1 Царств 15 – CARS & CCL

Священное Писание

1 Царств 15:1-35

Шаул должен истребить амаликитян

1Шемуил сказал Шаулу:

– Я тот, кого Вечный послал помазать тебя царём над народом Исраила. Выслушай же теперь слова Вечного. 2Так говорит Вечный, Повелитель Сил: «Я накажу амаликитян за то, что они сделали Исраилу, преградив путь исраильтянам, идущим из Египта. 3Ступай, напади на амаликитян и полностью уничтожь всё, что им принадлежит. Не щади их, предай смерти мужчин и женщин, детей и грудных младенцев, волов и овец, верблюдов и ослов».

4Шаул призвал народ и собрал их в Телаиме – двести тысяч пеших воинов и десять тысяч воинов из рода Иуды. 5Шаул подошёл к городу Амалика и устроил засаду в долине. 6Он сказал кенеям:

– Уходите, оставьте амаликитян, чтобы я не истребил вас вместе с ними, ведь вы оказали милость всем исраильтянам, когда они вышли из Египта15:6 См. Исх. 18:10-19..

И кенеи ушли от амаликитян. 7Шаул разбил амаликитян на всём пути от Хавилы до самого Сура, что в восточном Египте. 8Он взял Агага, царя амаликитян, живым, а весь его народ полностью истребил мечом. 9Но Шаул и его войско пощадили Агага. Они также оставили лучших овец и волов, жирных телят и ягнят – всё, что было ценно, они не хотели всё это уничтожать. Но всё слабое и плохое они уничтожили полностью.

Вечный отвергает Шаула

10Тогда к Шемуилу было слово Вечного:

11– Я жалею, что сделал Шаула царём, потому что он отвернулся от Меня и не выполнил Моих наставлений.

Шемуил разгневался на Шаула и всю ночь взывал к Вечному. 12Рано утром Шемуил встал, чтобы встретиться с Шаулом, но ему сказали:

– Шаул ушёл в город Кармил. Там он поставил себе памятник, а затем спустился в Гилгал.

13Когда Шемуил нагнал его, Шаул сказал:

– Да благословит тебя Вечный! Я выполнил наставления Вечного.

14Но Шемуил сказал:

– А почему же я тогда слышу блеяние овец и мычание волов?

15Шаул ответил:

– Воины привели их от амаликитян. Они пощадили лучших овец и волов, чтобы принести их в жертву Вечному, твоему Богу, но всё остальное мы полностью уничтожили.

16– Хватит, ни слова больше! – сказал Шаулу Шемуил. – Я скажу тебе то, что прошлой ночью сказал мне Вечный.

– Говори, – ответил Шаул.

17Шемуил сказал:

– Не стал ли ты главой родов Исраила, хотя сам когда-то невысоко себя ставил? Вечный помазал тебя царём над Исраилом. 18Вечный послал тебя с поручением, говоря: «Пойди и полностью истреби этот нечестивый народ – амаликитян. Веди с ними войну, пока не уничтожишь их». 19Почему ты не послушался Вечного? Почему ты бросился на добычу и совершил зло в глазах Вечного?

20– Но я же послушался Вечного, – сказал Шаул. – Я отправился исполнять поручение, которое дал мне Вечный. Я полностью истребил амаликитян и привёл их царя Агага. 21Воины взяли из добычи овец и волов, лучшее из подлежащего уничтожению, чтобы принести их в жертву Вечному, твоему Богу, в Гилгале.

22Но Шемуил ответил:

– Разве всесожжения и жертвы столь же приятны Вечному,

сколь послушание голосу Вечного?

Послушание лучше жертвы,

и повиновение лучше жира баранов.

23Ведь неповиновение подобно греху ворожбы,

и гордость – греху идолослужения.

Так как ты отверг слово Вечного,

то и Он отверг тебя как царя.

24Тогда Шаул сказал Шемуилу:

– Я согрешил. Я нарушил повеление Вечного и твои наставления. Я боялся народа и поэтому уступил им. 25Но теперь я молю тебя, прости мой грех и вернись со мной, чтобы мне поклониться Вечному.

26Но Шемуил сказал ему:

– Я не вернусь с тобой. Ты отверг слово Вечного, и Вечный отверг тебя как царя над Исраилом!

27Когда Шемуил повернулся, чтобы уйти, Шаул схватил его за край верхней одежды, и она порвалась. 28Шемуил сказал ему:

– Сегодня Вечный вырвал у тебя царство Исраила и отдал его другому – тому, кто лучше тебя. 29Верный Исраила не лжёт и не передумывает, ведь Он не человек, чтобы передумывать.

30Шаул ответил:

– Я согрешил. Но, пожалуйста, окажи мне уважение перед старейшинами моего народа и перед Исраилом, вернись со мной, тогда я смогу поклониться Вечному, твоему Богу.

31Шемуил вернулся с Шаулом, и Шаул поклонился Вечному. 32Тогда Шемуил сказал:

– Приведите ко мне Агага, царя амаликитян.

Агаг подошёл к нему уверенно, думая15:32 Или: «дрожа, но всё же думая».: «Конечно, горечь смерти прошла стороной». 33Но Шемуил сказал:

– Как меч твой лишал матерей их детей,

так твоя мать будет бездетной среди женщин.

И Шемуил рассёк Агага на части перед Вечным в Гилгале. 34Затем Шемуил ушёл в Раму, а Шаул поднялся к себе домой, в Гиву. 35До дня своей смерти Шемуил не виделся больше с Шаулом15:35 Шемуил сам никогда больше не искал встреч с Шаулом. Но он встречался с ним после (см. 19:24)., хотя и скорбел о нём. А Вечный сожалел, что сделал Шаула царём над Исраилом.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Samueli 15:1-35

Yehova Akana Sauli Kukhala Mfumu

1Samueli anawuza Sauli kuti, “Yehova anandituma ine kuti ndikudzozeni kukhala mfumu ya anthu ake, Aisraeli. Tsopano imvani zimene Yehova akunena. 2Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndidzalanga Aamaleki chifukwa cha zimene anawachita Aisraeli. Paja iwo analimbana ndi Aisraeli pa njira pamene Aisraeliwo ankachoka ku Igupto. 3Tsopano pita kathire nkhondo Aamaleki ndi kuwononga kwathunthu zinthu zonse zimene ali nazo. Musakasiyeko munthu ndi mmodzi yemwe. Mukaphe amuna ndi akazi, ana ndi makanda, ngʼombe ndi nkhosa, ngamira ndi abulu.’ ”

4Kotero Sauli anayitana ankhondo ake nawawerenga ku Telaimu. Ankhondo oyenda pansi analipo 200,000 ndipo mwa iwowa 10,000 anali a fuko la Yuda. 5Sauli anapita ku mzinda wa Aamaleki nawubisalira mʼkhwawa. 6Tsono Sauli anawuza Akeni kuti, “Samukani, muchoke pakati pa Aamaleki kuti ine ndisakuwonongeni pamodzi ndi iwo pakuti inu munaonetsa kukoma mtima kwa Aisraeli onse pamene ankatuluka mʼdziko la Igupto,” Choncho Akeni anachoka pakati pa Aamaleki.

7Tsono Sauli anakantha Aamaleki kuchokera ku Havila mpaka ku Suri, kummawa kwa Igupto. 8Sauli anatenga Agagi mfumu ya Aamaleki, koma anthu ake onse anawapha ndi lupanga. 9Koma Sauli ndi ankhondo ake sanaphe Agagi, sanaphenso nkhosa ndi ngʼombe zabwino ngakhalenso ana angʼombe ndi ana ankhosa onenepa. Chilichonse chimene chinali chabwino sanachiphe. Koma zonse zimene zinali zoyipa ndi zachabechabe anaziwononga.

10Kenaka Yehova anawuza Samueli kuti, 11“Ine ndikumva chisoni chifukwa ndinayika Sauli kukhala mfumu. Wabwerera mʼmbuyo, waleka kunditsata ndipo sanamvere malangizo anga.” Samueli anapsa mtima, ndipo analira kwa Yehova usiku wonse.

12Samueli anadzuka mmamawa ndipo anapita kukakumana ndi Sauli. Koma anthu anamuwuza kuti, “Sauli anabwera ku Karimeli, ndipo kumeneko wadziyimikira mwala wachikumbutso cha iye mwini. Tsopano wachokako ndipo wapita ku Giligala.”

13Samueli atamupeza Sauli, Sauliyo anati kwa Samueli, “Yehova akudalitseni! Ndachita zonse zimene Yehova analamula.”

14Koma Samueli anati, “Nanga bwanji ndikumva kulira kwa nkhosa ndi ngʼombe?”

15Sauli anayankha, “Zimenezi Asilikali azitenga kuchokera kwa Aamaleki. Iwo anasungako nkhosa ndi ngʼombe zabwino kuti akapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu, koma zina zonse anaziwononga.”

16Koma Samueli anati kwa Sauli, “Khala chete! Ima ndikuwuze zimene Yehova wandiwuza usiku wathawu.”

Sauli anayankha kuti, “Ndiwuzeni.”

17Apo Samueli anati, “Munali wamngʼono pa maso pa anthu, koma tsopano mwasanduka mtsogoleri wa mafuko a Israeli. Yehova anakudzozani kuti mukhale mfumu yolamulira Aisraeli. 18Ndipo Yehova anakutumani kuti, ‘Pitani mukawononge kwathunthu Aamaleki, anthu oyipa aja. Mukachite nawo nkhondo mpaka kuwatheratu.’ 19Chifukwa chiyani simunamvere mawu a Yehova? Chifukwa chiyani munathamangira zofunkha ndi kuchita choyipira Yehova?”

20Koma Saulo anawuza Samueli kuti, “Ine ndinamveradi mawu a Yehova. Ndinapita kukachita zimene Yehova anandituma. Ndinabwera naye Agagi, mfumu ya Amaleki, koma Aamaleki ena onse anaphedwa. 21Koma pa zofunkhazo anthu anatengapo nkhosa, ngʼombe ndi zabwino zina zoyenera kuwonongedwa kuti akapereke ngati nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala.”

22Koma Samueli anayankha kuti,

“Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina

kapena kumvera mawu a ake?

Taona, kumvera ndi kwabwino kuposa nsembe,

ndipo kutchera khutu ndi kwabwino kuposa kupereka mafuta a nkhosa.

23Pakuti kuwukira kuli ngati tchimo lowombeza,

ndipo kukhala nkhutukumve kuli ngati tchimo lopembedza mafano.

Chifukwa mwakana mawu a Yehova.

Iyenso wakukana kuti iweyo ukhale mfumu.”

24Tsono Sauli anati kwa Samueli, “Ine ndachimwa. Ndaphwanya malamulo a Yehova ndiponso malangizo anu. Ndinkaopa anthu ndipo ndinawamvera. 25Tsopano ndikukupemphani, khululukireni tchimo langa ndipo mubwerere nane kuti ndikapembedze Yehova.”

26Koma Samueli anawuza Sauli kuti, “Ine sindibwerera nawe. Inu mwakana mawu a Yehova. Choncho Iyenso wakukanani kuti musakhale mfumu yolamulira Aisraeli.”

27Samueli akutembenuka kuti azipita, Sauli anagwira mpendero wa mkanjo wake, ndipo unangʼambika. 28Samueli anati kwa iye, “Yehova wangʼamba ufumu wanu kuchoka kwa inu, ndipo waupereka kwa mnzanu woposa inu. 29Mulungu wa ulemerero wa Israeli sanama kapena kusintha maganizo ake; pakuti iye si munthu, kuti asinthe maganizo ake.”

30Sauli anati, “Ine ndachimwa. Komabe, chonde mundilemekeze pamaso pa akuluakulu, anthu anga, ndiponso pamaso pa Israeli. Mubwerere nane kuti ndikapembedze Yehova Mulungu wanu.” 31Pamenepo Samueli anabwerera ndi Sauli, ndipo Sauli anapembedza Yehova.

32Kenaka Samueli anati, “Bwera nayeni kuno Agagi, mfumu ya Amaleki ija.”

Choncho Agagi anapita kwa Samueli mokondwa chifukwa ankaganiza kuti, “Ndithu zowawa za imfa zapita.”

33Koma Samueli anati,

“Monga momwe lupanga lako linasandutsira amayi kukhala wopanda ana,

momwemonso amayi ako adzakhala opanda mwana pakati pa amayi.”

Ndipo Samueli anapha Agagi pamaso pa Yehova ku Giligala.

34Ndipo Samueli anapita ku Rama, koma Sauli anapita ku mudzi kwawo ku Gibeya wa Sauli. 35Samueli sanamuonenso Sauli mpaka imfa yake ngakhale kuti ankamulira Sauliyo. Yehova anamva chisoni kuti anasankha Sauli kuti akhale mfumu ya Israeli.