Numero 1 – APSD-CEB & CCL

Ang Pulong Sa Dios

Numero 1:1-54

Ang Unang Pagsensos sa Israel

1Sa unang adlaw, sa ikaduhang bulan, sa ikaduhang tuig human mibiya ang mga Israelinhon gikan sa Ehipto, nakigsulti ang Ginoo kang Moises didto sa Tolda nga Tagboanan1:1 Tolda nga Tagboanan: nga mao usab ang Tolda nga Simbahan. Tan-awa ang Lista sa mga Pulong sa luyo. sa kamingawan sa Sinai. Miingon siya, 2“Esensus ninyo ang tibuok katilingban sa Israel sumala sa ilang mga tribo ug pamilya. Ilista ang mga ngalan sa tanang mga lalaki 3nga nagaedad ug 20 ka tuig pataas, nga may katakos sa pagpakiggira. Kamo ni Aaron ang mangunay sa pag-ihap sa matag tribo. 4Motabang kaninyo ang matag pangulo sa matag tribo.” 5-15Mao kini ang mga pangulo sa matag tribo nga motabang kaninyo:

Ngalan sa Pangulo Ngalan sa TriboElizur nga anak ni Shedeur ReubenShelumiel nga anak ni Zurishadai SimeonNashon nga anak ni Aminadab JudaNetanel nga anak ni Zuar IsacarEliab nga anak ni Helon ZebulunElishama nga anak ni Amihud Efraim nga anak ni JoseGamaliel nga anak ni Pedazur Manase nga anak ni JoseAbidan nga anak ni Gideoni BenjaminAhiezer nga anak ni Amishadai DanPagiel nga anak ni Ocran AsherEliasaf nga anak ni Deuel GadAhira nga anak ni Enan Naftali

16Mao kini sila ang mga pangulo sa matag tribo nga napili gikan sa katilingban sa Israel.

17-18Gipatigom ni Moises ug ni Aaron kauban niining mga pangulo ang tibuok katilingban niana mismong adlawa. Gipanglista nila ang tanang mga lalaki nga nagaedad ug 20 ka tuig pataas, sumala sa ilang mga tribo ug pamilya. 19Gihimo ni Moises kining pagpanglista didto sa kamingawan sa Sinai, sumala sa gisugo sa Ginoo kaniya.

20-43Mao kini ang gidaghanon sa mga lalaki nga nagaedad ug 20 ka tuig pataas, nga may katakos sa pagpakiggira, nga nalista sumala sa tribo ug pamilya:

Ngalan sa Tribo GidaghanonReuben nga kamagulangang anak ni Jacob1:20-43 Jacob: sa Hebreo, Israel.46,500Simeon 59,300Gad 45,650Juda 74,600Isacar 54,400Zebulun 57,400Efraim (nga anak ni Jose) 40,500Manase (nga anak ni Jose) 32,200Benjamin 35,400Dan 62,700Asher 41,500Naftali 53,400

44Mao kini ang gidaghanon sa mga lalaki nga naihap ni Moises ug ni Aaron ug sa 12 ka mga pangulo sa Israel. 45Ang kada usa kanila nalista sumala sa ilang pamilya. Nagaedad silag 20 ka tuig pataas, nga may katakos sa pagpakiggira. 46Sa kinatibuk-an, mikabat ug 603,550 ang ilang gidaghanon. 47Wala iapil niini ang mga kaliwat ni Levi. 48Kay miingon ang Ginoo kang Moises, 49“Ayaw iapil ang tribo ni Levi sa pag-ihap uban sa mga Israelinhon. 50Ihatag kanila ang responsibilidad sa pag-atiman sa Tolda nga Simbahan diin nahimutang ang Kasugoan ug ang tanang mga kagamitan niini. Sila ang modala sa Tolda ug sa tanang kagamitan niini. Kinahanglang atimanon nila ang Tolda ug magkampo sila libot niini. 51Kon ibalhin ang Tolda, sila ang mohipos niini ug mopatindog pagbalik. Si bisan kinsa nga dili kaliwat ni Levi nga moduol sa Tolda, pagapatyon. 52Magkampo ang matag tribo sa Israel sa dapit nga gitagana kanila ug magbutang ug ilang bandera. 53Apan ang mga kaliwat ni Levi kinahanglan magkampo libot sa Tolda diin nahimutang ang Kasugoan, aron dili ako masuko sa tibuok katilingban sa Israel. Ang mga kaliwat ni Levi mao ang responsable sa pag-atiman sa Tolda.”

54Gihimo sa mga Israelinhon ang tanan sumala sa gisugo sa Ginoo kang Moises.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 1:1-54

Kalembera

1Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai, mu tenti ya msonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, mʼchaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, kuti, 2“Werengani Aisraeli onse mʼmafuko awo ndi mʼmabanja awo, lemba dzina la munthu wamwamuna aliyense, mmodzimmodzi. 3Iwe ndi Aaroni mwawerenge mwa magulu awo mu Israeli, amuna onse a zaka makumi awiri zakubadwa ndi opitirirapo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali. 4Munthu mmodzi wochokera ku fuko lililonse yemwe ndi mtsogoleri wa banja lake, ndiye akuthandizeni pa ntchitoyi. 5Mayina a anthu amene akuthandizeniwo ndi awa:

Elizuri mwana wa Sedeuri, kuchokera ku fuko la Rubeni,

6Selumieli mwana wa Zurisadai, kuchokera ku fuko la Simeoni,

7Naasoni mwana wa Aminadabu, kuchokera ku fuko la Yuda,

8Netanieli mwana wa Zuwara, kuchokera ku fuko la Isakara,

9Eliabu mwana wa Heloni, kuchokera ku fuko la Zebuloni,

10Mwa ana a Yosefe:

kuchokera ku fuko la Efereimu, Elisama mwana wa Amihudi;

kuchokera ku fuko la Manase, Gamalieli mwana wa Pedazuri;

11Abidani mwana wa Gideoni, kuchokera ku fuko la Benjamini,

12Ahiyezeri mwana wa Amisadai, kuchokera ku fuko la Dani,

13Pagieli mwana wa Okirani, kuchokera ku fuko la Aseri,

14Eliyasafu mwana wa Deuweli, kuchokera ku fuko la Gadi,

15Ahira mwana wa Enani, kuchokera ku fuko la Nafutali.”

16Amenewa ndi anthu amene anasankhidwa kuchokera mʼmagulu mwawo, eni mbumba a mafuko a makolo awo. Iwowa anali atsogoleri a mafuko a Israeli.

17Mose ndi Aaroni anatenga anthu amene mayina awo anaperekedwa, 18ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, anasonkhanitsa anthu onse pamodzi. Anthuwo anafotokoza za makolo awo mwa mafuko awo ndi mabanja awo. Ndipo mayina a amuna onse amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo analembedwa, mmodzimmodzi 19monga momwe Yehova analamulira Mose. Motero iyeyo anawawerenga mʼchipululu cha Sinai:

20Kuchokera mwa ana a Rubeni, mwana wamwamuna woyamba wa Israeli:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali, anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 21Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Rubeni chinali 46,500.

22Kuchokera mwa zidzukulu za Simeoni:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 23Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Simeoni chinali 59,300.

24Kuchokera mwa zidzukulu za Gadi:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 25Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Gadi chinali 45, 650.

26Kuchokera mwa zidzukulu za Yuda:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 27Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Yuda chinali 74, 600.

28Kuchokera mwa zidzukulu za Isakara:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 29Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Isakara chinali 54,400.

30Kuchokera mwa zidzukulu za Zebuloni:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 31Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Zebuloni chinali 57,400.

32Kuchokera mwa ana aamuna a Yosefe:

Kuchokera mwa zidzukulu za Efereimu:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 33Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Efereimu chinali 40,500.

34Kuchokera mwa zidzukulu za Manase:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 35Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Manase chinali 32,200.

36Kuchokera mwa zidzukulu za Benjamini:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 37Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Benjamini chinali 35,400.

38Kuchokera mwa zidzukulu za Dani:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 39Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Dani chinali 62,700.

40Kuchokera mwa zidzukulu za Aseri:

Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 41Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Aseri chinali 41,500.

42Kuchokera mwa zidzukulu za Nafutali:

Aamuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 43Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Nafutali chinali 53,400.

44Amenewa ndiwo anthu amene Mose ndi Aaroni anawawerenga mothandizidwa ndi atsogoleri khumi ndi awiri a Israeli, aliyense kuyimira fuko lake. 45Aisraeli onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli anawawerenga monga mwa mabanja awo. 46Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 603,550.

47Koma mabanja a fuko la Levi okha sanawawerenge pamodzi ndi ena. 48Pakuti Yehova anawuza Mose kuti, 49“Usawerenge fuko la Levi kapena kuliphatikiza mʼkawundula wa Aisraeli. 50Koma uyike Aleviwo kuti aziyangʼanira tenti yanga yopatulika, zipangizo zake ndi zonse zili mʼmenemo. Azinyamula tentiyo pamodzi ndi zipangizo zake zonse; azisamalira ndi kumanga misasa mozungulira tentiyo. 51Pamene akusamutsa tentiyo, Alevi ndiwo aziyitsitsa, akafuna kuyimanganso, Alevi ndiwo aziyimiritsa. Wina aliyense amene adzayandikire tentiyo adzaphedwa. 52Aisraeli azimanga matenti awo mʼmagulumagulu, munthu aliyense ku gulu lake pansi pa mbendera yake. 53Alevi nawonso, azimanga matenti awo mozungulira tenti yopatulika kuti chilango chisagwere Aisraeli onse. Ndipo Alevi aziyangʼanira ndi kusamalira tenti yopatulikayo.”

54Choncho Aisraeli anachita monga Yehova analamulira Mose.