Yesaia 53 – AKCB & CCL

Akuapem Twi Contemporary Bible

Yesaia 53:1-12

1Hena na wagye yɛn asɛm no adi?

na Awurade abasa no, hena so na ada adi?

2Onyin wɔ nʼanim te sɛ dua amono ketewa bi,

te sɛ ntin a efi asase wosee mu.

Onni ahoɔfɛ anaa anuonyam a ɛbɛtwetwe yɛn akɔ ne nkyɛn.

Ne tebea mu nni biribiara a ɛbɛma yɛapɛ no.

3Nnipa bɔɔ no ahohora na wɔpoo no,

Ɔwerɛhowni a onim ɔyaw.

Te sɛ obi a nnipa de wɔn anim hintaw no

wobuu no animtiaa na yɛammu no.

4Ampa ara ɔfaa yɛn mmerɛwyɛ,

na ɔsoaa yɛn awerɛhow,

nanso yebuu no sɛ Onyankopɔn na watwe nʼaso.

Yebuu no sɛ, Onyankopɔn na wabɔ no na wadwerɛw no.

5Nanso yɛn mmarato nti na wopiraa no,

yɛn amumɔyɛ nti na wɔdwerɛw no;

asotwe a ɛde asomdwoe brɛɛ yɛn no daa no so,

na nʼapirakuru mu na yenya ayaresa.

6Yɛn nyinaa ayerayera te sɛ nguan,

yɛn mu biara afa ne kwan;

na Awurade de yɛn nyinaa

amumɔyɛ ato no so.

7Wɔhyɛɛ no so, yɛɛ no ayayade,

nanso wammue nʼano;

wɔde no kɔɔ te sɛ oguamma a wɔrekokum no.

Sɛnea oguamma yɛ komm wɔ ne nwitwitwafo anim no,

saa ara na wammue nʼano.

8Wɔnam nhyɛso ne atemmu so faa no kɔe.

Na hena na obetumi aka nʼasefo ho asɛm?

Efisɛ woyii no fii asase yi so;

me nkurɔfo mmarato nti wɔtwee nʼaso.

9Wɔyɛɛ ne da wɔ abɔnefo mu,

na ne wu mu wɔde no too adefo mu

ɛwɔ mu, wanyɛ akakabensɛm biara,

na obiara ante atosɛm biara amfi nʼano.

10Nanso ɛyɛɛ Awurade pɛ sɛ ɔbɛdwerɛw no ama no ahu amane

mpo ɔde ne nkwa yɛ afɔdi afɔrebɔde,

obehu nʼasefo na ne nna bɛware,

na Awurade pɛ bɛkɔ so wɔ ne nsam.

11Ne kra amanehunu akyi,

obehu nkwa hann, na ne koma atɔ ne yam;

na ne suahu mu me somfo treneeni no bebu bebree bem,

na wasoa wɔn amumɔyɛ.

12Enti mɛma no kyɛfa wɔ atitiriw mu,

na ɔne ahoɔdenfo bɛkyɛ asade

efisɛ ɔde ne nkwa too hɔ maa owu,

na wɔkan no fraa mmaratofo.

Ɔsoaa nnipa bebree bɔne,

na odi maa mmaratofo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 53:1-12

1Ndani wakhulupirira zimene tanenazi;

kapena ndani amene Yehova wamuzindikiritsa mphamvu zake?

2Iye anakula ngati mphukira pamaso pake,

ndiponso ngati muzu mʼnthaka yowuma.

Iye analibe thupi labwino kapena nkhope yokongola yoti ife nʼkumamuchewukira,

analibe maonekedwe woti ife nʼkumamukhumbira.

3Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu,

munthu amene moyo wake unali wamasautso, wozolowera zowawa,

ndipo anali ngati munthu amene anzake amaphimba nkhope zawo akamuona.

Iye ananyozedwa, ndipo ife sitinamuyese kanthu.

4Ndithudi, iye anamva zowawa mʼmalo mwa ife;

ndipo anasautsidwa mʼmalo mwathu.

Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumulanga,

kumukantha ndi kumusautsa.

5Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu,

ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu;

iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere,

ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa.

6Ife tonse, ngati nkhosa, tasochera,

aliyense mwa ife akungodziyendera;

ndipo Yehova wamusenzetsa

zoyipa zathu zonse.

7Anthu anamuzunza ndi kumusautsa,

koma sanayankhule kanthu.

Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira,

kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta,

momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.

8Atatha kumugwira mwankhanza ndikumuyimba mlandu, kenaka anapita naye kukamupha.

Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake,

poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo?

Ndani anaganizirapo poona kuti iye anakanthidwa chifukwa cha zolakwa za anthu anga?

9Anamukonzera manda ake pamodzi ndi anthu oyipa

ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi anthu achuma,

ngakhale kuti iye sanachite za chiwawa,

kapena kuyankhula za chinyengo.

10Komatu ndi Yehova amene anafuna kuti amuzunze ndi kumusautsa.

Yehova anapereka moyo wa mtumiki wake kuti ukhale nsembe yoperekedwa chifukwa cha zolakwa.

Tsono iye adzaona zidzukulu zake ndipo adzakhala ndi moyo wautali,

ndipo chifuniro cha Yehova chidzachitika mwa iye.

11Atatha mazunzo a moyo wake,

adzaona kuwala, ndipo adzakhutira.

Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzalungamitsa anthu ambiri,

popeza adzasenza zolakwa zawo.

12Motero Ine ndidzamupatsa ulemu pamodzi ndi akuluakulu,

adzagawana zofunkha ndi ankhondo amphamvu,

popeza anapereka moyo wake mpaka kufa,

ndipo anamuyika mʼgulu la anthu olakwa kuti akhululukidwe.

Pakuti iye anasenza machimo a anthu ambiri,

ndipo anawapempherera anthu olakwa.