Иеремия 33 – CARSA & CCL

Священное Писание (Восточный перевод), версия с «Аллахом»

Иеремия 33:1-26

Обещание возрождения Исраила

1Когда Иеремия ещё был заключён в царской темнице, слово Вечного было к нему во второй раз:

2– Так говорит Вечный, Который сотворил землю, Вечный, Который создал её и утвердил, Тот, Чьё имя – Вечный: 3Воззови ко Мне, и Я тебе отвечу – возвещу тебе великое и недоступное, чего ты не знаешь.

4Ведь так говорит Вечный, Бог Исраила, о домах этого города и о царских дворцах Иудеи, которые были разрушены, чтобы построить защиту от осадных валов и от меча атакующих:

5– Исраильтяне будут сражаться с вавилонянами, но их дома наполнятся трупами тех, кого Я сражу в Своём гневе и ярости, потому что Я скрыл Своё лицо от этого города из-за всех его злодеяний. 6Но Я дам ему и здоровье, и исцеление; Я исцелю Мой народ и открою ему изобилие мира и безопасности. 7Я восстановлю Иудею и Исраил и отстрою их такими же, как прежде. 8Я очищу их от всех грехов, которые они совершили передо Мной, и прощу все их беззакония, которые они совершили, восстав против Меня. 9Тогда этот город принесёт Мне славу, радость, хвалу и честь перед всеми народами земли, которые услышат обо всём добре, которое Я делаю для него; они испугаются и затрепещут, узнав обо всём добре и мире, которые Я дам этому городу.

10Так говорит Вечный:

– Вы говорите об этой земле: «Это пустыня без людей и животных». Но раздадутся ещё в городах Иудеи и на опустевших улицах Иерусалима, где не живут ни люди, ни звери, 11звуки веселья и радости, голоса жениха и невесты, голоса несущих благодарственные жертвы в дом Вечного и говорящих:

«Славьте Вечного, Повелителя Сил,

потому что Он благ;

милость Его – навеки».

Ведь Я верну в эту землю благополучие, как прежде, – говорит Вечный.

12Так говорит Вечный, Повелитель Сил:

– В этом пустынном краю, где нет ни людей, ни животных, вблизи всех этих городов снова будут пастбища, на которых пастухи будут пасти свои стада. 13В городах нагорий, западных предгорий и Негева, в землях Вениамина, в окрестностях Иерусалима и в городах Иудеи стада будут вновь проходить под рукою того, кто их пересчитывает, – говорит Вечный.

14Непременно наступят дни, – возвещает Вечный, – когда Я исполню доброе обещание, которое Я дал Исраилу и Иудее.

15– В те дни и в то время,

когда Я произращу праведную Ветвь33:15 Ветвь – одно из имён Исы аль-Масиха (см. Ис. 4:2; Зак. 3:8; 6:12-13; Рим. 15:8-13). из рода Давуда,

Он будет вершить в стране справедливость и правосудие.

16В те дни Иудея будет спасена

и Иерусалим будет жить в безопасности.

Вот имя, которым его назовут:

«Вечный – наша праведность».

17Ведь так говорит Вечный:

– Давуд не останется без потомка, сидящего на престоле Исраила, 18а священнослужители-левиты не останутся без стоящего всегда передо Мной, чтобы совершать всесожжения, сжигать хлебные приношения и приносить жертвы.

19Было к Иеремии слово Вечного:

20– Так говорит Вечный: Если кто-нибудь сможет расторгнуть Мой союз с днём и Мой союз с ночью, чтобы день и ночь больше не наступали в положенное им время, 21то расторгнется и Моё соглашение с Давудом, Моим рабом, и со священнослужителями-левитами, которые несут службу предо Мной, и у Давуда не будет больше потомков, чтобы править на его престоле. 22Я сделаю потомков Давуда, Моего раба, и левитов, которые несут предо Мной служение, бесчисленными, как звёзды на небе, и неисчислимыми, как песок на морском берегу.

23Вечный обратился к Иеремии:

24– Разве ты не обратил внимания, как эти люди говорят: «Вечный отверг оба царства, которые Он избрал» – и до того презирают Мой народ, что даже народом его больше не считают?

25Так говорит Вечный:

– Как верно то, что Я заключил союз с днём и ночью и дал уставы для небес и земли, 26так верно и то, что Я не отвергну потомков Якуба и Моего раба Давуда и буду избирать из его потомков правителя над потомками Ибрахима, Исхака и Якуба. Я восстановлю и помилую их.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 33:1-26

Lonjezo la Kubwezeretsedwa

1Yeremiya akanali mʼndende mʼbwalo la alonda, Yehova anayankhula nayenso kachiwiri nati: 2“Yehova amene analenga dziko lapansi, kuliwumba ndi kulikhazikitsa; amene dzina lake ndi Yehova, akuti, 3‘Unditame mopemba ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuwuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziwa.’ 4Yehova Mulungu wa Israeli akunenapo pa za nyumba za mu mzinda muno ndiponso pa za nyumba za mafumu a Yuda. Zidzagwetsedwa, ndipo palibe chifukwa cholimbana ndi mitumbira ya nkhondo ya Ababuloni. 5Ababuloni akubwera kudzawuthira nkhondo mzindawu ndipo nyumba zake zidzadzaza ndi mitembo ya anthu amene ndidzawapha mokwiya ndi mwaukali. Ndawufulatira mzinda uno chifukwa cha zoyipa zake zonse.

6“ ‘Pambuyo pake mzindawu ndidzawupatsanso moyo ndi kuwuchiritsa; ndidzachiritsa anthu anga ndi kuwapatsa chitetezo ndi mtendere weniweni. 7Ndidzawakhazikanso Ayuda ndi Aisraeli ku dziko lawo, ndipo ndidzawabwezera monga mmene analili poyamba. 8Ndidzawayeretsa pochotsa zoyipa zonse zimene anandichitira, ndiponso ndidzawakhululukira machimo onse amene anachita pondiwukira. 9Mzinda wa Yerusalemu udzandipatsa chimwemwe, chiyamiko ndi ulemerero. Anthu a mitundu yonse adzanditamanda akadzamva za zabwino zonse zimene ndawuchitira mzindawu. Iwo adzachita mantha ndi kunjenjemera poona madalitso ochuluka ndi mtendere zimene ndapereka kwa mzinda umenewu.’

10“Yehova akuti, ‘Inu mumanena za malo ano kuti ndi bwinja,’ malo opandamo anthu kapena nyama. Komatu mizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu mʼmene tsopano muli zii mudzamvekanso 11mfuwu wachimwemwe ndi mawu achisangalalo, mawu a mkwatibwi ndi mkwati. Mʼnyumba ya Mulungu mudzamvekanso nyimbo za anthu amene akudzapereka nsembe zothokoza Yehova. Azidzati,

“Yamikani Yehova Wamphamvuzonse,

popeza Iye ndi wabwino;

pakuti chifundo chake nʼchamuyaya.”

Pakuti ndidzabwezeretsa zinthu zabwino za dziko lino monga zinalili poyamba, akutero Yehova.

12“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Malo ano, a chipululu ndi wopanda anthu kapena nyama, mʼmizinda yake yonse mudzakhala msipu umene abusa adzadyetserako nkhosa zawo. 13Ku mizinda ya kumapiri, ya kuchigwa, ya ku Negevi, ya ku dera la Benjamini, ku dziko lozungulira Yerusalemu, ndi ku mizinda ya Yuda, nkhosa zidzadutsanso pamaso pa munthu woziwerenga,’ akutero Yehova.

14“ ‘Taonani masiku akubwera,’ akutero Yehova, ‘pamene ndidzachitadi zokoma zimene ndinalonjeza Aisraeli ndi nyumba ya Yuda.

15“ ‘Mʼmasiku amenewo ndi pa nthawi imeneyo

ndidzaphukitsa Nthambi yolungama kuchokera ku banja la Davide;

munthuyo adzachita zolungama ndi zabwino mʼdziko.

16Mʼmasiku amenewo Yuda adzapulumuka

ndipo Yerusalemu adzakhala mwamtendere.

Dzina limene mzindawu udzadziwike nalo ndi ili:

Yehova Chilungamo Chathu.’

17Yehova akunena kuti, ‘Davide sadzasowa mdzukulu wolowa mʼmalo mwake pa mpando waufumu wa Israeli, 18ngakhale ansembe, amene ndi Alevi, sadzasowanso munthu woyima pamaso panga nthawi zonse wopereka nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi nsembe zina.’ ”

19Yehova anawuza Yeremiya kuti: 20Mawu anga ndi awa. Ine ndinachita pangano ndi usana ndi usiku kuti zizibwera pa nthawi yake. Pangano limeneli inu simungaliphwanye. 21Ndinachitanso pangano ndi Davide, mtumiki wanga kuti nthawi zonse adzakhala ndi mdzukulu wodzakhala pa mpando wake waufumu. Ndinachitanso pangano ndi Alevi kuti iwonso adzanditumikira nthawi zonse. Mapangano amenewa sadzaphwanyidwa nthawi zonse. 22Ndidzachulukitsa ngati nyenyezi zamlengalenga ndiponso ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja zidzukulu za mtumiki wanga Davide ndiponso za Alevi amene amanditumikira Ine.

23Yehova anafunsa Yeremiya kuti, 24“Kodi sunamve mmene anthu ena akumanenera kuti, ‘Yehova wakana maufumu awiriwa amene Iye anawasankha.’ Kotero anthuwo akunyoza anthu anga ndipo sakuwayesanso mtundu wa anthu. 25‘Koma Ine Yehova ndinachita pangano ndi usana ndi usiku. Ndinakhazikitsanso malamulo oyendetsa dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, 26monga ndachita zimenezi motsimikiza, choncho ndidzasunga pangano limene ndinachita ndi zidzukulu za Yakobo ndi Davide mtumiki wanga. Ndidzasankha mmodzi mwa ana a Davide kuti alamulire zidzukulu za Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Komatu ndidzawamvera chifundo ndi kuwakhazikanso pabwino.’ ”