Yeremia 44 – AKCB & CCL

Akuapem Twi Contemporary Bible

Yeremia 44:1-30

Abosonsom Mu Amanehunu

1Saa asɛm yi baa Yeremia nkyɛn; ɛfa Yudafo a wɔtete Misraim anafo fam wɔ Migdol, Tapanhes, Memfis ne Misraim atifi fam no ho. 2“Sɛɛ na Asafo Awurade, Israel Nyankopɔn, se: Muhuu amanehunu kɛse a mede baa Yerusalem ne Yuda nkurow nyinaa so no. Nnɛ wɔayeyɛ amamfo na wɔasɛesɛe 3esiane bɔne a wɔayɛ no nti. Wɔhyew nnuhuam, som anyame foforo a, wɔn anaa mo anaa mo agyanom nnim wɔn de hyɛɛ me abufuw. 4Mesomaa mʼasomfo adiyifo mpɛn pii a wɔkae se, ‘Monnyɛ saa atantanne a mikyi no!’ 5Nanso wɔantie, wɔamfa anyɛ asɛm, na wɔannan amfi wɔn amumɔyɛsɛm no ho na wɔannyae hyew a wɔhyew nnuhuam ma anyame foforo no. 6Enti mihwiee mʼabufuw gui, na ɛdɛw kɔɔ Yuda nkurow ne Yerusalem mmɔnten so ma ɛsɛesɛe na ɛdedaa mpan sɛnea ɛtete nnɛ yi.

7“Na mprempren, nea Asafo Awurade Nyankopɔn, Israel Nyankopɔn se ni: Adɛn nti na mode amanehunu kɛse aba mo ho so, sɛ muyii mmarima ne mmea, mmofra ne mmotafowa fii Yuda a moannyaw nkae biara amma mo ho. 8Adɛn nti na mode nea mo nsa ayɛ hyɛ me abufuw, na mohyew nnuhuam ma anyame foforo wɔ Misraim, baabi a moabɛtena hɔ no? Mobɛsɛe mo ho, na moayɛ nnome ne nsopa wɔ asase so amanaman nyinaa mu. 9Mo werɛ afi amumɔyɛsɛm a mo agyanom, Yuda ahemfo ne ahemmea yɛe, na mo ne mo yerenom nso yɛɛ wɔ Yuda asase ne Yerusalem mmɔnten so no ana? 10Ebesi nnɛ yi, wɔmmrɛɛ wɔn ho ase, wɔnnaa nidi adi na wonnii me mmara ne ahyɛde a mede maa mo ne mo agyanom no so.

11“Enti nea Asafo Awurade, Israel Nyankopɔn, se ni: Masi mʼadwene pi sɛ mede amanehunu bɛba mo so na masɛe Yuda nyinaa. 12Mɛfa Yuda nkae a wosii wɔn adwene pi sɛ wɔbɛkɔ Misraim akɔtena hɔ no. Wɔn nyinaa bewuwu wɔ Misraim; wɔbɛtotɔ wɔ afoa ano anaa ɔkɔm bekum wɔn. Efi akumaa so kosi ɔkɛse so, afoa ne ɔkɔm bekunkum wɔn. Wɔbɛyɛ nnome, ahodwiriwde, afɔbude ne ahohora. 13Mede afoa, ɔkɔm ne ɔyaredɔm bɛtwe wɔn a wɔtete Misraim no aso, sɛnea metwee Yerusalem aso no. 14Yuda nkae a wɔakɔtena Misraim no mu biara renguan, na wɔremfa wɔn ho nni na wɔasan aba Yuda, asase a wɔpɛ sɛ wɔsan bɛtena so no so; wɔn mu biara remma, gye aguanfo kakraa bi.”

15Afei mmarima a na wonim sɛ wɔn yerenom hyew nnuhuam ma anyame foforo, wɔne mmea a wɔwɔ hɔ no nyinaa, nnipadɔm no, ne nnipa a wɔwɔ Misraim Atifi fam ne Anafo fam ka kyerɛɛ Yeremia se, 16“Yɛrentie asɛm a waka akyerɛ yɛn wɔ Awurade din mu no! 17Ampa ara yɛbɛyɛ biribiara a yɛkae se yɛbɛyɛ: Yɛbɛhyew nnuhuam ama Ɔsoro Hemmea na yɛahwie ahwiesa ama no, sɛnea yɛne yɛn agyanom, ahemfo ne adwumayɛfo yɛɛ wɔ Yuda nkurow ne Yerusalem mmɔnten so no pɛpɛɛpɛ. Saa bere no na yɛwɔ aduan, na yedi yiye a yenni ɔhaw biara nso. 18Nanso efi bere a yegyaee nnuhuam a yɛhyew ma Ɔsoro Hemmea, na yegyaee ahwiesa a yɛde ma no no, biribiara abɔ yɛn na yɛrewuwu wɔ afoa ne ɔkɔm ano.”

19Na mmea no ka kaa ho se, “Bere a yɛhyew nnuhuam maa44.19 mmea—Esiane sɛ na Ɔsoro Hemmea no yɛ Babilonia bosom a ɔma awo no nti, na mmea di ne som no mu akoten. Ɔsoro Hemmea, na yehwiee ahwiesa maa no no, na yɛn kununom nnim sɛ yɛto ɔfam a ɛyɛ ne sɛso, hwie ahwiesa ma no ana?”

20Na Yeremia ka kyerɛɛ nnipa no nyinaa; mmarima ne mmea a wɔrebua no no se, 21“Mususuw sɛ, Awurade nnim sɛ, na mo ne mo agyanom, mo ahemfo, adwumayɛfo ne ɔmanfo no hyew nnuhuam ma ahoni wɔ Yuda nkurow so ne Yerusalem mmɔnten so ana? 22Bere a mo amumɔyɛ ne akyiwade a moyɛɛ no fonoo Awurade no, mo asase dannan nnomede ne amamfo a obiara nte so, sɛnea ɛte nnɛ yi. 23Esiane sɛ moahyew nnuhuam, ayɛ bɔne atia Awurade, na moanyɛ osetie amma no, na moanni ne mmara, nʼahyɛde ne nʼadansesɛm so nti, amanehunu aba mo so sɛnea muhu yi.”

24Afei Yeremia ka kyerɛɛ nnipa no nyinaa a mmea no ka ho se, “Mo Yudafo a mowɔ Misraim nyinaa muntie Awurade asɛm. 25Sɛɛ na Asafo Awurade, Israel Nyankopɔn, se: Mo ne mo yerenom de mo nneyɛe akyerɛ mo bɔ a mohyɛe se, ‘Ampa ara yebedi bɔ a yɛhyɛe sɛ, yɛbɛhyew nnuhuam ahwie ahwiesa ama Ɔsoro Hemmea no,’ no so.”

Monkɔ so, munni mo bɔhyɛ ne mo ntam so! 26Nanso muntie Awurade asɛm, mo Yudafo a mowɔ Misraim nyinaa. Mede me din kɛse no ka ntam se, nea Awurade se ni, obiara a ofi Yuda a ɔte Misraim asase so baabiara remmɔ me din nka ntam bio da se, “Sɛ Otumfo Awurade te ase yi.” 27Na mɛhwɛ ama wɔahu amane na ɛnyɛ yiyedi; Yudafo a wɔwɔ Misraim bewuwu wɔ afoa ne ɔkɔm ano kosi sɛ wɔbɛsɛe wɔn nyinaa. 28Wɔn a wobeguan afi afoa ano na wɔasan afi Misraim akɔ Yuda asase so no bɛyɛ kakraa bi. Afei Yuda nkae a wɔbɛtenaa Misraim no nyinaa behu nea nʼasɛm yɛ nokware; me de anaa wɔn de.

29“ ‘Eyi na ɛbɛyɛ nsɛnkyerɛnne ama mo sɛ mɛtwe mo aso wɔ ha, na moahu sɛ ampa ara mʼahunahuna a ɛfa ɔhaw ho no bɛba mu,’ Awurade na ose. 30‘Mede Misraimhene Farao Hofra rebɛhyɛ nʼatamfo a wɔpɛ sɛ wokum no no nsa, sɛnea mede Yudahene Sedekia hyɛɛ Babiloniahene Nebukadnessar, ne tamfo a na ɔrehwehwɛ no akum no no nsa. Sɛɛ na Awurade se.’ ”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 44:1-30

Masautso Chifukwa cha Kupembedza Mafano

1Uthenga umene Yeremiya analandira wonena za Ayuda onse amene ankakhala ku Igupto, ku mizinda ya Migidoli, Tapanesi ndi Mefisi, ndiponso ku Patirosi ndi uwu: 2“Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Inu mwaona mavuto aakulu amene ndinawabweretsa pa Yerusalemu ndi mizinda yonse ya Yuda. Lero mizinda yonseyo yasanduka mabwinja, yopanda munthu wokhalamo. 3Zimenezi zinachitika chifukwa cha zoyipa zomwe anachita. Iwo anaputa mkwiyo wanga pofukiza lubani ndi potumikira milungu ina imene iwo kapena inu ngakhalenso makolo anu sanayidziwe. 4Kawirikawiri Ine ndakhala ndikutuma atumiki anga, aneneri, amene anati, ‘Musachite chinthu chonyansachi chimene Ine ndimadana nacho!’ 5Koma iwo sanamvere kapena kulabadira; sanatembenuke kusiya zoyipa zawo kapena kuleka kufukiza lubani kwa milungu ina. 6Nʼchifukwa chake mkwiyo wanga unayaka ngati moto kutentha mizinda ya ku Yuda ndi misewu ya mu Yerusalemu ndi kuyisandutsa bwinja mpaka lero.

7“Ndiye tsopano Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena kuti, ‘Chifukwa chiyani mukufuna kudziwononga chotere? Kodi mukufuna kuti amuna, akazi, ana ndi makanda onse aphedwe ndi kuti mu Yuda musatsale ndi munthu mmodzi yemwe? 8Chifukwa chiyani mukuputa mkwiyo wanga popembedza mafano pofukiza lubani kwa milungu ina mʼdziko lino la Igupto mʼmene mukukhalamo. Kodi mukuchita zimenezi kuti mudziwononge nokha ndi kuti mudzisandutse chinthu choseketsa ndi chonyozeka pakati pa mitundu yonse ya dziko lapansi? 9Kodi mwayiwala zoyipa zimene anachita makolo anu, mafumu a ku Yuda ndi akazi awo, ndiponso zoyipa zimene munachita inuyo ndi akazi anu mʼdziko la Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu? 10Koma mpaka lero simunalape. Simunandilemekeze kapena kumvera malamulo anga amene ndinayikira inuyo ndi makolo anu.

11“Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, ‘Ine ndatsimikiza zobweretsa mavuto pa inu ndi kuwatheratu anthu a ku Yuda. 12Ndidzatenga anthu otsala a ku Yuda amene atsimikiza zopita ku Igupto ndi kukakhala kumeneko. Onse adzathera ku Igupto. Adzaphedwa ndi lupanga kapena kufa ndi njala. Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, adzaphedwa ndi lupanga kapena kufa ndi njala. Adzasanduka chinthu chotembereredwa ndi chochititsa mantha, chinthu choseketsa ndi chonyozeka. 13Ndidzalanga Ayuda okhala ku Igupto ndi lupanga, njala ndi mliri, ngati mmene ndinalangira anthu a ku Yerusalemu. 14Motero mwa anthu amene anapita ku Igupto palibe ndi mmodzi yemwe adzapulumuke, kapena kukhala ndi moyo, kapena kubwerera ku Yuda. Palibe amene adzabwerere kupatula othawa nkhondo.’ ”

15Tsono amuna onse amene anadziwa kuti akazi awo ankafukiza lubani kwa milungu ina, ndiponso akazi onse amene anali pamenepo, gulu lalikulu la anthu, pamodzi ndi anthu onse amene amakhala ku Patirosi mʼdziko la Igupto, anati kwa Yeremiya, 16“Ife sitimvera uthenga umene watiwuza mʼdzina la Yehova! 17Koma tidzachitadi chilichonse chimene tinanena kuti tidzachita: Tidzafukiza lubani kwa mfumukazi yakumwamba ndipo tidzayipatsa nsembe yachakumwa ngati mmene tinkachitira ifeyo ndi makolo athu, mafumu athu ndi akuluakulu mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu. Nthawi imeneyo ife tinali ndi chakudya chochuluka ndipo tinali pabwino, sitimapeza mavuto. 18Koma kuchokera nthawi imene tinasiya kufukiza lubani ndi kupereka chopereka cha chakumwa kwa mfumukazi yakumwamba, ifeyo takhala tikusowa zinthu ndipo takhala tikuphedwa ndi lupanga ndi kufa ndi njala.”

19Akazi anawonjezera kunena kuti, “Pamene tinkafukiza lubani kwa mfumukazi yakumwamba ndi kuyipatsa chopereka cha chakumwa, kodi suja amuna athu ankavomereza mmene timayipangira mfumukazi yakumwambayo makeke abwino olembapo chinthunzi chake ndi kuyipatsa chopereka cha chakumwa?”

20Yeremiya atamva kuyankha kumeneku anawawuza kuti, 21“Kodi mukuganiza kuti Yehova nʼkuyiwala kuti inuyo ndi makolo anu, mafumu anu ndi akuluakulu anu, ndiponso anthu onse, munkafukiza lubani kwa mafano a mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu? 22Ndiye Yehova sakanathanso kupirira ndi machitidwe anu ndi zonyansa zimene munkachita. Nʼchifukwa chake dziko lanu linasanduka chipululu, chinthu choopsa ndi chotembereredwa. Dziko lopandamo anthu monga zilili lero lino. 23Mavuto awa akugwerani chifukwa munkafukiza lubani ndipo munkachimwira Yehova pokana kumvera mawu ake ndi kutsatira malamulo ndi malangizo ake.”

24Kenaka Yeremiya anawuza anthu onse, makamaka akazi kuti, “Imvani mawu a Yehova, anthu onse a ku Yuda amene muli mu Igupto. 25Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Inu ndi akazi anu munalonjeza ndi pakamwa panu, ndipo malonjezowo mwakwaniritsa. Inu munanena kuti, ‘Tidzachita zimene tinalonjeza, kufukizira lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuyipatsa chopereka cha zakumwa.’ Tsopano chitanitu zimene munalonjezazo! Kwaniritsani malumbiro anu.

“Yambani, chitani zimene munalonjeza! Kwaniritsani malumbiro anu! 26Koma imvani mawu a Yehova, inu Ayuda nonse amene mukukhala mu Igupto: Yehova akuti, ‘Ine ndikulumbira mʼdzina langa lopambana kuti palibe wochokera ku Yuda amene akukhala mu Igupto amene adzatchule dzina langa polumbira kuti, ‘Pali Ambuye Yehova wamoyo.’ 27Pakuti ndionetsetsa kuti ndiwachitire choyipa, osati chabwino. Anthu a ku Yuda amene akukhala ku Igupto adzaphedwa pa nkhondo. Ena adzafa ndi njala mpaka onse atatheratu. 28Amene adzapulumuke ku lupanga ndi kubwerera ku dziko la Yuda kuchokera ku Igupto adzakhala ochepa kwambiri. Choncho otsala onse a ku Yuda amene anapita kukakhala ku Igupto adzadziwa kuti mawu woona ndi ati, anga kapena awo.

29“Ine Yehova ndikukupatsani chizindikiro chakuti ndidzakulangani ku malo ano. Motero mudzadziwa kuti mawu anga akuti ndidzakulangani ndi woona. 30Yehova akuti, ‘Ine ndidzamupereka Farao Hofira mfumu ya Igupto kwa adani ake amene akufuna kumupha, monga momwe ndinaperekera Zedekiya mfumu ya Yuda kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, mdani wake amene ankafuna kumupha.’ ”