами народов страны, которых Всевышний истребил перед ними. 26И Бог Исроила побудил Пула (он же Тиглатпаласар)5:26 Пул – другое имя Тиглатпаласара III. Он правил с 745 по 727 гг. до н. э., царя Ассирии, и тот взял роды Рувима, Гада и половину рода Манассы в плен. Он увёл их в Халах, Хавор, Ару и на реку Гозан, где они находятся и по сегодняшний день.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 5:1-26

Fuko la Rubeni

1Ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli (iye anali woyamba kubadwa, koma atagona ndi mkazi wamngʼono wa abambo ake, ulemu wake wokhala mwana woyamba unaperekedwa kwa ana a Yosefe. Kotero iye sanalembedwe pa mndandanda wa mayina ngati mwana woyamba kubadwa, 2ndipo ngakhalenso Yuda anali wamphamvu kwambiri pakati pa abale ake, ndi kuti wolamulira anachokera mwa iye, ulemu wa mwana woyamba kubadwa unaperekedwa kwa Yosefe) 3ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli ndi awa:

Hanoki, Palu, Hezironi, ndi Karimi.

4Ana a Yoweli anali awa:

Semaya, Gogi,

Simei, 5Mika,

Reaya, Baala,

6ndiponso Beeri, amene Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri anamugwira ukapolo. Mtsogoleri wa fuko la Rubeni anali Beeri.

7Abale awo mwa mabanja awo, potsata mndandanda wa mʼbado wawo, ndi awa:

Yeiyeli, mtsogoleri, Zekariya, 8ndiponso Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yoweli. Iwo ankakhala ku Aroeri mpaka ku Nebo ndi Baala-Meoni. 9Iwo anakhala cha kummawa mpaka kukafika polowera mʼchipululu cha mbali ina ya Mtsinje wa Yufurate, chifukwa ziweto zawo zinaswana kwambiri mʼdziko la Giliyadi.

10Pa nthawi ya Sauli anachita nkhondo ndi Ahagiri ndi kuwagonjetsa. Tsono iwo anakhala mʼmatenti a Ahagiri ku dera lonse la kummawa kwa Giliyadi.

Fuko la Gadi

11Anthu a fuko la Gadi anakhala moyandikana ndi fuko la Rubeni ku Basani mpaka ku Saleka:

12Mtsogoleri wawo ku Basani anali Yoweli, wachiwiri anali Safamu, kenaka Yanayi ndi Safati.

13Abale awo mwa mabanja awo anali awa:

Mikayeli, Mesulamu, Seba, Yorayi, Yakani, Ziya ndi Eberi, onse ali asanu ndi awiri.

14Amenewa ndiwo anali ana a Abihaili, mwana wa Huri, mwana wa Yarowa, mwana wa Giliyadi, mwana wa Mikayeli, mwana wa Yesisayi, mwana wa Yahido, mwana wa Buzi.

15Ahi mwana wa Abdieli, mwana wa Guni, anali mtsogoleri wa banja la makolo awo.

16Fuko la Gadi linakhala ku Giliyadi, ku Basani ndi midzi yozugulira, madera onse a msipu a ku Saroni mpaka kumene amalekezera.

17Mayina onsewa analembedwa potsata mndandanda wa mibado yawo pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu mfumu ya Yuda ndi Yeroboamu mfumu ya Israeli.

18Mafuko a Rubeni, Gadi ndi theka la Manase, anali ndi anthu 44, 760 okonzeka kulowa usilikali; anthu amatupi amphamvu, amene amatha kugwiritsa ntchito chishango ndi lupanga, amene amatha kugwiritsa ntchito uta, amene anaphunzitsidwa kumenya nkhondo. 19Iwo anachita nkhondo ndi Ahagiri, Yeturi, Nafisi ndi Nodabu. 20Iwowo anathandizidwa polimbana nawo ndipo Mulungu anapereka Ahagiri mʼmanja mwawo; popeza iwo anafuwulira kwa Mulungu pa nkhondopo. Iye anayankha mapemphero awo chifukwa anamudalira. 21Choncho iwo analanda ziweto za Ahagiri: ngamira 50,000, nkhosa ndi mbuzi 250,000 ndi abulu 2,000. Ndiponso anagwira akapolo 100,000, 22enanso ambiri anaphedwa, chifukwa nkhondoyo inali ya Mulungu. Ndipo iwo anakhala mʼdzikomo mpaka pa nthawi ya ukapolo.

Theka la Fuko la Manase

23Theka la fuko la Manase linkakhala ku dziko la kummawa kuyambira ku Basani mpaka ku Baala-Herimoni, kumene ndi ku Seniri (Phiri la Herimoni) ndipo anthuwo anali ochuluka kwambiri.

24Atsogoleri a mabanja awo anali awa: Eferi, Isi, Elieli, Azirieli, Yeremiya, Hodaviya ndi Yahidieli. Iwo anali asilikali olimba mtima, anthu otchuka, ndiponso atsogoleri a mabanja awo. 25Koma iwo anali osakhulupirika kwa Mulungu wa makolo awo ndipo anadzipereka okha kwa milungu ya anthu okhala mʼdzikomo amene Mulungu anawawononga pamene iwowo ankafika. 26Kotero Mulungu wa Israeli anayika mkwiyo mwa Puli mfumu ya Asuri (ameneyu ndi Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri) amene anatenga fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase kupita nawo ku ukapolo. Iye anapita nawo ku Hala, Habori, Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, kumene ali mpaka lero lino.