Klagesangene 2 – BPH & CCL

Bibelen på hverdagsdansk

Klagesangene 2:1-22

Guds dom over Jerusalem

1Ak, som en sort og truende tordensky lå Herrens vrede over Jerusalem.

Israels himmelske herlighed ligger knust i støvet.

End ikke Herrens eget tempel blev forskånet for hans vrede.

2Befolkningen i Juda blev nådesløst jaget fra hus og hjem.

Herren nedbrød i sin vrede hver eneste befæstet by.

Han ødelagde hele kongeriget til skam for dets ledere.

3Den samlede israelitiske hær blev løbet over ende.

Herren trak sin beskyttende hånd væk, da fjenden angreb.

Hans vrede hærgede landet som en fortærende ild.

4Eliten blandt landets ungdom blev dræbt.

Herren blev vores fjende og gjorde det af med os.

Han udgød sin vrede over Jerusalems indbyggere.

5Fjenderne viste sig at være sendt af Herren.

De ødelagde alle paladser og fæstninger i landet

og skabte sorg og smerte overalt i Juda.

6Grundlaget for at holde sabbat og højtid forsvandt,

da Herren nedrev sit tempel, som var det et skur.

Han forstødte i vrede både konger og præster.

7Han forkastede sit alter, forlod sit tempel,

lod fjenderne nedbryde palads og bymur.

De jublede i templet som på en højtidsdag.

8Intet i Jerusalem undgik ødelæggelsens svøbe.

Herren havde besluttet, at bymuren skulle falde.

Alle fæstningsværker og tårne blev lagt i ruiner.

9Jerusalems portslåer blev smadret og portene splintret.

Kongen og landets ledere blev ført bort til et fremmed land.

Toraen bliver glemt og profetisk åbenbaring er forbi.

10Klædt i sæk og med aske på hovedet

sidder de tilbageblevne ledere tavse på jorden.

De unge kvinder går nedbøjede omkring.

11Lidelsen er ikke til at bære, mine tårer er brugt op.

Mit hjerte er knust ved at se mit folks smerte.

Børn og spædbørn dør af sult midt på gaden.

12„Mad! Vand!” klager de små og besvimer.

De falder om som sårede soldater i byens gader.

Langsomt dør de i armene på deres mødre.

13Nøden og pinen i byen er ufattelig.

Åh, Jerusalem, din trøstesløse sorg er uden sidestykke.

Det er umuligt at lindre din grænseløse smerte.

14Ordene I hørte fra jeres såkaldte profeter, var falske.

Hvis de havde påtalt jeres synd i stedet for at lyve,

havde I måske kunnet undgå denne frygtelige skæbne.

15På vejen uden for byen går folk nu forbi og råber hånligt:

„Er det den by, man kaldte verdens skønneste?

Den skulle ellers have bragt glæde til hele jorden.”

16Raseriet står malet i deres ansigter, mens de håner dig:

„Endelig kom Jerusalem ned med nakken!

Det har vi set frem til meget længe.”

17Så fik Herren til sidst gjort alvor af sin trussel.

Han gennemførte uden skånsel den straf, han havde lovet.

Han gav fjenderne sejr og lod dem tage æren for det.

18Tårerne skal strømme som en flod dag og nat.

Græd øjnene ud af hovedet, Jerusalem, råb til Herren.

Lad selv dine nedbrudte mure hulke af gråd.

19Udgyd dine tårer for Herren natten igennem.

Løft hænderne og bønfald ham om at redde dine indbyggere,

som er ved at dø af sult i dine gader.

20„Vær nådig, Herre,” råber Jerusalem. „Stands denne frygtelige straf.

Skal mødre virkelig spise deres egne børn, som sad på deres skød?

Skal præster og profeter myrdes i dit hellige tempel?

21Yngre så vel som ældre ligger døde i gadens snavs.

Både unge mænd og piger blev hugget ned af sværdet.

Herre, du slog dem i din vrede og uden barmhjertighed.

22Ødelæggeren skabte rædsel overalt, så alle måtte smage din vrede.

Du inviterede mine fjender til at komme, som var det en festdag.

Fjenden dræbte alle mine kære, som var født og opvokset hos mig.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Maliro 2:1-22

1Haa, Ambuye waphimba mwana wamkazi wa Ziyoni

ndi mtambo wa mkwiyo wake!

Iye wataya pansi ulemerero wa Israeli

kuchoka kumwamba.

Pa tsiku la mkwiyo wake Iye sanakumbukirenso

popondapo mapazi ake.

2Ambuye anawononga midzi yonse ya Yakobo mopanda chifundo;

mu mkwiyo wake anagwetsa

malinga a mwana wamkazi wa Yuda.

Anagwetsa pansi mochititsa manyazi

maufumu ndi akalonga ake.

3Atakwiya kwambiri, Ambuye anathyola

nyanga iliyonse ya Israeli.

Anabweza dzanja lake lamanja

pamene mdani anamuyandikira.

Ambuye anatentha fuko la Yakobo ngati moto wonyeketsa

umene umawononga zinthu zonse zomwe zili pafupi.

4Wakokera uta wake pa ife ngati ndife adani;

wayimiritsa dzanja lake pa ife ngati ndife adani,

ndipo anapha onse amene tinkawayangʼana monyadira.

Ukali wake ukuyaka ngati moto

pa tenti ya mwana wamkazi wa Ziyoni.

5Ambuye ali ngati mdani;

wawonongeratu Israeli;

wawonongeratu nyumba zake zonse zaufumu

ndipo wawononga malinga ake.

Iye wachulukitsa kubuma ndi kulira

kwa mwana wamkazi wa Yuda.

6Wagwetsa malo ake okhalamo ngati khumbi la mʼmunda;

wawononga malo ake a msonkhano.

Yehova wayiwalitsa Ziyoni

maphwando ake oyikika ndi masabata ake.

Mokwiya kwambiri, Iye ananyoza

mfumu ndi wansembe.

7Ambuye wakana guwa lake la nsembe

ndipo wasiya malo ake opatulika.

Iye wapereka makoma a nyumba zake zaufumu

kwa mdani wake;

adaniwo anafuwula mʼnyumba ya Yehova

ngati kuti ndi pa tsiku la chikondwerero.

8Yehova anatsimikiza kugwetsa

makoma a mwana wamkazi wa Ziyoni.

Anawayesa ndi chingwe

ndipo sanafune kuleka kuwagwetsa.

Analiritsa malinga ndi makoma;

onse anawonongeka pamodzi.

9Zipata za Yerusalemu zalowa pansi;

wathyola ndi kuwononga mipiringidzo yake.

Mfumu ndi akalonga ake agwidwa ukapolo pakati pa mitundu ya anthu,

palibenso lamulo,

ndipo aneneri ake sakupeza

masomphenya kuchokera kwa Yehova.

10Akuluakulu a mwana wamkazi wa Ziyoni

akhala chete pansi;

awaza fumbi pa mitu yawo

ndipo avala ziguduli.

Anamwali a Yerusalemu

aweramitsa mitu yawo pansi.

11Maso anga atopa ndi kulira,

ndazunzika mʼmoyo mwanga,

mtima wanga wadzaza ndi chisoni

chifukwa anthu anga akuwonongeka,

chifukwa ana ndi makanda akukomoka

mʼmisewu ya mu mzinda.

12Anawo akufunsa amayi awo kuti,

“Kodi tirigu ndi vinyo zili kuti?”

pamene akukomoka ngati anthu olasidwa

mʼmisewu ya mʼmizinda,

pamene miyoyo yawo ikufowoka

mʼmanja mwa amayi awo.

13Ndinganene chiyani za iwe?

Ndingakufanizire ndi chiyani,

iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu?

Kodi ndingakufanizire ndi yani

kuti ndikutonthoze,

iwe namwali wa Ziyoni?

Chilonda chako ndi chozama ngati nyanja,

kodi ndani angakuchiritse?

14Masomphenya a aneneri ako

anali abodza ndi achabechabe.

Iwo sanakupulumutse kuti usapite ku ukapolo

poyika poyera mphulupulu zako.

Mauthenga amene anakupatsa

anali achabechabe ndi osocheretsa.

15Onse oyenda mʼnjira yako

akukuwombera mʼmanja;

akugwedeza mitu yawo ndi kukunyodola

iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu:

“Kodi mzinda uja ndi uwu umene unkatchedwa

wokongola kotheratu,

chimwemwe cha dziko lonse lapansi?”

16Adani ako onse akutsekulira pakamwa ndi kukunyoza;

iwo akunyogodola ndi kukukuta mano awo,

ndipo akuti, “Tamumeza.

Tsiku ili ndi lomwe timayembekezera;

tili ndi moyo kuti tilione.”

17Yehova wachita chimene anakonzeratu;

wakwaniritsa mawu ake,

amene anatsimikiza kale lomwe.

Wakuwononga mopanda chifundo,

walola mdani kuti akondwere chifukwa cha kugwa kwako,

wakweza mphamvu za adani ako.

18Mitima ya anthu

ikufuwulira Ambuye.

Iwe khoma la mwana wamkazi wa Ziyoni,

misozi yako itsike ngati mtsinje

usana ndi usiku;

usadzipatse wekha mpumulo,

maso ako asaleke kukhetsa misozi.

19Dzuka, fuwula usiku,

pamene alonda ayamba kulondera;

khuthula mtima wako ngati madzi

pamaso pa Ambuye.

Kweza manja ako kwa Iye

chifukwa cha miyoyo ya ana ako,

amene akukomoka ndi njala

mʼmisewu yonse ya mu mzinda.

20Inu Yehova, onani, ndipo ganizirani:

kodi ndani amene mwamuchitirapo zinthu ngati izi?

Kodi amayi adye ana awo,

amene amawasamalira?

Kodi ansembe ndi aneneri awaphere

mʼmalo opatulika a Ambuye?

21Anyamata ndi okalamba aligone pamodzi

pa fumbi la mʼmisewu ya mu mzinda;

anyamata anga ndi anamwali anga

aphedwa ndi lupanga.

Inu Yehova mwawapha pa tsiku la mkwiyo wanu;

mwawapha mopanda chifundo.

22Ngati momwe mumayitanira pa tsiku la phwando,

chimodzimodzinso mwandiyitanira zoopsa mbali zonse.

Pa tsiku limene Yehova wakwiya

palibe amene angathawe ndi kukhala ndi moyo;

mdani wanga wawononga

onse amene ndinkawasamala ndi kuwalera.