Dommerbogen 1 – BPH & CCL

Bibelen på hverdagsdansk

Dommerbogen 1:1-36

Juda og Simeon indtager deres område

1Efter Josvas død spurgte israelitterne Herren: „Hvem skal nu gå i spidsen i kampen mod kana’anæerne?”

2Herren svarede: „Judas stamme. Jeg vil hjælpe dem til at indtage det land, jeg har lovet dem.”

3Lederne af Judas stamme sagde til lederne af Simeons stamme: „Hjælp os med at besejre de kana’anæere, som bor i det område, der skal tilhøre os. Så hjælper vi bagefter jer med at indtage jeres område.” Så fulgte mændene fra Simeons stamme med Judas mænd.

4Da de angreb, gav Herren dem sejr over kana’anæerne og perizzitterne, så de dræbte 10.000 af fjendens krigere ved byen Bezek. 5Fjendens hær blev anført af kong Adonibezek, 6og det lykkedes ham at undslippe, men israelitterne fangede ham og huggede hans tommelfingre og storetæer af. 7„Jeg har selv behandlet 70 høvdinge på samme måde,” sagde kongen, „og jeg har ladet dem spise smulerne under mit bord. Nu gengælder Gud mig for, hvad jeg har gjort imod dem.” Derefter blev han ført til Jerusalem, hvor han blev til sin dødsdag.

8Judas mænd angreb også Jerusalem, huggede indbyggerne ned og satte ild til byen. 9Derefter rykkede de ud mod kana’anæerne i det sydlige højland, i Negev og på de vestlige bakkeskråninger. 10De gik til angreb på kana’anæerne i Hebron, det tidligere Kirjat-Arba, og besejrede Sheshajs, Ahimans og Talmajs mænd. 11De angreb også byen Debir, der tidligere hed Kirjat-Sefer. 12Kaleb havde forinden sagt: „Den, der indtager Kirjat-Sefer, får min datter Aksa til kone.” 13Otniel, der var søn af Kalebs yngre bror, Kenaz, erobrede byen og fik som belønning Aksa til kone.

14Efter brylluppet bad Aksa sin mand om tilladelse til at tage hjem til sin far og bede om et stykke agerjord. Da hun kom derhen og stod af sit æsel, spurgte Kaleb hende: „Hvad kan jeg gøre for dig?” 15„Velsign mig med en afskedsgave. Du har jo bortgiftet mig til det tørre sydland, så jeg har brug for nogle vandkilder.” Så gav Kaleb hende de øvre og de nedre kilder.

16Dengang Judas stamme drog op fra Palmernes By,1,16 Det vil sige Jeriko. fulgte efterkommerne af Moses’ svigerfar med dem. De hed kenitterne, og de slog sig ned blandt de øvrige beboere i Negevs ørken syd for Arad.

17Da Judas og Simeons mænd drog i kamp sammen, udryddede de kana’anæerne i Zefat og udslettede byen totalt. Derfor kaldes byen nu Horma.1,17 Horma betyder „udslettelse”. 18Judas hær indtog også byerne Gaza, Ashkalon og Ekron med de omkringliggende områder. 19Herren hjalp Judas stamme med at indtage højlandet, men de klarede ikke at få alle folkene i lavlandet drevet bort, fordi de havde stridsvogne af jern.

20Kaleb havde nu fået Hebron, som Moses i sin tid havde lovet ham, og han fik jaget de folk bort, som boede der. De var efterkommere af Anaks tre sønner.

De øvrige stammer fordriver ikke alle de oprindelige indbyggere

21Benjamins stamme fordrev ikke alle jebusitterne fra Jerusalem. Derfor bor jebusitterne stadig i byen sammen med benjaminitterne.

22-23Efraims og Manasses stammer angreb byen Betel, tidligere kaldet Luz, og Herren var med dem. De sendte først spioner af sted, 24som fangede en mand, der var på vej ud af byen. De sagde så til ham: „Hvis du viser os, hvordan vi kommer ind i byen, vil vi skåne dit liv.” 25Manden viste dem et smuthul, hvorefter hele byens befolkning blev hugget ned, med undtagelse af den mand og hans familie. 26Senere flyttede han til hittitternes land og grundlagde der en by, som han kaldte Luz.1,26 Opkaldt efter det gamle navn på hans hjemby. Det vides ikke, hvor denne by lå. Byen ligger der den dag i dag.

27Manasses stamme fordrev ikke alle indbyggerne i Bet-Shan, Ta’anak, Dor, Jibleam og Megiddo og landsbyerne deromkring, for kana’anæerne var fast besluttet på at blive boende. 28Senere, da israelitterne blev stærkere, gjorde de kana’anæerne til slaver, men de fik aldrig fordrevet dem fra landet. 29På samme måde gik det for Efraims stamme. Kana’anæerne blev boende side om side med dem i Gezer.

30Zebulons stamme udryddede heller ikke kana’anæerne i Kitron og Nahalol, men gjorde dem til slaver, 31og Ashers stamme fordrev ikke indbyggerne i Akko, Sidon, Ahlab, Akzib, Helba, Afik og Rehob. 32Kana’anæerne blev boende side om side med Ashers stamme. 33På samme måde gik det for Naftalis stamme: de fordrev ikke indbyggerne i Bet-Shemesh og Bet-Anat, men de gjorde dem til slaver.

34Amoritterne holdt stand mod Dans stamme, så de ikke kunne bosætte sig i lavlandet. 35Amoritterne blev også boende på Heresbjerget, i Ajjalon og i Sha’albim, men da Efraims og Manasses stammer blev stærkere, gjorde de dem til slaver. 36Amoritternes sydlige grænse løber fra Akrabbimpasset til Sela og videre opefter.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Oweruza 1:1-36

Aisraeli Achita Nkhondo ndi Akanaani Otsala

1Atamwalira Yoswa Aisraeli anafunsa Yehova kuti, “Ndani mwa ife ayambe nkhondo yomenyana ndi Akanaani?”

2Yehova anayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo liyambe kupita. Ndawapatsa dzikolo mʼmanja mwawo.”

3Choncho Ayuda anawuza abale awo a fuko la Simeoni kuti, “Bwerani tipitire limodzi mʼdziko limene tapatsidwa kuti tikamenyane ndi Akanaani. Ifenso tidzapita nanu mʼdziko limene anakugawirani.” Ndipo Asimeoni anapita nawo.

4Choncho Ayuda ananyamuka, ndipo Yehova anapereka Akanaani ndi Aperezi mʼmanja mwawo. Ndipo anapha anthu 10,000 ku Bezeki. 5Ku Bezekiko anakumana ndi ankhondo a mfumu Adoni-Bezeki ndipo anamenyana nawo, ndipo Ayudawo anagonjetsa Akanaani ndi Aperezi. 6Adoni-Bezekiyo anathawa, koma anamuthamangira ndi kumupeza, namugwira. Atamugwira anamudula zala zake zazikulu za ku manja ndi miyendo.

7Tsono Adoni-Bezeki anati, “Mafumu 70 omwe anadulidwa zala zazikulu za ku manja ndi miyendo yawo ankatola nyenyeswa pansi pa tebulo langa. Mulungu tsopano wandibwezera zomwe ndinawachita.” Kenaka anapita naye ku Yerusalemu ndipo anafera komweko.

8Pambuyo pake Ayuda anakathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu ndipo anawulanda. Anapha anthu ambiri ndi kutentha mzinda wonse.

9Kenaka Ayuda anapita kukamenyana ndi Akanaani omwe amakhala ku dziko la ku mapiri, dziko la Negevi kummwera ndiponso mu zigwa. 10Anakalimbananso ndi Akanaani amene ankakhala ku Hebroni (mzinda womwe kale unkatchedwa Kiriyati-Araba). Kumeneko anagonjetsa Sesai, Ahimani ndi Talimai.

11Kuchokera kumeneko, iwo anakathira nkhondo anthu amene ankakhala ku Debri (mzindawu poyamba unkatchedwa Kiriati Seferi). 12Tsono Kalebe anati, “Munthu amene angathire nkhondo mzinda wa Kiriati Seferi ndi kuwulanda, ndidzamupatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.” 13Otanieli mwana wa Kenazi, mngʼono wake wa Kalebe, ndiye anawulanda. Choncho Kalebe anamupatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake.

14Tsiku lina atafika Akisayo, Otanieli anamuwumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe abambo ake. Pamene Akisa anatsika pa bulu wake, Kalebe anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna ndikuchitire chiyani?”

15Iye anayankha kuti, “Mundikomere mtima. Popeza mwandipatsa ku Negevi, kumalo kumene kulibe madzi, mundipatsenso akasupe amadzi.” Choncho Kalebe anamupatsa akasupe a kumtunda ndi a kumunsi.

16Tsono zidzukulu za Hobabu, Mkeni uja, mpongozi wa Mose, zinachoka ku Yeriko mzinda wa migwalangwa pamodzi ndi anthu a fuko la Yuda mpaka ku chipululu chimene chili kummwera kwa Aradi ndi kukakhala ndi Aamaleki.

17Kenaka anthu a fuko la Yuda anapita pamodzi ndi abale awo a fuko la Simeoni ndi kukagonjetsa Akanaani amene amakhala ku Zefati, ndipo mzindawo anawuwononga kwambiri. Choncho mzindawo anawutcha Horima. 18Anthu a fuko la Yuda analandanso mzinda wa Gaza ndi dziko lonse lozungulira, mzinda wa Asikeloni pamodzi ndi dziko lake lonse lozungulira, ndi mzinda wa Ekroni pamodzi ndi dziko lonse lozungulira.

19Yehova anathandiza anthu a fuko la Yuda. Iwo analanda dziko la kumapiri, koma sanathe kuwachotsa anthu ku zigwa, chifukwa anali ndi magaleta azitsulo. 20Monga analonjezera Mose, Kalebe anapatsidwa Hebroni. Kalebe anapirikitsa mafuko atatu a Anaki mu mzindamo. 21Koma fuko la Benjamini linalephera kuwachotsa Ayebusi, amene amakhala mu Yerusalemu. Choncho Ayebusiwo akukhalabe ndi fuko la Benjamini mu Yerusalemu mpaka lero.

22A banja la Yosefe nawonso anathira nkhondo mzinda wa Beteli, ndipo Yehova anali nawo. 23Anatumiza anthu kuti akazonde Beteli. Mzindawo kale unkatchedwa Luzi. 24Anthu okazondawo anaona munthu akutuluka mu mzindamo ndipo anamuwuza kuti, “Tisonyeze njira yolowera mu mzindamu, ndipo ife tidzakuchitira chifundo.” 25Choncho iye anawaonetsa njirayo, ndipo iwo anapha anthu onse mu mzindamo ndi lupanga koma munthu uja pamodzi ndi banja lake sanawaphe. 26Ndipo iye anapita ku dziko la Ahiti, kumene anamangako mzinda nawutcha dzina lake Luzi. Mpaka lero lino mzindawo dzina lake ndi lomwelo.

27Koma a fuko la Manase sanachotse nzika za mzinda wa Beti-Seani pamodzi ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapena nzika za mzinda wa Taanaki ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapenanso nzika za mzinda wa Dori ndi mʼmidzi yake yozungulira. Iwo sanapirikitse nzika za mzinda wa Ibuleamu ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapena mzinda wa Megido ndi mʼmidzi yake yozungulira. Choncho Akanaani anapitirirabe kukhala mʼdzikomo. 28Aisraeli atakhala amphamvu, anawagwiritsa Akanaaniwo ntchito yakalavulagaga, koma sanawapirikitse. 29Nawonso Aefereimu sanathamangitse Akanaani amene amakhala mu Gezeri, choncho Akanaaniwo ankakhalabe pakati pawo ku Gezeriko. 30Azebuloni sanathamangitse Akanaani amene amakhala mu Kitironi kapena a ku Nahaloli. Iwo ankakhala pakati pawo ndipo ankawagwiritsa ntchito yakalavulagaga. 31A fuko la Aseri nawo sanathamangitse amene amakhala mu Ako, Sidoni, Ahilabu, Akizibu, Heliba, Afiki, ndi Rehobu. 32Choncho anthu a fuko la Aseri anakhala pakati pa Akanaani amene ankakhala mʼdzikomo popeza sanawapirikitse. 33Nalonso fuko la Nafutali silinathamangitse anthu amene ankakhala ku Beti Semesi kapena ku Beti Anati. Koma Anafutaliwo ankakhala pakati pa Akanaaniwo mʼdzikomo. Koma anthu amene ankakhala ku Beti Semesi ndi ku Beti Anati anawasandutsa kukhala ogwira ntchito yathangata. 34Aamori anapirikitsira anthu a fuko la Dani ku dziko la ku mapiri popeza sanawalole kuti atsikire ku chigwa. 35Aamori anatsimikiza mtima zokhalabe ku phiri la Hara-Heresi, ku Ayaloni, ndiponso ku Saalibimu. Koma a fuko la Yosefe anakula mphamvu ndipo anagwiritsa Aamoriwo ntchito yakalavulagaga. 36Malire a Aamori anayambira ku chikweza cha Akirabimu nʼkulowera ku Sela napitirira kumapita chakumapiri ndithu.