Nnwom 58 – AKCB & CCL

Akuapem Twi Contemporary Bible

Nnwom 58:1-11

Dwom 58

Dawid “miktam” dwom.

1So mo asodifo, ampa ara sɛ, moka asɛm a ɛteɛ ana?

Mubu atɛntrenee wɔ nnipa mu ana?

2Dabi da! Modwene ntɛnkyew wɔ mo koma mu

na mo nsa de akakabensɛm ba asase so.

3Amumɔyɛfo fom kwan fi awo mu;

wɔyɛ mmaratofo fi awotwaa mu na wodi atoro.

4Wɔn ano bɔre te sɛ ɔwɔ de,

ɛte sɛ ɔprammiri a wawɛn nʼaso,

5a ɔnte ntafowayifo dwom,

na ne dwom dɛdɛ no mpo mfa ne ho.

6Ao Onyankopɔn, bubu ɛse a egu wɔn anom,

Awurade, tutu gyata no sebɔmmɔfo no gu!

7Ma wontwa mu nkɔ sɛ sunsuan;

sɛ wɔtwe wɔn agyan a, ma wɔn bɛmma no ano nwu.

8Ma wɔnyɛ sɛ nwaw horɔdɔhorɔdɔ bi a ɔrenan agu wɔ bere a ɔretene no.

Ma wɔnyɛ sɛ ɔba a owu wɔ awoe a onhu owia koraa.

9Ansa na mo nkuku bɛte nsɔe ano yaw,

sɛ ɛyɛ amono anaa awo no, wɔbɛpra amumɔyɛfo akɔ.

10Sɛ wɔtɔ were ma atreneefo a wɔn ani begye,

na wɔbɛhohoro wɔn anan ho wɔ amumɔyɛfo mogya mu.

11Afei nnipa bɛka se, “Ampa ara atreneefo kɔ so nya wɔn akatua;

na ampa ara Onyankopɔn bi wɔ hɔ a obu wiase atɛn.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 58:1-11

Salimo 58

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide.

1Kodi inu olamulira mumayankhuladi molungama?

Kodi mumaweruza mwachilungamo pakati pa anthu?

2Ayi, mʼmitima mwanu mumakonzekera zosalungama,

ndipo manja anu amatulutsa zachiwawa pa dziko lapansi.

3Ngakhale kuchokera tsiku lawo lobadwa oyipa amasochera;

kuchokera mʼmimba ya amayi awo, iwo ndi otayika ndipo amayankhula mabodza.

4Ululu wawo uli ngati ululu wa njoka,

ngati uja wa mphiri imene yatseka mʼmakutu mwake.

5Imene simva liwu la munthu wamatsenga,

ngakhale akhale wa luso lotani munthu wamatsengayo.

6Gululani mano mʼkamwa mwawo, Inu Mulungu,

Yehova khadzulani mano a mikango!

7Mulole kuti asowe ngati madzi oyenda

pamene iwo akoka uta mulole kuti mivi yawo ikhale yosathwa.

8Akhale ngati nkhono imene imasungunuka pamene ikuyenda;

ngati mwana wakufa asanabadwe, iwo asaone dzuwa.

9Miphika yanu isanagwire moto waminga ya mkandankhuku,

kaya iyo ndi yobiriwira kapena yowuma, oyipa adzachotsedwa.

10Olungama adzasangalala poona kubwezera chilango,

pamene adzasambitsa mapazi awo mʼmagazi a anthu oyipa.

11Ndipo anthu adzanena kuti,

“Zoonadi, olungama amalandirabe mphotho;

zoonadi kuli Mulungu amene amaweruza dziko lapansi.”