Забур 78 – CARS & CCL

Священное Писание

Забур 78:1-13

Песнь 78

Песнь Асафа.

1О Всевышний, чужие народы вторглись в Твой удел,

осквернили святой храм Твой

и превратили Иерусалим в развалины.

2Они отдали трупы Твоих рабов

на съедение небесным птицам,

тела верных Тебе – земным зверям.

3Они пролили кровь их, как воду,

вокруг всего Иерусалима,

и некому было похоронить их.

4Мы сделались посмешищем у наших соседей;

окружающие презирают и упрекают нас.

5Как долго, Вечный, Твой гнев будет длиться – бесконечно?

Как долго Твоя ревность будет пылать, как огонь?

6Пролей Свой гнев на народы, которые не знают Тебя,

и на царства, которые не призывают Твоего имени,

7потому что они истребили потомков Якуба

и землю их опустошили.

8Не вмени нам грехов наших предков;

пусть милость Твоя поспешит к нам навстречу,

потому что мы в полном отчаянии.

9Помоги нам, Всевышний, наш Спаситель,

ради славы имени Твоего.

Избавь нас и прости нам наши грехи

ради имени Твоего.

10Для чего народам говорить: «Где их Бог?»

Пусть станет известно между народами,

как отомстил Ты за пролитую кровь Твоего народа,

и пусть это увидят наши глаза.

11Пусть дойдёт до Тебя стенание узника;

сильной рукою Своею сохрани обречённых на смерть.

12Семикратно возврати нашим соседям их оскорбление,

которое они Тебе нанесли, о Владыка.

13А мы, народ Твой и овцы пастбищ Твоих,

вечно будем восхвалять Тебя

и возвещать о славе Твоей

из поколения в поколение.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 78:1-72

Salimo 78

Ndakatulo ya Asafu.

1Inu anthu anga imvani chiphunzitso changa;

mvetserani mawu a pakamwa panga.

2Ndidzatsekula pakamwa panga mʼmafanizo,

ndidzayankhula zinthu zobisika, zinthu zakalekale

3zimene tinazimva ndi kuzidziwa,

zimene makolo athu anatiwuza.

4Sitidzabisira ana awo,

tidzafotokozera mʼbado wotsatira

ntchito zotamandika za Yehova,

mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.

5Iye anapereka mawu wodzichitira umboni kwa Yakobo

ndi kukhazikitsa lamulo mu Israeli,

zimene analamulira makolo athu

kuphunzitsa ana awo,

6kotero kuti mʼbado wotsatira uthe kuzidziwa,

ngakhale ana amene sanabadwe,

ndi kuti iwo akafotokozere ana awonso.

7Choncho iwo adzakhulupirira Mulungu

ndipo sadzayiwala ntchito zake

koma adzasunga malamulo ake.

8Iwo asadzakhale monga makolo awo,

mʼbado wosamvera ndi wowukira,

umene mitima yake inali yosamvera Mulungu,

umene mizimu yake inali yosakhulupirika kwa Iye.

9Anthu a ku Efereimu, ngakhale ananyamula mauta,

anathawabe pa nthawi ya nkhondo;

10iwo sanasunge pangano la Mulungu

ndipo anakana kukhala mʼmoyo wotsatira lamulo lake.

11Anayiwala zimene Iye anachita,

zozizwitsa zimene anawaonetsa.

12Iyeyo anachita zodabwitsa makolo athu akuona,

mʼdziko la Igupto, mʼchigawo cha Zowani.

13Anagawa nyanja pakati ndi kudutsitsapo iwowo,

Iye anachititsa madzi kuyima chilili ngati khoma.

14Anawatsogolera ndi mtambo masana

ndi kuwala kwa moto usiku wonse.

15Iye anangʼamba miyala mʼchipululu

ndi kuwapatsa madzi ochuluka ngati a mʼnyanja zambiri;

16Anatulutsa mitsinje kuchokera mʼmingʼalu ya miyala

ndi kuyenda madzi ngati mitsinje.

17Komabe iwowo anapitiriza kumuchimwira Iye,

kuwukira Wammwambamwamba mʼchipululu.

18Ananyoza Mulungu mwadala

pomuwumiriza kuti awapatse chakudya chimene anachilakalaka.

19Iwo anayankhula motsutsana naye ponena kuti,

“Kodi Mulungu angatipatse chakudya mʼchipululu?

20Iye atamenya thanthwe

madzi anatuluka,

ndipo mitsinje inadzaza ndi madzi.

Koma iye angatipatsenso ife chakudya?

Kodi angapereke nyama kwa anthu akewa?”

21Yehova atawamva anakwiya kwambiri;

moto wake unayaka kutsutsana ndi Yakobo,

ndipo mkwiyo wake unauka kutsutsana ndi Israeli,

22pakuti iwo sanakhulupirire Mulungu

kapena kudalira chipulumutso chake.

23Komabe Iye anapereka lamulo kwa mitambo mmwamba

ndi kutsekula makomo a mayiko akumwamba;

24anagwetsa mana kuti anthu adye,

anawapatsa tirigu wakumwamba.

25Anthu anadya buledi wa angelo,

Iye anawatumizira chakudya chonse chimene akanatha kudya.

26Anamasula mphepo ya kummwera kuchokera kumwamba,

ndi kutsogolera mphepo ya kummwera mwa mphamvu zake.

27Iye anawagwetsera nyama ngati fumbi,

mbalame zowuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.

28Anazibweretsa kwa iwo mʼkati mwa misasa yawo,

kuzungulira matenti awo onse.

29Iwo anadya mpaka anatsala nazo zochuluka

pakuti Iye anawapatsa zimene anazilakalaka.

30Koma iwowo anasiya kudya chakudya anachilakalakacho,

chakudya chili mʼkamwa mwawobe,

31mkwiyo wa Mulungu unawayakira;

Iye anapha amphamvu onse pakati pawo,

kugwetsa anyamata abwino kwambiri mu Israeli.

32Ngakhale zinali chomwechi, iwo anapitirira kuchimwa;

ngakhale anaona zozizwitsa zakezo iwowo sanakhulupirirebe.

33Kotero Mulungu anachepetsa masiku awo kuti azimirire ngati mpweya.

Iye anachepetsa zaka zawo kuti zithere mʼmasautso.

34Mulungu atawapha, iwo amamufunafuna Iyeyo;

iwo ankatembenukiranso kwa Iye mwachangu.

35Ankakumbukira kuti Mulungu ndiye Thanthwe lawo,

kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye Mpulumutsi wawo.

36Komabe ankamuthyasika ndi pakamwa pawo,

kumunamiza ndi malilime awo;

37Mitima yawo sinali yokhazikika pa Iye,

iwo sanakhulupirike ku pangano lake.

38Komabe Iye anali wachifundo;

anakhululukira mphulupulu zawo

ndipo sanawawononge.

Nthawi ndi nthawi Iye anabweza mkwiyo wake

ndipo sanawutse ukali wake wonse.

39Iye anakumbukira kuti iwo anali anthu chabe,

mphepo yopita imene sibwereranso.

40Nthawi zambiri iwo ankamuwukira Iye mʼchipululu

ndi kumumvetsa chisoni mʼdziko lopanda kanthu!

41Kawirikawiri iwo ankamuyesa Mulungu;

ankamuputa Woyera wa Israeli.

42Sanakumbukire mphamvu zake,

tsiku limene Iye anawawombola kwa ozunza,

43tsiku limene Iyeyo anaonetsa poyera zizindikiro zozizwitsa zake mu Igupto,

zozizwitsa zake mʼchigawo cha Zowani.

44Iye anasandutsa mitsinje yawo kukhala magazi;

Iwo sanathe kumwa madzi ochokera mʼmitsinje yawo.

45Iye anawatumizira magulu a ntchentche zimene zinawawononga,

ndiponso achule amene anawasakaza.

46Iye anapereka mbewu zawo kwa ziwala,

zokolola zawo kwa dzombe.

47Iye anawononga mphesa zawo ndi matalala

ndiponso mitengo yawo yankhuyu ndi chisanu.

48Iye anapereka ngʼombe zawo ku matalala,

zoweta zawo ku zingʼaningʼani.

49Anakhuthula moto wa ukali wake pa iwo,

anawapsera mtima nawakwiyira nʼkuwabweretsera masautso.

Zimenezi zinali ngati gulu la angelo osakaza.

50Analolera kukwiya,

sanawapulumutse ku imfa

koma anawapereka ku mliri.

51Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto,

zipatso zoyamba kucha za mphamvu zawo mʼmatenti a Hamu

52Koma Iye anatulutsa anthu ake ngati ziweto;

anawatsogolera ngati nkhosa kudutsa mʼchipululu.

53Anawatsogolera bwinobwino kotero kuti analibe mantha

koma nyanja inamiza adani awo.

54Kotero anawafikitsa ku malire a dziko lake loyera,

ku dziko lamapiri limene dzanja lake lamanja linawatengera.

55Iye anathamangitsa mitundu ya anthu patsogolo pawo

ndipo anapereka mayiko awo kwa Aisraeli kuti akhale awo;

Iye anakhazikitsa mafuko a Israeli mʼnyumba zawo.

56Koma iwo anayesa Mulungu

ndi kuwukira Wammwambamwamba;

sanasunge malamulo ake.

57Anakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo awo,

anapotoka monga uta wosakhulupirika.

58Anakwiyitsa Iyeyo ndi malo awo opembedzera mafano;

anawutsa nsanje yake ndi mafano awo.

59Pamene Mulungu anamva zimenezi, anakwiya kwambiri;

Iye anakana Israeli kwathunthu.

60Anasiya nyumba ya ku Silo,

tenti imene Iyeyo anayimanga pakati pa anthu.

61Anatumiza mphamvu zake ku ukapolo,

ulemerero wake mʼmanja mwa adani.

62Anapereka anthu ake ku lupanga;

anakwiya kwambiri ndi cholowa chake.

63Moto unanyeketsa anyamata awo,

ndipo anamwali awo analibe nyimbo za ukwati;

64ansembe awo anaphedwa ndi lupanga,

ndipo amayi awo amasiye sanathe kulira.

65Kenaka Ambuye anakhala ngati akudzuka kutulo,

ngati munthu wamphamvu wofuwula chifukwa cha vinyo.

66Iye anathamangitsa adani ake;

anawachititsa manyazi ku nthawi zonse.

67Kenaka Iye anakana matenti a Yosefe,

sanasankhe fuko la Efereimu;

68Koma anasankha fuko la Yuda,

phiri la Ziyoni limene analikonda.

69Iye anamanga malo ake opatulika ngati zitunda,

dziko limene analikhazikitsa kwamuyaya.

70Anasankha Davide mtumiki wake

ndi kumuchotsa pakati pa makola ankhosa;

71kuchokera koyangʼanira nkhosa anamubweretsa

kuti akhale mʼbusa wa anthu ake, Yakobo,

wa Israeli cholowa chake.

72Ndipo Davide anawaweta ndi mtima wolungama;

ndi manja aluso anawatsogolera.