Dwom 46
Koramma dwom. Wɔto no “alamot” sanku nne so.
1Onyankopɔn ne yɛn guankɔbea ne yɛn ahoɔden,
amanehunu mu boafo a ɔwɔ hɔ bere biara.
2Enti sɛ asase ani dan butuw,
na mmepɔw tutu kogu po ase a, yɛrensuro,
3sɛ po bɔ asorɔkye na ehuru
na ɛma nkoko wosow mpo a, yɛrensuro.
4Asuten bi wɔ hɔ a
ne nsuwansuwa de anigye ba Onyankopɔn kuropɔn mu,
beae kronkron a Ɔsorosoroni no te.
5Onyankopɔn te kuropɔn no mu, na ɔrenhwe ase;
Onyankopɔn bɛboa no anɔpahema.
6Amanaman yɛ hoo, na ahenni hwehwe ase;
ɔma ne nne so ma asase nan.
7Asafo Awurade ka yɛn ho.
Yakob Nyankopɔn yɛ yɛn aban.
8Bra bɛhwɛ Awurade nnwuma,
ɔsɛe a ɔde aba asase no so.
9Ɔma akodi gyae kosi asase ano.
Obubu agyan mu na ɔsɛe peaw;
ɔde ogya hyew nkatabo.
10Monyɛ komm na munhu sɛ me ne Onyankopɔn;
wɔbɛma me so wɔ amanaman no mu,
wɔbɛma me so wɔ asase so.
11Asafo Awurade ka yɛn ho;
Yakob Nyankopɔn yɛ yɛn aban.
Salimo 46
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Nyimbo ya anamwali.
1Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu,
thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.
2Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike,
ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,
3ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu,
ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake.
4Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu,
malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako.
5Mulungu ali mʼkati mwake, iwo sudzagwa;
Mulungu adzawuthandiza mmawa.
6Mitundu ikupokosera, mafumu akugwa;
Iye wakweza mawu ake, dziko lapansi likusungunuka.
7Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,
Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.
8Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova,
chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi.
9Iye amathetsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi;
Iye amathyola uta ndi kupindapinda mkondo;
amatentha zishango ndi moto.
10Iye akuti, “Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu;
ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu;
ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi.”
11Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,
Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.