1 Царств 12 – CARSA & CCL

Священное Писание (Восточный перевод), версия с «Аллахом»

1 Царств 12:1-25

Прощальная речь Шемуила

1Шемуил сказал народу Исраила:

– Я послушался вас во всём, что вы мне сказали, и поставил над вами царя. 2Теперь ваш вождь – царь. А я стар и сед, но мои сыновья здесь с вами. Я был вашим вождём с юности до сегодняшнего дня. 3Вот я. Свидетельствуйте против меня в присутствии Вечного и Его помазанника. Чьего вола я взял? Чьего осла? Кого обманул? Кого притеснял? У кого я брал взятку, чтобы ею закрыть себе глаза? Свидетельствуйте против меня, и я верну вам то, что взял.

4– Ты не обманывал и не притеснял нас, – ответили они. – Ты ничего ни у кого не брал.

5Шемуил сказал им:

– Вечный свидетель против вас, и Его помазанник также свидетель сегодня, что вы ничего не нашли за мной.

– Да, Вечный – свидетель, – сказали они.

6Тогда Шемуил сказал народу:

– Вечный избрал Мусу и Харуна и вывел ваших предков из Египта. 7Итак, встаньте здесь, а я буду судиться с вами перед Вечным о всех спасительных делах Вечного, которые Он совершил для вас и ваших предков.

8После того как Якуб пришёл в Египет, они в беде воззвали к Вечному о помощи, и Вечный послал Мусу и Харуна, которые вывели ваших предков из Египта и поселили здесь.

9Но ваши предки забыли Вечного, своего Бога, и Он отдал их в руки Сисары, начальника войска Хацора12:9 См. Суд. 4:2., и в руки филистимлян, и в руки царя Моава, которые воевали против них. 10Ваши предки воззвали к Вечному и сказали: «Мы согрешили. Мы оставили Тебя и служили статуям Баала и Астарты. Но теперь спаси нас от врагов, и мы будем служить Тебе». 11Тогда Вечный послал судей: Гедеона12:11 Букв.: «Иеруб-Баала». Иеруб-Баал – второе имя Гедеона (см. Суд. 6:32)., Варака, Иефтаха и наконец меня12:11 В других рукописях: «Самсона»., и спас вас от окружавших вас со всех сторон врагов, чтобы вы жили в безопасности.

12Но когда вы увидели, что Нахаш, царь аммонитян, двинулся против вас, вы сказали мне: «Нет, мы хотим, чтобы нами правил царь», несмотря на то что вашим царём был Аллах. 13Итак, вот ваш царь, которого вы выбрали, тот, о ком вы просили. Вечный поставил над вами царя. 14Если вы будете бояться Вечного, служить Ему и слушаться Его, не станете бунтовать против Его повелений, и если и вы, и царь, который станет править вами, будете следовать Вечному, вашему Богу, – прекрасно! 15Но если вы не будете слушаться Вечного и станете бунтовать против Его повелений, то Его рука будет против вас, как была против ваших предков.

16Теперь встаньте и посмотрите на то великое дело, которое Вечный совершит у вас на глазах! 17Не жатва ли сейчас пшеницы? Но я воззову к Вечному, и Он пошлёт гром и дождь. Тогда вы поймёте, какой грех в глазах Вечного вы совершили, когда просили о царе.

18Шемуил воззвал к Вечному, и в тот же день Вечный послал гром и дождь. Весь народ очень испугался Вечного и Шемуила. 19Народ сказал Шемуилу:

– Помолись Вечному, твоему Богу, за нас, твоих рабов, чтобы нам не умереть. Ведь ко всем нашим прочим грехам мы прибавили ещё один, попросив себе царя.

20– Не бойтесь, – ответил Шемуил. – Вы совершили зло, но всё-таки не отступайте от Вечного, служите Вечному от всего сердца. 21Не уклоняйтесь от Него вслед за никчёмными идолами. Они не могут сделать никакого добра и не могут защитить вас, потому что они – ничто. 22Ради Своего великого имени Вечный не отвергнет Свой народ, потому что Вечному было угодно сделать вас Своим народом. 23Что же до меня, то да не согрешу я перед Вечным в том, что перестану молиться о вас. Я буду наставлять вас на добрый и правильный путь. 24Только бойтесь Вечного и верно служите Ему от всего сердца. Помните, какие великие дела Он для вас совершил. 25Но если вы станете и дальше делать зло, то и вы, и ваш царь будете уничтожены.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Samueli 12:1-25

Samueli Atsanzika Anthu

1Pambuyo pake Samueli anawuza Aisraeli onse kuti, “Ine ndamvera zonse zimene munandiwuza ndipo ndakupatsani mfumu kuti izikulamulirani. 2Tsopano muli ndi mfumu imene izikutsogolerani, koma ine ndakalamba, kumutu kwanga kuli imvi zokhazokha ndipo ana anga ali pamodzi ndi inu. Ndakhala ndili mtsogoleri wanu kuyambira ndili mnyamata mpaka lero. 3Ine ndili pano. Ngati ndinalakwa chilichonse nditsutseni pamaso pa Yehova ndi wodzozedwa wake. Kodi ndinalanda ngʼombe ya yani? Kodi ndinalanda bulu wa yani? Kodi ndani amene ndinamudyera masuku pa mutu? Kodi ndinazunza yani? Kodi ndinalandira kwa yani chiphuphu choti nʼkundidetsa mʼmaso? Ngati ndinachita chilichonse cha izi, ine ndidzakubwezerani.”

4Iwo anayankha kuti, “Inu simunatidyere masuku pamutu kapena kutizunza. Simunalande kanthu kalikonse ka munthu.”

5Samueli anawawuza kuti, “Yehova ndiye mboni pakati pa inu ndi ine, ndiponso wodzozedwa wake ndi mboni kuti lero simunapeze chilichonse mʼdzanja langa.”

Iwo anati, “Inde, Yehova ndiye mboni.”

6Samueli anawawuzanso kuti, “Yehova ndiye amene anasankha Mose ndi Aaroni kuti atulutse makolo anu mʼdziko la Igupto. 7Nʼchifukwa chake tsopano imani pomwepa kuti ndikufotokozereni pamaso pa Yehova, za ntchito za chipulumutso zimene Yehova anachitira inu ndi makolo anu.

8“Yakobo atapita ku dziko la Igupto, Aiguptowo akuwazunza, iwo analirira kwa Yehova kuti awathandize, ndipo Yehova anatumiza Mose ndi Aaroni, amene anatulutsa makolo anu mʼdziko la Igupto ndi kudzawakhazika pa malo ano.

9“Koma iwo anayiwala Yehova Mulungu wawo, choncho Yehova anawapereka mʼdzanja la Sisera mkulu wa ankhondo wa mzinda wa Hazori, ndiponso mʼmanja mwa Afilisti ndi mfumu ya Mowabu. Mafumu onsewa anathira nkhondo makolo anu. 10Tsono iwo analira kwa Yehova nati, ‘Ife tachimwa, chifukwa tamusiya Yehova ndi kumatumikira mafano a Baala ndi Asiteroti. Koma tsopano tilanditseni mʼmanja mwa adani athu ndipo tidzakutumikirani.’ 11Choncho Yehova anatumiza Yeru-Baala, Bedani, Yefita ndi Samueli ndipo anakulanditsani mʼmanja mwa adani anu amene anakuzungulirani, kotero munakhala mwamtendere.

12“Koma mutaona kuti Nahasi mfumu ya Amoni inkabwera kudzamenyana nanu, inu munandiwuza kuti, ‘Ayi, ife tikufuna mfumu kuti itilamulire,’ ngakhale kuti Yehova Mulungu wanu ndiye anali mfumu yanu. 13Tsopano nayi mfumu imene mwayisankha, imene munayipempha. Onani, Yehova wakupatsani mfumu. 14Ngati muziopa Yehova ndi kumamutumikira ndi kumamumvera, osamupandukira ndiponso ngati inu pamodzi ndi mfumu yanu mudzatsata Yehova Mulungu wanu, ndiye zinthu zonse zidzakuyenderani bwino. 15Koma mukapanda kumvera Yehova ndi kumupandukira, ndiye adzakulangani pamodzi ndi mfumu yanu yomwe.

16“Tsono imani pomwepa kuti muone chinthu chachikulu chimene Yehova ali pafupi kuchita pamaso panu! 17Kodi ino si nthawi yokolola tirigu? Komabe ndipemphera kwa Yehova kuti agwetse mvula ya mabingu. Zikatero mudzadziwa kuti tchimo lanu limene mwachita popempha mfumu kwa Yehova ndi lalikulu.”

18Choncho Samueli anapemphera, ndipo Yehova anatumiza mvula ya mabingu tsiku lomwelo. Apo anthu aja anaopa kwambiri Yehova ndi Samueli.

19Tsono anamupempha Samueli nati, “Chonde mutipempherere kwa Yehova, ife atumiki kuti tingafe pakuti pa machimo athu onse tawonjezapo tchimo lopempha mfumu.”

20Samueli anayankha kuti, “Musaope, inu mwachitadi tchimo ili, koma musaleke kumutsata Yehova ndi kumutumikira ndi mtima wanu wonse. 21Ndipo musatsate mafano achabechabe amene alibe phindu ndipo sangakupulumutseni popeza ndi achabechabe. 22Yehova adzakana anthu ake kuopa kuti dzina lake lamphamvu linganyozeke, pakuti chinamukondweretsa Yehova kuti akusandutseni inu kukhala anthu ake. 23Ndiponso kunena za ine, zisachitike kuti ndichimwire Yehova pakulephera kukupemphererani. Ndipo ine ndidzakuphunzitsani njira yabwino ndi yolungama kuti muziyendamo. 24Koma onetsetsani kuti mukuopa Yehova ndi kumutumikira mokhulupirika ndi mtima wanu wonse. Nthawi zonse muziganizira zinthu zazikulu wakhala akukuchitirani. 25Komabe mukapitirira kuchita zoyipa, ndiye kuti inu pamodzi ndi mfumu yanu mudzachotsedwa.”